Back to God Ministries

Back to God Ministries Back to God Ministries, is a self supporting ministry that preaches the word of God through Online and public Preachings..

we work hand in hand with with the Seventh-day Adventist Church in proclaiming the Gospel and promoting Church Programs.

Molere Zone Camp Meeting yaitana kuyambira mawali🔥
10/08/2026

Molere Zone Camp Meeting yaitana kuyambira mawali🔥

10/08/2026

"Mukapeza abwenzi abwino don't abuse them"

Amenewa ndimawu amene Brian Banda watisiira kuti tiziwagwilitsa ntchito. Lero Brian akhala akulowa m'manda pamene mitima ya anthu ambiri idakali yosweka. Ife kuno tidzawakumbukira malemuwa chifukwa timagwira nawo ntchito bwino. Anali munthu ofikilika tikafuna thandizo lililonse ku MBC.

Koma poti Mau a Mulungu amati kwaikika kwa munthu kufa kamodzi chotero ifenso tingoti dzina la Mulungu lilemekezeke poti Iyeyo anatipatsa ndipo lero Mulungu yemweyo watenga moyo wa Brian. Kufikiranso tsiku lina lomwe tidzaonananso tikachita bwino pansi pano poti Bible limati onse ogona mwa Ambuye adzauka ndipo tili nacho chiyembekezo kuti tsiku lina posachedwapa tidzaonananso.

Mulungu atonthoze onse olira ndikupukuta misonzi

🥳🥳🔥🙌🏼Anthu aku Zomba Tsiku Ndi lerotuu, kwa anthu onse ozungulira Zomba mwayi wanu uja ndi lero kumvera komanso kuonera ...
09/08/2026

🥳🥳🔥🙌🏼Anthu aku Zomba Tsiku Ndi lerotuu, kwa anthu onse ozungulira Zomba mwayi wanu uja ndi lero kumvera komanso kuonera nyimbo za;

family 🙏
Davie chiwaya 🥳
Florence massea 🌝
Kanyan'gama 🥳🥳🔥

Tikakhala ife ndiye tanyamuka kale!

Sipazakhala nthawi 🤗

See you there 🥳🔥

SEMC 2026 Camp Meetings UpdatePamene misonkhano ya misasa ikupitilira, lero ku Malamulo Mission akhala akuyamba msonkhan...
09/08/2026

SEMC 2026 Camp Meetings Update

Pamene misonkhano ya misasa ikupitilira, lero ku Malamulo Mission akhala akuyamba msonkhano wawo wa misasa. Msonkhanowu ukhala wa ma tsiku 7 ndipo ukuyembekezereka kutha pa 15 lomwe ndi Lasabata likudzali.

Alaliki omwe azidzapezeka mu msonkhanowu ndi monga; Pastor Lt. Masco Chataika, Evangelist Dr. Ernest Kaonga, Evangelist Charles Nakhonyopa komanso Evangelist Richard Sopa.

Abusa a Shadreck Msuka omwenso ndi a Director a Personal Ministries muchigawochi adzakhalanso akupezeka mu msasawu pa ntchito yawo yoyendera misasa. Kupatula kupezeka mu msasa wa Malamulo Mission, sabata imeneyi akhalanso akuyendera misasa ina yomwe ikuchitika mozungulira Thyolo, kuonesetsa kuti misasa yonse ikutsatira ndondomeko zomwe mpingo unakhazikitsa poonesetsa kuti anthu ochuluka akumagonera ku msasa komanso kuonesetsa kuti alaliki onse omwe anatumizidwa akufika m'misasa. Mwazina akhalanso akuonesetsa kuti misasa yonse ikutsatiranso njira zaukhondo. Iwo atisimikizira kuti ayesetsa kuyendera misasa yochuluka chaka chino poonesetsa kuti mfundo zonse zikutsatidwa, iwo alimbikitsa a Khristu kumakagonera ku msasa komweko monga mwa dongosolo lake.

(Olemba: Chicco Friday Banda- SEMC Personal Ministries _Communication 09/08/26)_

Palibe nthawi yokoma kuposa nthawi ya msonkhano wa misasa. Abusa a Ghanamba komanso abusa ena omwe anali nawo ku msonkha...
09/08/2026

Palibe nthawi yokoma kuposa nthawi ya msonkhano wa misasa. Abusa a Ghanamba komanso abusa ena omwe anali nawo ku msonkhano wa misasa wa Mgwalangwa kulandira mphatso pa tsiku lotsekera msasa

Msonkhano wa misasa omwe unayamba pa 4 August ku Ntaja pa mpingo wa Mbenjere watha lero. Poyamkhula potsekera msonkhanow...
08/08/2026

Msonkhano wa misasa omwe unayamba pa 4 August ku Ntaja pa mpingo wa Mbenjere watha lero. Poyamkhula potsekera msonkhanowu abusa achigawochi abusa Wilfred Kachingwe ayamikira atumiki onse omwe anafika mu msonkhanowu chifukwa chogwira ntchito ya Mulungu mozipereka.

Poyankhula m'malo mwa azitumiki onse abusa a Petros Sukali omwenso ndi a President a Malawi Union ayamikira kuti msonkhanowu unali opambana kwambiri chifukwa anthu ochuluka amagonera ku msasawu.

Mu msasa umenewu kunali a President a Malawi Union abusa a Petros Sukali, a Director a Personal Ministries kuchigawo cha South East Malawi Conference abusa a Shadreck Msuka, Evangelist Dr. Ernest Kaonga komanso abusa achigawochi abusa a Wilfred Kachingwe.

(Olemba: Chicco Friday Banda- Back to God Media 08/08/26)

Imfadi sidziwika💔Director General for the Malawi Broadcasting Corporation (MBC), Brian Banda, has died. Banda died at Mw...
08/08/2026

Imfadi sidziwika💔

Director General for the Malawi Broadcasting Corporation (MBC), Brian Banda, has died. Banda died at Mwaiwathu Private Clinic in Blantyre, after a short illness. While confirming the death, MBC Public Relations and Customer Affairs Manager Chisomo Mwamadi said more details will follow.

08/08/2026

Devine Service

Ntaja Camp Meeting

Preacher: Pastor Petros Sukali (Malawi Union President)

08/08/2026

Nthawi zina mukakhala ndi zinthu, okuyandikirani muzidabwa nawo || Ps. Petros Sukali- Malawi Union President

Ntaja Camp Meeting- Mbenjere SDA Church

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Back to God Ministries posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share