06/09/2026
Mwambo wansembe ya Ukaristia ya Chaka Cha Ulimbitso komanso wotsekulira mwezi wa Bible pa mzere wa Dayosizi uli mkati ku Holly Trinity Matawale Parish mu Diocese ya Zomba ndipo ukutsogoleredwa ndi Ambuye Alfred Mateyu Chaima omwe ndi Episkopi wa Diocese ya Zomba.
Ku mwambowu kwafika akhristu eni ake ochokera mma out church ozungulira Holly Trinity Matawale Parish pofuna kudzachitira umboni kulimbitsidwa kwa Ana awo. Ana amene akulandira Sacrament la Ulimbitso mu tsiku la lero ndi ana okwanira 200.
Mu ulaliki wawo Ambuye Alfred Mateyu Chaima alangiza makolo a ana amene alandira Sacrament la Ulimbitsoli kuti ayesetse kuwalimbikitsa anawa kulowa mmagulu osiyanasiyana a mumpingo komaso kuti ayenera kumabwera ku church mokhulupirika. Ndipo Iwo anatsindika ponena kuti mwa anawa akuonamo Asistere komaso Ansembe.
Chaka ndi Chaka mwezi wa September mpingo wa Katolika umachita Chaka Cha Bible ndipo ku Dayosizi ya Zomba mwambo waukulu wotsekulira mwezi wa Bible ukuchitikira ku Holly Trinity Matawale Parish.