26/06/2023
kumvetsetsa bukhu la danier gawo7 lomaliza.
Danier 1:17 koma anyamata amenewa anai, mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Danieli anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse. apa tikuona okondedwa kuti Danier anali wanzeru za masophenya. amaziwa kutanthauzira malota; nkhani imeneyi yokhunza Danier kumasulira maloto. tiyiwona mu gawo 8 ikubwelayo kuchokera pa danier chapter 2.ndiye amnzake adanier anapatsidwa nzeru ndi chidziwitso cha mabukhu. anali anthu, anzeru amawaziwa mabukhu sinakha anali anthu ophunzira magraduate anali ndi madegree. amawatanthauzira bwino mabukhu chifukwa anali ophunzira ngakhale anali ophunzira amaopa mulungu. pakuti chiyambi cha nzeru ndi kuziwa mulungu (miyambo 1:7) danier 1:18 atantha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkuru wa adindo analowa nao pamaso pa nebukadinezara.ndipo mfumu inalakhula nao, koma mwa iwo onse sanapezeke monga Danier, Hananiya, misaeli, ndi Azariya; naimirira iwo pamaso pa mfumu.ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira, inawapeza akuposa alembi ndi openda onse m'ufumu wake wonse. nakhala moyo Danier mpaka chaka choyamba cha koresi.mfumu nubukadinezara, inazizwa ndi anyamata inanena ndi mkuru wa adindo kuti abwele ndi anyamata anai danier ndi anzake. Koma mfumu, inanena kwa danier ndi amnzake amene angoyima chiriri pamaso pa amfumu. mfumu inati kwa danier ndi anzake kuti sipazapezeka mwa inu ku Babulo kuno anzeru ngati inu. Chifukwa anthu awa kunena zoona nzeru zawo zili ten times times nzeru zoopya.ifenso mulungu, amatikonda kwambili; tikhonza kukhala ndi nzeru zotele osazidelela. chongofunika kukhala wokhulupilika pamanso pa mulungu komanso kumvera malamulo amulungu ndi malamulo azanthanzi. mneneli, danier ndi amnzake anali mu chaka choyamba cha mfumu koresi. Koresi tizamuona kutsogoloko ndi amene anali mfumu ya amedi ndi apelesi . tizamuona kutsogoloko kuti koresi anagwira ntchito yolanda mzinda wa Babulo. Ankolo ake akoresi ali mfumu Dariyo .
Yatsala part 8.