01/09/2026
*AKUFA KU TCHIMO*
Hallelujah!!
Kumwamba kulandile ulemu chifukwa cha moyo komaso nthawi yomwe tapasidwa, moti ndichisomo ndithu kupezeka ndi moyowu Hallelujah!!!
Lero Mulungu mwabvumbuluso akufuna kutitengela kuchiziwitso pama Funso awiri; Loyamba ndi lonena kuti :
*[1]_(AKUFA KU TCHIMO, ZIKUTATHAUZANJI?)_*
Hallelujah!!!!
Mwa mau wopezeka m'buku la *(Aroma 6:11)*
Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa Ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu
__________
So kutengela ndi mau omwe tawelenga tiwona za *IMFA* Kuti ndichiyani ndipo yimakhala yotani, kuyakha kapena kufotokozela kwa gawo ili, zitisogolela kuzindikila za tathauza LA Funso loyamba Hallelujah!
Tikamati imfa, ndichithu chomwe chimadza ku chithu chilichonse cha moyo, ndipo imfayi yimaza mwazizi, ndipo imfa yikakumana ndi chithu cha moyo, nde kuti chamoyochi chimasiya kugwila nchito iliyonse, chifukwa, mtima umasiya kugunda ndipo magazi amawuma mphweya umachoka Hallelujah!! So m'menemu ndimomwe imfa yimakhalila
So *UTCHIMO* Umakhala wa moyo, pa moyo wamunthu wina aliyense amene akuchita..... So kukhala akumfa kuuchimo nde kuti kusamvomekeza kuyenda kapena kuchita choyipa, kumene kuja kumfa Ku utchimo, chifukwa uchimo uja sugwilaso nchito pa iwe, monga tamvela kuti chakufa sichimachita kalikonse Hallelujah!!
So chilakolako chomwe chimabwela kuti tichite chigololo, kapena kuonela zolaula or kuzigona tokha, zimachitika pa ife chifukwa choti uchimo uja uli active, koma titavomekeza kumulandila Yesu, uchimo umafa ndipo zilakolako zathupi sizimakula mphamvu Hallelujah!!!!!!!
______________________
Tiyimile apa lero
Ndipo tipitiliza pa verse lomweli kuona za *KUKHALA A MOYO MWA MULUNGU* Kuti zimatathauza chani
*_MTUMIKI JOSHUA_*
Funso kapena ndemanga 0880310689
Kwamene muli pa group funsani pa group popa tiyakha
AMEN AMEN