One Ummah Islamic Foundation of Malawi

One Ummah Islamic Foundation of Malawi One ummah was created with the purpose of teaching about the fear of Allah to the Nation of Malawi

22/06/2026

Sheikh Siraji Hussein writes:

UBWINO OPEWA MACHIMO AKULUAKULU...

Kuchisilamu kuno, machimo Sali level imodzi. Pali pachimo ena ndi akulu kwambili, ena akulu, pomwe ena ndi ang'ono ang'ono.

Chinthu chomwe chili chofanana pamachimo onse mchakuti, munthu umalembedwa Msambi ukawapanga. Ndipo ngati suwalapa kapena ngati Allah ﷻ sakukhululukira, utha kulangidwa nawo, pena padziko pano, mmanda kepena ku Akhirah, Allah atiteteze.

Koma machimo akuluakulu ali ndi vuto loti samachoka wamba mpakana munthu ulape zeni zeni kwa Allah ﷻ ndi kutsindika kuti suzawachitaso. Ena amafuna mpakana ukawapepese eni ake omwe unawalakwira. Pachifukwa chimenechi machimo akuluakulu amafunika kuwapewa ndi kuwatalikira. Amafunikaso ngati zatheka, kutseka njira zomwe zingakutengere ku machimowo ngakhale pazokha njirazo zingakhale kuti si Haram.

Ubwino waukulu opewa machimo akuluakulu ndiwoti zimampangitsa kuti Allah ﷻ akukhululukire machimo ang'ono ang'ono iye wati:-

إِن تَجْتَنِبُوا كَبَائِرَ مَا تُنْهَوْنَ عَنْهُ نُكَفِّرْ عَنكُمْ سَيِّئَاتِكُمْ وَنُدْخِلْكُم مُّدْخَلًا كَرِيمًا

Ngati mupewe machimo akuluakulu omwe mwaletsedwa, tikukhululukirani machimo anu (ang'ono ang'ono) ndipo tizakulowetsani Malo olemekezeka (Jannah).

Awa ndi ena mwa machimo akuluakulu omwe Ali common pakati pathu masiku ano:-

Kupha munthu
Chiwelewele
Kuba
Kunyoza makolo
Kuyikira umboni Zabodza
Kudya chuma cha masiye
Kupanga chinyengo pa malonda
Kudula ubale
Kupondeleza
Kuyankhula paza Allah zomwe sukudziwa
etc etc

Tiyeni tiyesetse kupewa machimo akulu, ndipo omwe tawapanga kale aja tiyeni tilape, kwinaku tikupempha Allah ﷻ kuti atipatse mtima opewa machimowa.

13/05/2026

Sheikh M***a Adam writes:
𝐊𝐔𝐋𝐀𝐋𝐈𝐊𝐈𝐑𝐀 𝐏𝐀 𝐌𝐀𝐋𝐈𝐑𝐎 /𝐊𝐔𝐌𝐀𝐍𝐃𝐀

Anthu ambiri lero atembenuza zinthu akuchita mosemphana ndi mmene ziyenera kuchitikira kapena mmene anaphunzitsira Mtumiki (ﷺ), kulalikira pa maliro kapena kumanda ndi nkhani ya bwino ndipo ndi ntchito yoti ili ndi ma umboni.

Mwachitsanzo imaam Bukhar (رحمه الله) anayika mutu mu book lake la saheeh Bukhar onena kuti:

باب موعظة المحدث عند القبر وقعود أصحابه حوله

Topic yofotokoza za (kuvomerezeka kwa) kulalikira ku manda oyankhula atakhala ndi omvera atakhala momuzungulira mbari mwake ,kuchokera pa mutu umenewu imaam bukhar anasonkhanitsa ma hadith omwe Mtumiki (ﷺ) anali kuphunzitsa ndi kulalikira pa maliro kapenanso ku manda ,monga hadith ya Allie (رضي الله عنه) yonena kuti:

كنا في جنازة في بقيع الغرقد, فأتانا النبي , فقعد وقعدنا حوله, فقال: ما منكم من نفس منفوسة إلا كتب مكانها في الجنة أو النار....

Tinali ku maliro ndipo tili ku manda otchedwa (Baqī‘ aI-Gharqad) anatipeza Mtumiki (ﷺ) anakhala pansi ndipo tinakhala mbari momuzungulira ndipo Mtumiki (ﷺ) ananena kuti: palibe kuchokera mwa inu mzimu omwe wawuziridwa kupatula kuti unalemberedwa malo ake (okakhala) ku Jannah kapena ku moto….

Mu hadith imeneyi muli chilolezo cholalikira kapena kuphunzitsa pa maliro kapenanso ku manda, ma hadith ngati amenewa alipo ambiri komanso a saheeh…

Apa tidziwe kuti kulalikira pa maliro komanso ku manda ndi zinthu zovomerezeka zili ndi ma umboni okhazikika komanso odziwika ,kulalikira pa maliro kapenanso ku manda sizingakhale bid’ah ngati mmene anthu ena akuphunzitsira…

Dziwani kuti ngati pafunikira kuti anthu akufunikira kuphunzitsa zina zake mwachangu changu ndiye kuti sipakufunikanso kuchedwetsa koma kuwaphunzitsa anthu... Qaidah imanena kuti:

عدم جواز تأخير البيان عن وقت الحاجة

Ndi zoletsedwa kuchedwetsa ulaliki nthawi yomwe ukufunikira kwambiri, kutanthauza kuti ngati papezeka chifukwa china chake chomwe pakufunikira kuti anthu awunikiredwe ,ndizoletsedwa kuchedwetsa kuwaphunzitsa anthu pomwe akufunikira kuphunzitsidwa kwambiri..

𝑲𝒐𝒎𝒂𝒏𝒐 𝒏𝒈𝒂𝒌𝒉𝒂𝒍𝒆 𝒛𝒊𝒍𝒊 𝒄𝒉𝒐𝒏𝒄𝒉𝒊 𝒑𝒂𝒍𝒊 𝒛𝒊𝒏𝒕𝒉𝒖 𝒛𝒊𝒏𝒈𝒂𝒑𝒐 𝒛𝒐𝒇𝒖𝒏𝒊𝒌𝒊𝒓𝒂 𝒌𝒖𝒛𝒊𝒘𝒖𝒏𝒊𝒌𝒊𝒓𝒂 𝒎𝒐𝒏𝒈𝒂 𝒊𝒛𝒊:

1) Mtumiki (ﷺ) zolalikira pa maliro zi kapena kumanda sichinali chizolowezi chake amkalalikira pokha pokha pomwe pafunikirapo ,simaliro aliwonse omwe amkalalikira ayi, panayikidwa maliro ambiri mu umoyo wa Mtumiki (ﷺ) omwe sipanalalikidwepo…. choncho zinthu zomwe Mtumiki (ﷺ) sanazisandutse chizolowezi zimakhalanso zoletsedwa kuzisandutsa chizolowezi, kumeneko kumakhala kusemphana ndi Mtumiki (ﷺ)...

2) Mtumiki (ﷺ) pa maliro kapena ku manda amkalalikira atakhala pansi komanso anthu omvera amakhala momuzungulira ,choncho pofuna kutsata chiphunzitso cha Mtumiki (ﷺ) pakafunikira kulalikira olalikira yo ayenera akhale pansi komanso omvera ulalikiwo akhale pansi..izi zikuthanthauza kuti omwe amayima lero lino mkumalalikira anthu atakhala khala ndi zosemphana ndi chiphunzitso cha Mtumiki (ﷺ)..chifukwa ma hadith onse akuphunzitsa kuti Mtumiki (ﷺ) anakhala ndipo ife tinakhala mbari mwake momuzungulira…palibe hadith yoyima mkumalalikira ku maliro kapena ku manda...

3) Mtumiki (ﷺ) amkalalikira uku mkuti ntchito yokonza manda ikugwirika osati ntchito imayima ayi …

Choncho apa tidziwe kuti anthu omwe amayima mkumalalikira amakhala akulakwitsa chifukwa zoyenera mogwirizana ndi chiphunzitso cha Mtumiki (ﷺ) ndi kulalikira olalikira yo atakhala pansi komanso omvera akhale pansi,kmanso zisasanduke chizolowezi chifukwa Mtumiki (ﷺ) sizinali chizolowezi chake..kuti maliro ali onse afumikra alalikire ayi.

BREAKING: Iran's Supreme Leader Ayatollah Ali Khamenei has been killed and his body has been found, reports Reuters, cit...
28/02/2026

BREAKING: Iran's Supreme Leader Ayatollah Ali Khamenei has been killed and his body has been found, reports Reuters, citing Israeli media reports.

Mtsogoleri Wamkulu wa Iran Ayatollah Ali Khamenei waphedwa ndipo thupi lake lapezeka, malinga ndi malipoti a Reuters, ponena za malipoti a atolankhani aku Israeli.

koma Akulu akulu ku Iran akuti Tsogoleriyu alimoyo ndipo alakhula ku Mtundu wa Anthu posachedwapa.


🔴 LIVE updates: aje.news/s9152d

NKHANI ZOMWE ZILI MKAMWA MKAMWA ZIMENE ZIKUCHITIKA PA USIKU WA 28 FEBRUARY 2026pomwe Israeli Prime Minister Benjamin Net...
28/02/2026

NKHANI ZOMWE ZILI MKAMWA MKAMWA ZIMENE ZIKUCHITIKA PA USIKU WA 28 FEBRUARY 2026

pomwe Israeli Prime Minister Benjamin Netanyahu akunena kuti pali zizindikiro zoti Ayatollah Ali Khamenei, mtsogoleri wa pa mfundo za boma ku Iran, wafa pomwe Ma bomba a US ndi Israel agwera ku nyumba Kwake

Netanyahu akunena kuti pali zizindikiro kuti Khamenei ‘satha kukhala ali ndi moyo’ pambuyo pa mazana a ma bomba a US‑Israel omwe atsekula nyumba zoyambira za mtsogoleriyo ku Tehran.
kuphatikiza kubowola malo ena okhudzana ndi utsogoleri wa Iran ndi pulogalamu yake ya nyukiliya.

Komabe, palibe umboni wovomerezeka kuti Khamenei wafa kapena kuti ali ndi moyo,
kuchokera kumabungwe a boma lililonse la Iran, la United States kapena la Israel.

Iran ikuti mtsogoleri wake ali ndi moyo, ngakhale kuti Ma news akupitilira popanda umboni weniweni.

Netanyahu akulangiza anthu aku Iran kuti adzuke ndi kuchita zomwe iwo amawona kuti ndi zoyenera ndi kulimbikitsa kuti boma lawo lisinthe, pomwe limodzi ndi US akupitiliza kuwononga malo a utsogoleri wa Iran.

22/12/2025

Sheikh Siraj Hussein writes:

ومن طلب غريب الحديث كذب

NDIPO AMENE AMASAKASAKA NKHANI ZA CHILENDO AMANAMA.

Kavuto kena komwe kamapezeka mu zifuwa za ma student panthawi yomwe akusakasaka maphunziro a deen ndi:-

Kufuna kubweletsa zinthu za new-one kugulu zoti ambili sanazinveko ndi cholinga choti apange shine pamaso pa anthu.

Ndizodziwika kuti munthu amene ali ndi Ilm yambiri komaso amadziwa zinthu zambili zoti ena samadziwa, amakhala munthu osililika komaso oyamikilidwa ndi anthu. Zimenezi zimapangitsa ma student ena kuti akomedwe ndipo azisakasaka zinthu zooneka za chilendo komaso zosowa cholinga anthu akazinva, aziwayamilira ndikuwaona kuti iwo ndi ozama pa Ilm.

Mchitidwe umenewo umakhala ndi mavuto ambiri kuyambira kwa iwe student komaso anthu okutsata. Apart from kusowetsa Ikhlaas, mavuto ena awili akulu omwe amabwela ndi mchitidwe umenewo ndi awa:-

1. Kuthawitsa anthu kuti asanve uthenga wako.
Munthu ukakhala kuti nkhani zako za deen zomwe umabwela nazo nthawi zonse zimakhala zachilendo komaso zosemphana ndi zomwe anthu amaziziwa, anthu amakukayikira ndipo amakutenga ngati ndiwe munthu wabodza ongofuna attention. Mentality imeneyo imadza poona kuti mchifukwa chani awa nthawi zonse amabwela ndi zinthu zoti ena sakamba? Tiziti odziwa ndi iwo okha? Nde anthu amakukayikira.

2. Kuwapatsa anthu uthenga osathyakuka pa kafukufuku.
Pokhala kuti iweo cholinga chako ndichakuti uwapatse anthu uthenga wa chilendo, sumalabada kwambiri za tsatane tsatane wa uthengawo. Sumafufuza kuti ma Ulama ena anati chani pa nkhaniyo, koposaposa sulabada kuti mchifukwa chani nkhaniyo ili yosaziwika ndi yosatchuka pamaso pa ambili.

Mu Sharh ya Aqeedah twahawiyyah ya Naasr Al Aql polongosola mawu a Abu Yusuf onena kuti

Munthu amene amafunafuna nkhani za chilendo amazanama anatu:-

إذا طلب غريب الحديث -سواء ما يتعلق بالأحاديث المكذوبة مثلاً أو بالأحاديث التي فيها نوع من الإشكال أو الاشتباه أو غيرها-

Munthu akamasakasaka nkhani za chilendo kaya zikhala ma Hadeeth abodza kaya nkhani zoti nkati mwake muli ma complications kapena kulowana kapena kusakanikirana kapena zina zotero

وولج في هذا الباب وأكثر منه فلابد أن يتأثر على نحو يجعله يتعلق ببعض الإشكالات،

Ndikulowa pa khomo la nkhani zimenezi nkumachulutsa za izi, munthu ameneyo zimapezeka kuti basi amakhala ndi zinthu zoti zimampangitsa kuti alowe mma complications ena.

فتثير في نفسه الشك، أو تجعله ممن يثيرون الشكوك بدعوى أن عنده علماً وأن عنده طرائف، وأن عنده أشياء ليست عند الناس،

Nde amatha kuzibweletsera zikayiko mu mtima mwake kapena kuwabweletsera ena zikayiko poganizira kuti iye ali ndi ilm yoti ena alibe kapena ali ndi zinthu zoti ena sazidziwa.

فيقع في هذه الظواهر التي تئول بالإنسان إلى الكذب والدجل والشك والريب.

Nde amagwela mu izi zomupititsa ku kunama, kupena chinyengo komaso chikayiko

Sheikh Manyamba Abdul Aziz writes:وَلَأُضِلَّنَّهُمْ وَلَأُمَنِّيَنَّهُمْ وَلَآمُرَنَّهُمْ فَلَيُبَتِّكُنَّ آذَانَ الْأَ...
22/12/2025

Sheikh Manyamba Abdul Aziz writes:

وَلَأُضِلَّنَّهُمْ وَلَأُمَنِّيَنَّهُمْ وَلَآمُرَنَّهُمْ فَلَيُبَتِّكُنَّ آذَانَ الْأَنْعَامِ وَلَآمُرَنَّهُمْ فَلَيُغَيِّرُنَّ خَلْقَ اللَّهِ ۚ وَمَن يَتَّخِذِ الشَّيْطَانَ وَلِيًّا مِّن دُونِ اللَّهِ فَقَدْ خَسِرَ خُسْرَانًا مُّبِينًا

Surat An-Nisaa’ (4:119)

“Ndithu ndidzawasokeretsa, ndidzawapatsa ziyembekezo zabodza, ndidzawalamulira motero adzadula makutu a ziweto, ndipo ndidzawalamuliranso motero adzasintha chilengedwe cha Mulungu. Ndipo aliyense amene amamupanga Satana kukhala mtetezi wake kusiya Mulungu, ndithu watayika kutayika koonekera.”

Kusintha chilengedwe nkoletsedwa kwa Msilamu munjira iliyonse yomwe angaichitire, kaya ndi HD yokhala ndi filter yosintha mmene munthu alili kapena kudzola mafuta osintha chilengedwe( oyeretsa) kukuza zida, ma hip, mabere, matako, kukuza maso, njira ya operation, , , ma apps kapena ma software ndi kumwa mankhwala zonsezi ndi Haram.

Address

Sankontshe Masjid, Hammarsdale, , Mr430 Road, Sankontshe, Ilanga, 3700
Hammarsdale
FEARALLAH

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when One Ummah Islamic Foundation of Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Place Of Worship

Send a message to One Ummah Islamic Foundation of Malawi:

Shortcuts

Share