26/01/2023
KUSAMALA NTHAWI ZONSE KUKHALA NDI ZOVALA ZABWINO KWA YEMWE ANGATHE KUPEZA
Kutchena kwa msilam ndi chinthu chofunikira kwambiri, msilamu aziwoneka bwino,msilamu azitchena ,zovala zabwino ukakhala nazo uzivala ,msilamu azitchena nthawi yomwe akuchita ibaadah ,pa swalah sipovala nyangwita ,chonsecho uli ndi zovala zabwino ukusungira ,pa swalah osamavala ngati nsing’anga ,pa swalah sipovala ngati munthu okhwima wanyanga,msilamu zoona azivala ngati omanga mvula? Msilamu azipha ulusi msilam azisita chovala,ngati mmavala mikanjo kupha mikanjo yabwino ,ngati umapha ma suit iphani jacket yabwino ka necktie kabwino ,kutchena sikuletsedwa mchislam as long as zovalazo sizinalowe mgulu la zinthu zoletsedwa ,zozimana zija kukanika kugula nsapato chikang’a mkuphulika ,pozemba kuti musachite manyazi mkumati ndi sunnah kukhala ndi zikang’a ayi bodza limenero kanamireni kwina..
Allah (ﷻ) amasangalatsidwa ndikuwona mtendere omwe wamupatsa kapolo wake ukuwonekera poyera,tsiku lina Mtumiki (ﷺ) anamuwona mkulu wina wavala tinyangwita chonsecho Allah (ﷺ) anamudalitsa anampatsa makobiri,ali mkuthekera kogula zovala zabwino ,choncho Mtumiki (ﷺ) atamuwona mkuluyi sanakhale chete koma kumudzudzula mchitidwe ovala nyangwitawu anati:
.....ألك مال؟ قال: نعم، قال من أي المال؟ قال: قد اَتاني الله من الإبل والغنم والخيل والرقيق، قال: فإذا اَتاك الله مالا فلير أثر نعمته عليك وكرامته...
…...Kodi Allah (ﷻ) anakupatsa chuma? anayakha kuti: Inde! Mtumiki (ﷺ) anafunsanso kuti: ndi chuma chanji chomwe Allah (ﷻ) anakupatsacho? Anayankha nati: anandipatsa ngamila ,nkhosa ma horse (hatchi) komanso akapolo…Mtumiki (ﷺ) Allah (ﷻ) akakupatsa chuma ,ziziwoneka zizindikiro za mtendere wakewo pa iwe komanso kufewa mtima kwake….
Hadith ya saheeh ndipo ikupezeka mma book monga (أبوداود) (4063) komanso (النسائي) (5224) komanso ili ndi ma umboni kuchokera mma hadith monga a ibn Mas’ood, Abdullah bin Amri, Abu Hurayrah,komanso Omran bin Huswayn ndi ena ambiri…
Anthu ena amaletsa kutchena amvekere osamayiwala ndife akapolo a Allah (ﷻ) nde ofunika munthu ukayima pamaso pa Allah (ﷻ) uzivala mnyozeka, zoona pamaso pa Allah (ﷻ) muzivala monyozeka kuvala nyangwita ,koma moti tsiku lina mutachita mwayi oyitanidwa ndi mtsogoleri wadziko ku state house mungapiteko mutavala nyangwita? Mesa mukhoza kusakasaka zovala zabwino zapamwamba kuzilemekeza kusangalatsa munthu chifukwa choti ndi president wadziko, kulibwanji kuzilemekeza kuvala zapamwamba pofuna kusangalatsa Allah (ﷻ) bwana wa ma bwana president wa ma president?
Amene mmaletsa anzanu kutchena dziwani kuti mukulimbana ndi malamulo a Allah (ﷻ), Allah (ﷻ) akunena mu Qur’an yake yolemekezeka kuti:
قُلْ مَنْ حَرَّمَ زِينَةَ اللَّهِ الَّتِي أَخْرَجَ لِعِبَادِهِ وَالطَّيِّبَاتِ مِنَ الرِّزْقِ قُلْ هِيَ لِلَّذِينَ آمَنُوا فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا خَالِصَةً يَوْمَ الْقِيَامَةِ كَذَلِكَ نُفَصِّلُ الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَعْلَمُونَ
Nena: "kodi ndi ndani waletsa zokongoletsa za Allah (ﷻ), (kuvala zovala zabwino), zomwe Iye (Allah) adawatulutsira akapolo ake ndi zakudya zabwino?" Nena: "Zinthu zimenezo (kutchena komanso kudya zakudya zabwino) nzololedwa kwa amene akhulupirira (Asilamu) pamoyo wapadziko lapansi. (Zidzakhala) zawozawo tsiku la chimaliziro. M'menemo ndi mom we Tikulogosolera ma verse athu kwa anthu ozindikira."
Mmamva bwanji mukamawerenga verse limeneri amene mmavalabe nyangwita chonsecho muli ndi kuthekera kopeza zovala zabwino? Mmamva bwanji mukamawawona asilamu anzanu akusowa zovala zabwino chonsecho muli mkuthekera kowathandiza? Mmamva bwanji mukamatenga nyangwita zomwe inu simuzifuna mkumawapatsa anzanu mowatayira chonsecho mmawerenga kuyankhula kwa Allah (ﷻ) konena kuti:
لَنْ تَنَالُوا الْبِرَّ حَتَّى تُنْفِقُوا مِمَّا تُحِبُّونَ وَمَا تُنْفِقُوا مِنْ شَيْءٍ فَإِنَّ اللَّهَ بِهِ عَلِيمٌ
Simudzapeza zabwino mpaka mutapereka zomwe mmazikonda. Ndipo cha ulere chilichonse chomwe mupereka, ndithudi, Allah (ﷻ) amachidziwa...
Kutchena sikuzikweza ngati mmene ena amaganizira ,ngakhalebe pena zikhoza kusokonekera kugwera mukuzitukumula malingana ndi niyah ya munthu,koma kuchenako pakokha sikuzitukumula ayi…kuchokera mu hadith ya saheeh yomwe anayilandira ibn Mas’ood (رضي الله عنه) kuchokera kwa Mtumiki (ﷺ) yemwe anaphunzitsa kuti:
لا يدخل الجنة من كان في قلبه مثقال ذرة من الكبر، فقال رجل: إن الرجل يحب أن يكون ثوبه حسنا، ونعله حسنة، قال: إن الله جميل يحب الجمال، الكبر بطر الحق، وغمط الناس...
Sakalowa ku Jannah amene mumtima mwake muli kuzikweza ngakhale kochepa ngati njere,munthu wina ananena kuti: ndithudi munthu amakonda nthawi zonse kuti zovala zake zikhale zabwino nsapato zakenso zabwino,anaynkha Mtumiki (ﷺ) kuti: ndithudi Allah (ﷻ) ndi wabwino ndipo amakonda zobwino ,akati kuzikweza ndiko kukana chilungamo komanso kuwawona anthu ngati apansi kwambiri iweyo wapamwamba..
Hadith ya saheeh ndipo ikupezeka mu (مسلم) (91) komanso (أبو داود) (4092) ndi ma book ena
PHUNZIRO MU HADITH IMENEYI
Kuchokera mu hadith imeneyi muli ma phunziro angapo omwe tikuphunziramo monga:
1) Kuvala zabwino kapena kuzisamalira munthu mkumawoneka bwino sizitanthauza kuti munthu yo akuzikweza ayi…
2) Allah (ﷻ) ndiwabwino ndipo amakonda zabwino ,choncho msilam ozisamalira wawukhondo otchena bwino ndi wabwino kuposa yemwe akuvala masanza ngati nsing’anga chonsecho ali ndikuthekera kovala bwino
3) Mu hadith imeneyi kuzikweza amatanthauza munthu otsutsana ndi chilungamo chikamufikira ,mkumachitabe makani ,monga anthu a bid’ah ndi ozikweza pambuyo poti alangizidwa sunnah
4) Mtumiki (ﷺ) amalimbikitsa zovala zabwino choncho ma sahabah ake analinso kuvala bwino,mchifukwa atamva hadith anadabwa ndikufunsa kuti amvetsetse kuzikweza kweni kweni ndi kuti
عدم الإسراف في اللباس
KUPEWA KUWONONGA (CHUMA) PA ZOVALA
Ngakhale kuti kutchena kuli kofunikira Allah (ﷻ) watiletsa kuwononga kutaya chuma chambira mosasamala Kamba kogula zovala chabe,pena mawanja akumasokonekera akazi kuvuta kwambiri nkhani yatchenedwe mwamuna kukhala pa mpeni tipewe kuwononga kwambiri kumakhala moderate ,osati kalikonse mukawone mukhale nako ayi….Allah akunena kuti:
يَا بَنِي آدَمَ خُذُوا زِينَتَكُمْ عِنْدَ كُلِّ مَسْجِدٍ وَكُلُوا وَاشْرَبُوا وَلَا تُسْرِفُوا إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُسْرِفِينَ…
Oh! inu ana a Adam! tengani (valani) zovala zanu zabwino pamene mukukapemphera swalah iliyonse ndipo idyani ndi kumwa; koma musapyole muyeso (kuwononga). Iye (Allah (ﷻ)) sakonda opyoza muyeso (owononga)…
Mtumiki (ﷺ) naye ananena kuti:
كُلوا واشرَبوا وتَصدَّقوا والْبَسوا ما لم يخالِطْهُ إسرافٌ أو مَخيَلةٌ.....
Idyani ndi kumwa ,ndi kuperekani swadaqa,ndipo valani (zabwino) mpanda kulwetsa kuwononga kapena kufuna kuzitukumuula…
Ndi hadith ya hassan ndithu imeneyi iikupezeka mu (النسائي) (2559) komanso (ابن ماجه) (2605) ndi ma book ena ambiri ngakhalenso imam Bukhar anayichita ta’aleeq pa topic ya zovala.
PHUNZIRO MU HADITH IMENEYO
Hadith imeneyi ikutiphunzitsa zambiri, komanso ikutiphuzitsa zinthu zomwe nzofunikira pa moyo wa munthu zomwe ndi:
1) Kupeza cha chakudya mopanda kuwononga
2) Kupeza chakumwa koma apewe kuwononga
3) Kupeza zovala zabwino koma apewe kuwononga
4) Kupereka swadaqah apewe kuzkweza