08/08/2026
πππ¨π¦π π π π’πππππ‘ππ: "π§ππ¦ππ πππ π‘π§πππͺπ" ππ¨ππ ππ‘π§ππ¨ π£π π ππππ₯π’ π π ππ¬π π π’π₯πππ‘ π¦ππ‘ππ
Akhristu adasonkhana mmudzi mwa a Maganga ku Bangwe pa mwambo wa maliro a Mayi Moreen Kampani Senga omwe anamwalira pa
6 August 2026 ali ndi zaka 46. Mayi Senga anabadwa pa 16 September 1979.
Pa utumiki wa malirowo, abusa a Orlac Mozalande achigawo cha Malabvi adapereka ulaliki womwe mutu wake unali "KUMASAMALA NTHAWI".
M'busa Mozalande analimbikitsa akhristu kuti atsatire Yesu chifukwa Iye yekha ndi amene amadziwa za nthawi ya moyo wa munthu aliyense. Iye anati palibe mmodzi mwa ife amene amadziwa za mawa, ndipo ndi chifukwa chake ndikofunika kwambiri kumpatsa Ambuye moyo wathu kuti aulamulire.
"Ino sinthawi yochita zibwana ndi nthawi yopanga zauchimo. Tiyenera kukhala tcheru chifukwa tikuneyera kufa tili ndi Yesu," adatero m'busa Mozalande polimbikitsa mabanja ndi okhulupirira omwe anali pamalirowo.
Iye anatinso "mphindi yatsoka sifanana" ndipo anachenjeza akhristu kuti asamakopere ena pochita zoipa ponena kuti mwina anzathuwo atha kuzalapa pamaliro athu atadzidzimuka. "Aliyense adzayankha yekha kwa Mulungu. Tiyeni tiyende m'njira ya Ambuye osati kutsatira zitsanzo zoipa za anthu," adatero.
M'busa Mozalande anamaliza ndi kukumbutsa mpingo kuti moyo uli m'manja mwa Mulungu, choncho tiyeni tigwiritse ntchito tsiku lililonse pothandiza ntchito ya Mulungu ndi kukhala okonzeka kubweranso kwa Khristu.
Mayi Senga anali nkhristu wa mpingo wa Lisanjala SDA, Mgomanjira B - Jesus Way.
Akubanja adandaula koma akuti alimbikitsika ndi uthenga komanso kupezeka kwa anthu pamodzi ndi akhristu pozawatonthoza.
Wolemba : McAllan Mapinda
Lisanjala Media