25/05/2026
Komatu Likoma Island pa map imaonetsa kuti ili mu Mozambique?
Mu 15th century, Inatchuka ndi za Malonda komanso zipembezo ndi mtundu wa anthu otchedwa 'Nyanja'. Mu 18th century, gulu la zamalonda la Swahili linagundika kwambiri ndi za malonda ao pa malopa. Mu 1861 Dr David Livingstone naye anasangalatsidwa ndi kukongola kwa Likoma island. Komano mu zaka za 1890's Britain imene inkalamulira Malawi komanso Portugal imene inkalamulira Mozambique anakokana malaya pa umwini wa chilumba chimenechi. Panadziwika kuti Britain, inkafuna malowa chifukwa anali pakati pa nyanja ya Lake Nyasa, pamene Portugal inkafuna malowa pazifukwa zoziwa okha, koma ena anakhulupirira kuti Portugal inkafuna kuzikuzira malire komanso mphamvu. Mu chaka cha 1891, maiko awiriwa anachita zokambilana zimene anazitcha,The Anglo-portuguese treaty zimene zinapereka malowa. Ku mbali ya Britain pa zokambiranazi, kunali a Foreign Secretary Lord Salisbury 🇬🇧 pamene ku mbali ya Portugal kunali Minister António de Serpa Pimentel 🇵🇹. Mpingo wa Universities Mission to Central Africa (UMCA) ndi umene unathandizira kwambiri kuti Britain itenge malowa chifukwa unali ndi zochika zina pa malowa, nde sumafuna kulamuliridwa ndi ma Portuguese. Mu 20th Century, mpingo wa Anglican ndi umene unali woyamba kuzamanga pa Likoma island. Kufikira pano Likoma ili ndi anthu ochuluka a chipembezo cha chi khristu kuposa zipembezo zina. Dziko la malawi litatenga ufulu wozilamulira palokha, malowa anapitilira kukhala ku mbali ya dziko la Malawi, komano ojambula map sanasinthebe za mizere imene amaitcha international boundaries, imene imaonetsabe kuti Likoma ili mu Mozambique.
Follow this page kuti muzimva ma history obeba aja Mwauka SHOW