15/06/2026
LILONGWE MALAWI
Muli bwanji a Malawi azanga, ndakhala matsiku angapo sopano ndikuva kuwawa kumafuna nditayakhulapo pa zoipa ndi zachisoni zikuchitiki ku South Africa.
Ndine muthu okhuzika dzedi ndimomwe a mayi ndi ana akuvutikira kugona panja pa chifukwa choti sizika za South Africa. Ndizoona boma lalowerelapo kumbali ya transport komabe matsiku otidikira ndi ambili.
Kodi Boma palibe kuthekela kochita machawi makamaka kwa a mayi ndi ana?
Nanga madela ena akutipo chani ?
Nanga athu omwe akuthandizidwa kubwelela ku Malawi sangawakozele zochita chifukwa kuvutika ku pitilira ngati palibe zochita.
Ganizo langa ndimati ngati nkotheka boma likana wapasako ka starter park or pali pa ngongole, taona Ghana itspanga izi kuwapatsa athu ake poyambila.
Ndipepheso kwa mabugwe obwelekesa ndalama atalowelelapo chifukwa athu avutika zedi.
Komaso umbanda utha kuchuluka pomwe a chinyamata akhale opanda chochita mmamidzimu.
Ndikhala ndikuyakhulapo pankhani yi, ndayesa kuzilesa koma ndili wachisoni ndi wamatha ndi zomwe zikuchitika .
Zikomo
M.Malemia