01/06/2026
*TIYANKHULENI AMBUYE*
_1 JUNE, 2026_
Kulemekeza *Justin Mmalitri Woyera*
*LOLEMBA LAMULUNGU WA 9 PACHAKA (II)*
*MAU OYAMBA, MAU A MKALATA YACHIWIRI YA PETRO 1:2-7*
Ndine, Simoni Petro, mtumiki ndi mthumwi ya Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa anthu amene adalandira chikhulupiriro chomwe ifenso tidalandirako. Iwonso adachilandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu, ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wochuluka, pakumudziŵa Iyeyo, ndiponso Yesu Ambuye athu. Mulungu, mwa mphamvu zake, adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa. Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, adatipatsa madalitso aakulu ndi a mtengo wapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chionongeko chimene chili pa dziko lapansi, chifukwa cha zilakolako zoipa. Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo, muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.
*Mau a Ambuye*
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 91: 1-2, 14-15B, 15C-16
*Inu Chauta, ndinu kothaŵira kwanga* (2b).
Munthu amene amakhala mu linga la Wopambanazonse,
Iye amene amakhala mu mthunzi mwa Mphambe,
Adzanena kwa Chauta kuti:
“Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa,
Ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
*Inu Chauta, ndinu kothaŵira kwanga*.
Pakuti amene amandikangamira,
Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa.
Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha,
Ndidzakhala naye pa nthaŵi ya mavuto.
*Inu Chauta, ndinu kothaŵira kwanga*.
Ndidzamulanditsa ndi kumulemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
*Inu Chauta, ndinu kothaŵira kwanga*.
*Aleluya*: (_Chivumbulutso 1: 5ab_) Ambuye Yesu Khristu, ndinu Mboni yokhulupirika, amene muli woyambirira kulandira moyo wa ulemerero; mudatikonda, ndipo ndi magazi anu, mudatimasula ku machimo athu, _Aleluya_.
*MTHENGA WA AMBUYE MONGA ADALEMBERA MARKO 12:1-12*
Yesu adayamba kulankhula ndi akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu ena m’mafanizo, adati: “Munthu wina adabzyala mipesa m’munda mwake, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba moponderamo mpesa, namanga nsanja ya olondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina. Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti alimiwo akampatsireko zipatso za m’munda muja. Koma alimiwo adamugwira wantchitoyo nammenya, nkumubweza osampatsa kanthu. Munthu uja adatumanso wantchito wina, koma alimi aja adampweteka m’mutu ndi kumunyoza. Munthuyo adatumanso wantchito wina, uyu ndiye adangomupheratu. Adachita chimodzimodzi ndi antchito ena ambiri, ena adaŵamenya, ena kuŵapheratu. Munthu uja adangotsala ndi mmodzi basi, mwana wake weniweni wapamtima.
Ndiye pambuyo pa onse, adadzatuma iyeyu. Adati: ‘Mwana wanga yekhayu akamuchitira ulemu.’ Koma alimi aja adayamba kuuzana kuti: ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamusiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’ Tsono adamugwiradi, namupha nkumuponya kunja kwa mundawo. Kodi mwini munda wa mpesa uja adzachita chiyani? Ndithu, adzabwera naŵapha alimiwo, munda uja nkuubwereka alimi ena. Nanga monga simudaŵerenge Malembo aja akuti: ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wa pa ngodya, wofunika koposa. Ambuye Mulungu ndiwo adachita zimenezi, ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’” Pamene akulu a Ayuda aja adazindikira kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo, adafunitsitsa kumugwira, koma ankaopa khamu la anthu. Tsono adangomusiya nachokapo.
*Mthenga wa Ambuye*