EverJoy SeventhDay Pentecost Church Ministries

  • Home
  • EverJoy SeventhDay Pentecost Church Ministries

EverJoy SeventhDay Pentecost Church Ministries (Bringing Joy to Joyless Souls)

Welcome to Everjoy SeventhDay Pentecost Church Ministries:
• Seeking God's Kingdom is our Foundation.
• Matthew 6:33 --Seek first the kingdom of God and his righteousness, and all these things will be given to you as well.

-- Mateyu 6:24 --_Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winay...
12/04/2026

-- Mateyu 6:24 --

_Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma._

A little Brief:

Inu ndiinu ambassador wa kumwamba, oimilira dziko la kumwamba. Muli mdziko muno, koma kwathu ndi kumwamba.

- ngati tili ambassador, ndekuti solution ku bvuto lilironse lathu ndi yochokera ku dziko lakwathu

- ambassador amaimira dziko la kwawo, zakudya zake ndi za dziko la kwawo,
- anthu kuti adziwe za culture ya kwawo anaonera pa iye.

Ambassador salankhula maganizo ake, koma zomwe president wakwawo walankhula.
- ambassador akalankhula ndekuti dziko lake lalankhula.

Ambassador simungamuone ku zinjoyi kapena kumpeza ataledzera.
- Akaledzera ndekuti dziko lakwawo laledzera.
- Ngati ali ambassador wa ku America ndekuti America yaledzera.

Ngakhale embassy/office yake ikhale mu dziko losauka, koma umphawi wa mdzikomo siwungamulepheretse iye kudya zonona zakwawo.
- ngakhale galimoto limene amakwera linayenera kukhala lopangidwa kwawo.

Ambassador wa America sizitheka kukhala mbadwa or mdzika ya dziko lino.
- Choncho kapolo saakhala wa Ambuye awiri.
- Sungakhale wopemphera, nkudzakhala wa za mdziko. Chimodzi chikuyenera chife kuti china chikayende.

Kodi inu ndi ine tikupanga reflect kapena kuimilira dziko liti?
Zochita ndi zoganiza zathu zilidi moyimilira kumwamba?

Ufumu wa Mulungu sukudikira kudzalowamo popeza mwalowa kale ngati Mfumu ili mwa inu.

Pa Luka 17:21 mmwambamo akunena kuti Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu.
- nde ngati uli mkati mwathu, therefore; authority/ulamuliro uli ndi ife.

Declaration:

1. Chilichonse chimakuberani umwini zinthu, ulamuliro, komanso mphamvu yanu, chife mu Dzina La Yesu Khristu.

2. Zisomo ndi chifundo ca Mulungu chikumbukire inu, maka zabwino zonse munazichita ku ntchito ya Mulungu: zopereka zanu, kuzipereka kwanu ndi chikondi chanu.

3. Akangaude onse otchingira ndi omanga kutseka madalitso anu aduke, mu Dzina La Yesu Khristu Ambuye.

🕊️"EVERJOY MINISTRIES FAMILY"📖

GOOD FRIDAY PRAYERLord Jesus Christ,  on this holy day of Your Passion,  I pause before Your Cross with a humbled heart....
03/04/2026

GOOD FRIDAY PRAYER

Lord Jesus Christ,
on this holy day of Your Passion,
I pause before Your Cross with a humbled heart.

You carried my burdens,
You embraced my wounds,
You loved me to the very end.

May Your sacrifice cleanse my soul,
soften my heart,
and draw me closer to Your mercy.

Teach me to forgive as You forgave,
to love as You loved,
and to trust the Father as You trusted Him.

Jesus Crucified,
have mercy on me,
on my family,
and on the whole world.
Amen.

🕊️"EVERJOY MINISTRIES FAMILY"📖

CHIPHUNZITSO CHA IMFA ndi KUWUKA KWA YESU KHRISTUAliyense amaopa imfa, ndipo ikafika nthawi imeneyi anthu amatha mnzeru:...
02/04/2026

CHIPHUNZITSO CHA IMFA ndi KUWUKA KWA YESU KHRISTU

Aliyense amaopa imfa, ndipo ikafika nthawi imeneyi anthu amatha mnzeru:

- za imfa sitifuna kulingaliranso
- imfa palibe angailesetse.
- siyithawika
- paimfa ndalama ndi ma degree saapereka mayankho.

Zipembezo zambiri zimakamba za imfa, koma sizipereka mayankho enieni, mmalo mwake zimaonjezera chisoni ndi kulira.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

Muli ndi ine Rev. Sangwati.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::

-- AHebri 9:27 --
- Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, ciweruziro.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Okondedwa wathu akamwalira, amakhala wangosintha malo okhala;

- Ngati wanyamuka alibe cholemetsa, amakasungidwa malo abwino, ongoyembekezera tsiku lenileni lomaliza

- Ngatinso sananyamuke bwino, amakasungidwanso malo, ozunzika, koma ongoyembekezera tsiku lomakizanso.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

-- AHebri 2:14-15 --
14. Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi.

15. Nakamasule iwo onse amene, cifukwa ca kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Pa chifukwa choti imfa inali ndi mphamvu pa munthu, Yesu Khristu Anazipereka kukagonjetsa imfa mmalo mwathu, kuti tikawomboledwe ku chilango chathu.

Imfa inalengedwa ndi Mulungu, ndipo inali pambali pa moyo, mmunda mwa Eden muja, koma inalibe mphamvu ilionse pa munthu.

Why? Chifukwa munthu anali ndi ulamuliro wonse pa imfa, komanso zonse zinali mdzikoli.

Inali ngati, chinjuchi chopanda sting/mbola. Kapena mkango opanda mano.

Koma pali chinthu chimodzi chomwe chinalakwika kuti imfa ikakhale ndi mphamvu, kuti ikakhale yamoyo pa munthu.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

-- Genesis 2:16-17 --
16. Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko;
17. koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa, usadye umenewo; cifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Kusamvera ndilo tchimo lomwe linapereka mphamvu ku imfa yomwe inali chete mdzikomu.

Meaning: Adam anali ndi choice chosankha kumvera, kapena kusamvera.

Therefore: rebellion made sin, and sin activated death, and death killed a man.

Kusamvera kunabweretsa tchimo, nde tchimo lipereka mphamvu imfa kuti ikayambe ntchito yake yomwe anaipangira. Kenaka imfa inaphano munthu.

Apanso zikutitsimikizira kuti;
Imfa inalengedwa ndi Mulungu, osati satana. Koma ntchito yomwe satana Lucifer amachita ndi kukunyenga, kukupusitsa, uparamule nde akuthawe.

Zikutanthauza kuti; munthu ali ndi choice cholibvomereza ntchimo, kapena ayi mopanda kukakamizika ndi satana.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

-- Genesis 3:1-5 --
1. Ndipo njoka inali yakucenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu, Ndipo inati kwa mkaziyo, Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?

2. Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m'mundamu tidye.

3. Koma zipatso za mtengo umene uti m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.

4. Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;

5. Cifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Tonse amene tinabadwa ku mbewu ya Adam tinabadwa mu mbewu ya uchimo ndithu, ndipo tchimo linasefukira kuchoka kwa munthu mmodzi/banja lija.

Kutanthauza kuti: Adam ndi mkazi wake ngati munthu mmodzi anafa kuti Mawu a Mulungu, lomwe linali lamulo, akakhale owona, chifukwa Mulungu Akalankhula limakhala lamulo pompopompo.

Anachita kutsimikiza, "udzafa ndithu" kunali kulumbira, kuti ufune usafune, ukadzadya udzafa ndithu.

Adam anafa kuti Mulungu mawu Ake akhale owona;
- popeza Iye ndi okhulupilika pa Mawu Ake, ndipo Akalankhula, Naye Mulungu Amawatsatira Mawu Ake.
- ndipo limakhala lamulo ngakhale kwa Iye Mulungu, kuti Akhale owona ndi okhulupilika pa mawu Ake.
.. All people became the victims of sin. So Jesus Christ came to deal with the spirit of sin, not death, bcoz sin brought death to a man.

Why? He (Jesus )was not fearing death, bcoz he came obeying everything that God wanted.

Apapa munthu anakhala kapolo wa imfa kudzera mwa munthu mmodzi uja Adam, nde Yesu, ngati Adam omaliza, Anabwera kudzamvera chilichonse chomwe Adam oyamba uja anachikanika, nangoluzapo mphamvu ndi ulamuliro wake.. pokhala padziko lapansi.

Tchimo lomwe linaipitsa dzikoli ndi kubweretsa mabvuto omwe tikuwaona lerowa ndilo "KUSAMVERA"

Nde Mulungu sanakondwelebe kuti munthu opanga Yekha, kuti akalangidwe ndi ukali Wake wonse ayi. Chinamuwawa kwambiri Mulungu.
Apa ndi pamene pagona chikondi cha Mulungu.

Komabe poti Mawu Ake kuti akakhale okhulupilika, kumayenerabe kuti munthu wina AKAMUZINGE, AKAKHETSE MWAZI kuti munthu akafe ndithu, kukwaniritsa Mawu a Mulungu, koma anthu onse akhalebe opulumuka ku chilamulo cha imfa.

Koma nanga ndi ndani anakakwanitsa zimenezi, popeza anthu onse ndi ochimwa?
Chifukwa akafa ochimwa, imfa ikawasungabe ku ndende. Ndipo satana zimenezi amazidziwa bwino lomwe, moti anali kuseka phwete lamwano pamaso pa Mulungu kuti tikuwonerani kuti musova bwanji, ma key ndalama popeza munthu wanu wandimvera ine.

Nde Yehova Mulungu wamphamvu zonse Analamula mwana wa nkhosa, wofatsayo, wokhala ku dzanja lache la manja kuti, MWANA WANGA, PITA UKAKHALE Munthu pakati pawo, chilango Ichi ukachibvale ndi iwe, ukachite zonse zomwe ndakulamula, ukhale chitsanzo chakumvera.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

-- Yesaya 52:13-15 --
13. Taonani, Mtumiki wanga adzacita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.

14. Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israyeli, momwemo nkhope yace yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu ali yense, ndi maonekedwe ace kupambana ana a anthu;

15. momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti cimene sicinauzidwa kwa iwo adzaciona, ndi cimene iwo sanamva adzazindikira.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Ndipo lonjezo ili lakubadwa kwa Yesu Khristu linaperekedwa ku;

-- Genesis 3:14-15 --
14. Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Cifukwa kuti wacita ici, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya pfumbi masiku onse a moyo wako:

15. ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi MBEU YACE; NDIPO IDZALALIRA MUTU WAKO, ndipo iwe udzalalira citende cace.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Mbewu iyi, yomwe ili Mesiya mwiniwake, inali solution yomwe inaperekedwa munthu atangochimwa, ngakhale Adam asanafunsidwe kuti wachita chiyani.

Zikutanthauza kuti;
Mulungu mwiniwake.. anazikhalitsa munthu, nkuzipachika Yekha, kuti akathetse chilamulo cha imfa pa munthu chisakagwire ntchito.
This is the HIGHEST LOVE OF GOD.
Popeza Yesu akuti; Ine ndi Atate ndi Amodzi,
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

-- Yohane 10:30 --
Ine ndi Atate ndife amodzi.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

So, satana akuwonelera mission yonseyi, koma chomwe saakudziwa ndi choti;
- zitheka bwanji kuti iwe (Yesu) ufe, chifukwa munthu kuti afe akuyenera kukhala ochimwa.
- Iwe ndi oyera, ndipo zowona sunachimwepo. Koma ufa bwanji. That's why satanayu akubwera kudzamuyesa, mchipululu muja, kuti ngati uli Mwana wa Mulungu, sanditsa mwalawo ukhale mkate udye, ndipo ziponye adzakuwakha.

Mateyu 4:1-11
Mariko 12-13
Luka 4:1-13
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Pamafunika mwazi wa munthu ukakhetsedwe ndithu, popeza msembe za nyama zimafunika chaka ndi chaka pa munthu aliyense.

- Nde sitinalakwanitsa aliyense azipha ng'ombe kapena nkhosa chaka chilichonse ndi ana athu onse.
- Komanso chilango cha imfa chija chinanenedwa pa munthu, osati pa nyama.

Lonjezo la kudza Kwake linabvumbulutsidwanso kwa Yesaya mneneri.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

-- Yesaya 53:2-12 --

2. Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pace ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.

3. Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeza.

4. Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuvesa wokhomedwa wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wobvutidwa.

5. Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natundudzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu; cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa.

6. Tonse tasocera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.

7. Iye anatsenderezedwa koma anadzicepetsa yekha osatsegula pakamwa pace; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pace.

8. Anacotsedwa ku cipsinjo ndi ciweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wace? pakuti walikhidwa kunja kuno; cifukwa ca kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.

9. Ndipo anaika manda ace pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yace, ngakhale Iye sanacita ciwawa, ndipo m'kamwa mwace munalibe cinyengo.

10. Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wace ukapereka nsembe yoparamula, Iye adzaona mbeu yace, adzatanimphitsa masiku ace; ndipo comkondweretsa Yehova cidzakula m'manja mwace.

11. Iye adzaona zotsatira mabvuto a moyo wace, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zace mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.

12. Cifukwa cace ndidzamgawira gawo ndi akuru; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wace kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula macimo a ambiri, napembedzera olakwa.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

This is the real Jesus Christ the messiah

Komanso ku
-- Malaki 3:1-6 --
Za mthenga wokonzeratu njira ya Ambuye:

1. Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kacisi wace modzidzimutsa; ndiye mthenga wa cipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.

2. Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwace? ndipo adzaima ndani pooneka Iye? pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;

3. Ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'cilungamo.

4. Pamenepo copereka ca Yuda ndi Yerusalemu cidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija ndi ngati zaka zoyamba zija.

5. Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi acigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa nchito pa kulipira kwace, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

6. Pakuti Ine Yehova sindisinthika, cifukwa cace inu ana a Yakobo simunathedwa.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Khristu Anabvomera kuwusiya ulemelero wonse, wa Mulungu, nachibvumbulutsa ichi kwa aneneri akale aja.

Remember Jesus is not an Angel. Si mngero Yesuyu, koma Angelo amagwada natumikira Iye ngati Prince okalowa mnyumba ya Mulungu.
Palibe analowamo mnyumba ya Mulungu, koma Christ Jesus/Yesu Khristu ndiye akudziwamo.

Uyu ndi yemwe amanyamuka pemphero la inu ndi ine, kukatipepesera pamaso pa Atate.

Ngati tipemphera osatchula Dzina La Yesu, pemphero silifika kwa Atate.

Ndipo Atate Amayankha pomukonda Mwana wawo Wokondedwa uyu.

Remember uwu ndi Ufumu, si boma la democracy lofuna kuvota, kusintha mtsogoleri ayi. So, boma la chifumu, zonse za mdzikomo zimakhala za mfumuyo.

Ndipo mabvuto onse a mdzikomo okonza imakhala mfumuyo.

Nde kwa mfumu, sumupita nokha direct.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

Choncho amene akupachikidwa pa Good Friday ndi Mwana woyamba wa mwamuna, wa Mfumu,
- kufera mbabva zonse zili kunjako,
- kufera onse oyenda ndi maliseche.
- kufera onse onyoza ndi kutama mnzeru zawo ndi chuma chawo.
- kufera onse otama kukongola kwawo.
- kufera onse amene amati Mulungu kulibe, napembeza azising'anga, nalowa usatanic, nakhwima, kuchita zaufiti ndi zambiri

Chifukwa cha kuzichepetsa kwake pamaso pa Atate Wake, analibvala thupi la munthu, koma sanalore kuti akabadwe ndi mbewu yamwamuna, munthu ochimwa ujanso ayi, ngakhale sanakhudzana ndi thupi la mkazi ayi.

Mutafufuza bwinobwino, sipamakhala kukhudzana pakati pa mwana ndi mayi ake mmimba.

Chifukwa cha ululu pamtanda paja, anayesetsa kupempha Atate kuti mwina asinthe maganizo, koma Mulungu ndi okhulupilika pa lonjezano Lake, moti sanalorenso kuti kuti achibweze chilango ichi.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

-- Mateyu 27:46 --
46. Ndipo poyandikira ora lacisanu ndi cinai, Yesu anapfuula ndi mau akuru, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

It was too painful;
Thupi lake linaima pa misomali, and thupi lake kumva kuwawa kwake kunali komwe inu ndi ine timamva panalibe kuti uyu ndi mwana wa Mulungu.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

-- Mateyu 27:50-53 --
50. Ndipo pamene Yesu analiranso mofuwula, anapereka mzimu wake.

51. Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika.

52. Manda anatsekuka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera mtima amene anafa inaukitsidwa.

53. Anatuluka mʼmanda mwawo, ndipo chitachitika chiukitso cha Yesu, anapita mu mzinda woyera naonekera kwa anthu ambiri.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Apa ndi pamene pali pachimake pa kutulutsidwa kwa anthu a Mulungu, mu ndende yomwe imasunga aneneri onse omwe anachita bwino, koma amasungidwa ndi ndende za imfa zomwe zinali mmanja mwa Lucifer satana mdyelekezi.

Apa kunali koyamba mu history, imfa kuwona munthu osachimwapo chiyambile akulowa mu ndende.

Nde popeza imfa siyisunga munthu amene sanachimwepo, inagwada pansi kupereka mphamvu kwa Yesu Khristu ndi kulanda ma key a zipinda zonse zomwe zimasunga onse omwe amakhulupilira Mulungu.

Awa anatulutsidwa, ndikukasiyidwa malo a mtendele. That's why apo bible analemba ngati anauka kuwoneka ku dziko, koma zinachitika mu system ya kuuzimu, mu nthawi yomwe chinsalu chinang'ambika, ndinso chibvomerezi chinagwedeza, popeza kunali ma billion a mizimu ya athu kumalo kumeneku.

Mwa chifukwa ichi, mission ya Yesu Khristu, mu gawo loyamba inatheka.

Kwatsala kubweranso kwake, kudzatenga oyera mtima onse, mu mkwatulo, akakhalebe malo abwinowo, kufikira kutachitika chiweruzo chotsiriza. Akamubwezeretse munthu ku dziko lapansi, koma lokonzedwa mwatsopano, limene sitidzawonamo adani athu onse aja anakutsendezani, kukunyozani, kukulabvulani ayi.

Umu mulibe corruption, mulibe chinthu chako chako ayi, mulibenso mdima ayi, koma dziko lowala kowopsa, mmene simudzakhala kodetsa kalikonse.
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

-- Mateyu 6:33 --
Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::📖:

Inu ndi ine tiwufunefune ndi kukhala ana a ufumuwo, wa Mulungu, ndipo akuti zonse timazifunazo, zidzabwera mongowonjezera ngati kampunga komwe mwagula moyezetsa, amapatsira kumapeto. Moti sizingatheke kuyamba kuitanitsa owonjezera munagule, ndekuti sangakupatseni, muwoneka ngati okuba.

Ndekuti onse opempha asali ana a ufumuwo ndi akuba, awa akapeza amasiya kupemphera nkukalowelera, kukasakaza mwachikunja zabwino zija. Dalitso limapangidwa misuse.

Ambuye Akhale Nanu mu zonse 🙏
📖:::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️
🕊️"EVERJOY MINISTRIES FAMILY"📖

DANGEROUS: HIDDEN SECRETS GOING ON TO ALTER THE BIBLEA MUST READ IF YOU ARE A TRUE FOLLOWER OF CHRISTWhat a powerful and...
16/02/2026

DANGEROUS:
HIDDEN SECRETS GOING ON TO ALTER THE BIBLE

A MUST READ IF YOU ARE A TRUE FOLLOWER OF CHRIST

What a powerful and touching testimony. Please take your time and read it to the end.

ALTERATIONS OF BIBLE VERSES
By Amina Hassan

Some Of The Bible Verses Corrupted Or Deleted

- John 3:16
- John 14:6
- 1 Timothy 2:5
- Acts 4:12
- Romans 10:9
- 1 John 5:7

THE TESTIMONY

My name is Amina Hassan, and I am currently in Amman, Jordan. I am 34 years old. Just four months ago, I was living a completely different life in Riyadh, Saudi Arabia, working for an organization that most people do not even know exists.

But I need to tell you everything, because your faith, your Bible, and your understanding of God’s Word might already be compromised without you even knowing it.

For three years, I worked in the shadows changing the Word of God itself. We printed over one million fake Bibles and sent them across the world.

But one verse I was assigned to corrupt became the very thing that saved my soul. My name is on a hit list right now, and if they find me, I am dead.

What you are about to read is not just my story. It is a warning for every Christian on earth. We need to pray for each other and stay alert together.

I was born and raised in Riyadh as a devoted Muslim. My family was moderately religious, not extreme, but faithful to Islam in every way. I attended university and studied literature and linguistics, specializing in ancient texts and translation work. My skills with languages, especially Arabic, English, and French, made me valuable in ways I never imagined.

In November 2021, I was approached by a man who said he represented an Islamic educational organization. He offered me a job that paid extremely well, far more than any normal editing or translation position.

The work, he explained, involved reviewing and editing religious texts to make them more accessible to modern readers. It sounded legitimate and even noble. I accepted without hesitation. What I did not know at the time was that this organization was actually called Al Fath Al Kabir, meaning “the silent conquest.”
This was not just an educational group. It was a secret, well-funded operation with one ultimate goal: to make the entire world an Islamic state. Not through violence alone, but through infiltration, deception, and the systematic destruction of other faiths from within.

During my first month, I was introduced to the larger mission. The leadership explained that for decades, some groups had sponsored armed struggles across different parts of the world. Yet after years of conflict, they believed this strategy was not achieving their long-term goals. In many places, Christianity was actually growing, especially in Africa and Asia.

They realized they needed a new strategy. If they could not destroy Christianity from the outside, they would attempt to weaken it from the inside by corrupting the very foundation of the faith: the Holy Bible.

The plan was simple but dangerous. They would produce Bibles that looked identical to genuine ones. The same covers, paper, fonts, and layout. But inside, key verses would be altered. Not every word, only critical doctrines and essential truths about Jesus and salvation. The changes would be subtle enough that most readers might not notice.

My job, along with about thirty other editors and translators, was to make these changes. We worked in a secure facility that looked like a normal office from the outside but contained advanced printing equipment and a large database of Bible translations.

By late 2024, we had produced over one million counterfeit Bibles in multiple languages. These were distributed through various channels, including online retailers, bookstores, and free donations.

Some of the changes included altering verses to remove the divinity of Jesus, weaken the message of salvation by grace, and shift the focus toward human effort.

But everything changed for me on 19 November 2024. While working on the Gospel of John, I read the words of Jesus in chapter 15:
“I am the vine; you are the branches… apart from me you can do nothing.”
As I read those words, something inside me broke. I suddenly realized what I had been doing. I was not defending truth. I was helping to destroy it. Tears filled my eyes as I continued reading.

Later, I read about the Holy Spirit and Jesus’ prayer in John 17. I understood that eternal life was not about rules, but about knowing God personally through Jesus. For the first time in my life, I prayed to Him.

At that moment, I felt peace and love unlike anything I had ever experienced. I knew that Jesus was real and alive.

From that day, I secretly began reading the Bible. I compared the original text with the altered versions and was horrified. I knew I could not continue.

When my supervisors discovered my actions, I was imprisoned and beaten. I was told I would be executed. But through unexpected events, I escaped and eventually found refuge in Jordan.

Now I am sharing this testimony to warn Christians everywhere. Please examine your Bibles carefully. Compare them with trusted sources. Be alert. Know the truth of God’s Word.

Pray for persecuted believers around the world. Pray for wisdom, courage, and faith.
If you are seeking truth, know that Jesus is ready to receive you. He offers forgiveness, peace, and eternal life.

Stay strong in faith. Test everything. Hold fast to what is good. Pray continually.
Thank you for reading my testimony. Sharing this message may put me at risk, but I must speak. Too much is at stake.

May God bless you and keep you.
May His face shine upon you and give you peace.

May you stand firm in the truth of His Word. Amen.

I plead with you in the name of Jesus Christ: if you are a genuine Christian, help this message reach others.
✝️✝️✝️

🕊️EVERJOY✝️7thDay🔥PENTECOST(Church)MINISTRIES📖

Moni Abwenzi mwa Ambuye!Lingalirani za Buku la;-- Jeremiah/Yeremiya 29:11 --For I know the plans I have for you,” declar...
15/02/2026

Moni Abwenzi mwa Ambuye!

Lingalirani za Buku la;

-- Jeremiah/Yeremiya 29:11 --

For I know the plans I have for you,” declares the Lord;
- Plans to prosper you,
- And not to harm you,
- Plans to give you hope and a future.

Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova;
- Malingiriro a mtendere,
- Si a coipa,
- Akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.
📖::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::::🕊️

Jeremiah 29:11 is a powerful reminder of God's sovereign plans for our lives.
- It encourages us to trust in His goodness and surrender to His will 🙏.
- Every experience, whether joyful or challenging, is an opportunity to learn and grow.
- Just as gold is refined through fire, we too can emerge stronger and more radiant through life's trials 💪.
- Let's choose to obey God, trusting that He's working all things for our good, even when the path isn't clear 🌟.
----------------------------------------------------------------------🕊️
Okondedwa vesi limeneri, litikumbutse za chikondi ndi cholinga cha Mulungu potipanga ifeyo.
- Likutilimbikitsa za kudalira ndi kuzipereka kwathu kwa Mulungu.
- Chilichonse timakomana nacho, chabwino kapena choipa Mulungu Amaikamo chinachake choti chikakuwumbeni inu kukhala wabwino ndikuphunzira chatsopano, chokachitira ubwino tsogolo lanu.
- Monga golidi kuti awale, amalowa pamoto. Munthu wabwino amakhala kuti anamvapo kuwawa nthawi inayake. Ubwino siwumangobwera poyera.
- Ife tisankhe kumvera ndi kuchita chifuniro cha Mulungu kuti chifuniro chake chikakwaniritsidwe, popeza saatifunira zoipa koma zabwino nthawi zonse. Ngakhale nyengo ziwoneke zolusa, koma ife tisachoke pamaso pa Mulungu.

-- Rev. F. Sangwati --

🕊️Everjoy✝️7thDay🔥Pentecost(Church)Ministries

Moni anthu a Mulungu!Njira zina zothana ndi umphawi wakhomo:Zofunika:1. Kulemba maso mphenya2. Kuyambapo kuchita chinach...
12/02/2026

Moni anthu a Mulungu!

Njira zina zothana ndi umphawi wakhomo:

Zofunika:
1. Kulemba maso mphenya
2. Kuyambapo kuchita chinachake, kusakasaka, ndi kugwiritsa ntchito chomwe muli nacho
3. Kukhala osaziyang'anira pansi, ndi kupanga ma connection ndi anthu oyenera, aphindu okhaokha, osati okuyamwanso komwe uli nako. Koma okupanga build.
4. Osatafuniratu ka ndalama konse, kapena osagula zoti anthu akuwone. Apa pakhalenso tithe, seed ndi budget.
5. Seed udzale mu chinachake choti chizikaoanganso ndalama.

Ma Jews/Ayuda ku Israel jdu America amakhulupilira kupanga ndalama kuti izikupangira ndalama. Osati kuchikuda kwathu amati rimagwilira ntchito ndalama, koma iwo ndalama imawagwilira ntchito.

6. Go for your priorities, osagula zopanda plan, zomwe sizinali mma plan ako.. ukalemba siumaiwala.
7. Pangani maintain mtendele ndi mgwirizano wa khomo lanu/pabanja lanu chifukwa ngakhale ndalama imatupa, siisakazika.

Amen!

Moni anthu a Mulungu!Ndikhulupira muli bwino komwe muli.  Tiyeni tikhalebe anthu omapemphelerana nthawi zonse, maka tsog...
10/02/2026

Moni anthu a Mulungu!

Ndikhulupira muli bwino komwe muli.

Tiyeni tikhalebe anthu omapemphelerana nthawi zonse, maka tsogolo, chitetezo ndi kudalitsika kwa ife ndi mabanja athu.

Pemphero langa ndi loti;

• Zinthu zanu zikhale ziyenda bwino, kuti mukathe kukwaniritsa zokhumba za mtima wanu.

Note:
- Ndikulimbikitsani kuti mupeze hard cover ngati Visionary Book, muzilembamo ma plan anu zonse zomwe, maka zomwe mukufuna kudzachita ndi kukwaniritsa.
- Nde muzichonga chimene mwakwaniritsa, kaya ndi zofunika kuyamba kugula.

- Nde mukapeza ndalama, you just go straight kukapanga chinthucho, chinachake osalowelera.

-- Hahakuk 2:2-3 --
2. Ndipo Yehova anandiyankha nati, Lembera masomphenyawo, nuwacenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira.
3. Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pace, osanama; akacedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.

-- Habakkuk 2:2-3 --
2. And the Lord answered me, and said, Write the vision, and make it plain upon tables, that he may run that readeth it.
3. For the vision is yet for an appointed time, but at the end it shall speak, and not lie: though it tarry, wait for it; because it will surely come, it will not tarry.

• Bible limakambanso zolemba maso mphenya. Chilichonse chabwera mmutu lembani, ndikumachipemphelera, chifukwa ndalama ikabwera satana amaiwaritsa ma plan abwino onse.

• Nde mukalemba mumazipanikiza kuchita ndendende zomwe munalemba, and simulora kuti ndalama ipite ku zomwe simunalembe.

That's why anthu omwe amalemba masomphenya awo, nawapemphelera, nkuyambapo kuchita kanthu, zinthu zawo zimapita chitsogolo mosabvuta.

Ichi ndi chifukwanso ma antichrist akufuna kusowetsa ma bible kuti azilemera okha, chifukwa mu Bible muli njira zonse zopezera chuma ndi mabanja komanso umoyo wabwino.

Write it down, pray it through, and walk it out!

Habakkuk 2:2-3 reminds us to write our vision, make it plain, and wait for it.
Prosperous people plan, pray, and pursue their God-given vision.
What's your vision? Write it down, pray over it, and take steps to make it happen. The vision will speak, it'll come to pass, and you'll see it come to life. God bless you!

Yehova Mulungu Akudalitseni!

(Rev. Sangwati)

Address

P. O. Box 1928, Blantyre

312219

Telephone

+265888988882

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when EverJoy SeventhDay Pentecost Church Ministries posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Place Of Worship

Send a message to EverJoy SeventhDay Pentecost Church Ministries:

  • Want your place of worship to be the top-listed Place Of Worship?

Share