06/06/2026
KODI CHIKUKU CHIMATANTHAUZANJI?
By Fr. J.E Manyoni, Dp - Namitete Parish, Lilongwe
Ndinalandira funso kuchokera kwa inu a Salah Kaunda komanso a Mary Msiska, kuti kodi Chikuku Chimatanthauzanji kwenikweni. Tsono ndinaona kuti funsoli lisangothera ku comment section koma lithandizenso ena kuti amvetse bwino za yankho lake.
✝️ Poyambirira penipeni tidziwisaneko kuti mau oti Chikuku ndi olakwika makamaka ngati tiwagwiritsa ntchito pofuna kutanthauza Chikondwerero cha Thupi ndi Magazi a Yesu Khristu.
Mau amenewa adayamba kugwiritsidwa ntchito ndi makolo athu kuno ku Malawi potengera zimene zinkachitika pa tsiku lokondwerera Ukaristia.
Paja tikamaliza Nsembe ya Ukaristia, wansembe atanyamura Ukaristia, mophathana ndi akhristu eni ake amayenda mdipiti wosangalalira Ukaristia. Ndipo pamdipiti umenewu wansembe amanyamura Ukaristia mu Monstrus ndipo anthu ena amamuphimba ndi ka tent kapena tinene kuti kachikuku.
Ndiye makolo athu chifukwa chosowekera mau olondora a chikondwerero chimenechi amauzana kuti akupita ku Misa ya Chikuku. Choncho mau amenewa adafalikira ndithu.
Koma pofuna kupereka tanthauzo lenileni la chikondwerero cha tsikuli, Mpingo kuno kwathu wakhara ukutipempha kuti tisiye kugwiritsa ntchito mau oti CHIKUKU. m'malo mwake tiziti CHIKONDWERERO CHA THUPI NDI MAGAZI A KHRISTU, Kapena kuti CHAKA CHA UKARISTIA.
Ngati tifuna kudziwa zambiri za CHIKONDWERERO CHA THUPI NDI MAGAZI A KHRISTU,
Ndikufunireni kukozekera kwabwino kwa CHIKONDWERERO CHA THUPI NDI MAGAZI A KHRISTU, chomwe chichitike Lamulungu likubwerari.
ZIKOMO KWAMBIRI POWERENGA, MULUNGU ATIDALITSE TONSE NDIKULIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHATHU.
🙏🙏