Phalombe Zone Adventist Youth Ministries

Phalombe Zone Adventist Youth Ministries Spreading the word of God in this generation

KUMAWAKUMBUKIRA AJA ANATITHANDIZA!Zilipo nthawi zina tinazingidwa ndi mavuto ndipo sitinadziwe koti titembenukire. Anthu...
20/07/2026

KUMAWAKUMBUKIRA AJA ANATITHANDIZA!

Zilipo nthawi zina tinazingidwa ndi mavuto ndipo sitinadziwe koti titembenukire. Anthu ambiri, kuphatikizapo amene tinkawadalira, analephera kutithandiza. Koma panabwera munthu amene mwina sankadziwika kwambiri, ndipo atatimvera chisoni anatithandiza.
Munthu ameneyo musadzamuiwale mukadzadalitsidwa. Ana ake musadzawaiwale. Chitirani iwo zabwino monga momwe iwo anakuchitirani zabwino.

Mawu a Mulungu akuti:
Miyambo 3:27
"Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino."

M'moyo uno:
1. Alipo amene tinali m'mavuto anatithandiza.
2. Alipo amene anatipatsa chakudya pamene tinalibe.
3. Alipo amene anatithandiza kupeza ntchito kapena mwayi wina.
4. Alipo amene anatipempherera ndi kutilimbikitsa pamene tinkafooka.
5. Alipo amene anatitsegulira chitseko chimene chinasintha moyo wathu.

Musawaiwale anthu amene Mulungu anagwiritsa ntchito kukuthandizani. Kuyamikira ndi chizindikiro cha mtima wabwino.

Copied pr chataika

Tizakhala ndi camp ya achinyamata mu zone mwanthumu kuyambila pa 6 mpaka pa 13 September chaka chomwe chino....
19/07/2026

Tizakhala ndi camp ya achinyamata mu zone mwanthumu kuyambila pa 6 mpaka pa 13 September chaka chomwe chino....

π—¨π—§π—›π—˜π—‘π—šπ—” π—ͺ𝗔 π—–π—›π—œπ—¦π—’π—‘π—œNdi chisoni chachikulu  tikudziwitsa akhristu onse komanso anthu onse kuti Mayi Stellia Deleza Shakier...
19/07/2026

π—¨π—§π—›π—˜π—‘π—šπ—” π—ͺ𝗔 π—–π—›π—œπ—¦π—’π—‘π—œ

Ndi chisoni chachikulu tikudziwitsa akhristu onse komanso anthu onse kuti Mayi Stellia Deleza Shakier atisiya pa 18 July 2026.

Mayi Shakier anali mayi, agogo, mlongo ndi bwenzi lokondedwa kwambiri. Iwo anali mayi awo a m’busa Aaron Shakier, yemwe ndi Mtsogoleri wamaulaliki komanso Mlembi wa abusa ku Malawi Union Conference.

Iwo anabadwa pa 10 July 1950 ndipo atisiya pa 18 July 2026 ndi zaka 76.
Mwambo woika m'manda uchitika mawa ku Nalingula

Tiyeni tiwaikize m'pempherero banja la a Shakier ndi mabanja ena onse omwe asiyidwa pa nthawi yovutayi. Tipempha Mulungu wa chitonthozo kuti awalimbikitse ndi kuwapatsa mtendere.

16/07/2026

I got over 10 reactions on one of my posts last week! Thanks everyone for your support! πŸŽ‰

π—¨π—§π—›π—˜π—‘π—šπ—” π—ͺπ—”π—–π—›π—œπ—¦π—’π—‘π—œ  Ndi chisoni chachikulu ndi mitima yosweka kwambiri, talandira uthenga wa imfa ya South East Malawi Co...
01/07/2026

π—¨π—§π—›π—˜π—‘π—šπ—” π—ͺπ—”π—–π—›π—œπ—¦π—’π—‘π—œ

Ndi chisoni chachikulu ndi mitima yosweka kwambiri, talandira uthenga wa imfa ya South East Malawi Conference *Master Guide Pastor Yolos Nkuziona* omwe atisiya dzuro chakumadzuloku.

Tili ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa imeneyi yomwe yadzidzimutsa utumiki wonse komanso banja lonse la mpingo. Abusa Nkuziona anagwira ntchito ya Mulungu mokhulupirika. Kudzipereka kwao, utsogoleri wao, ndi kukhulupirika kwao pa ntchito ya utumiki tidzawasowa kwambiri.

Abusa anapita kuntchito koma anangogwa kupita ku Blantyre Adventist Hospital komwe achipatala anati atisiya kale

PROGRAM YA MALIRO A PASTOR YOLOS NKUZIONA

Program ya maliro a Pastor Nkuziona ili motere:

10:00am kuchoka ku Siwa ku Chileka kupita ku nyumba ya chisoni ya Taprama ku green corner komwe kukachitikile mwambo wonse wamaliro kuyambira 11:30am mamawa asananyamuke kupita ku Zalewa.

Malirowa aikidwa mawa pa 03 July 2026 ku Zalewa.

Directions/Mayendedwe aku Zalewa ali motere:

Mukafika pa Zalewa mukatenga nseu opita ku Lilongwe mukafika pa mudzi wa Kandoje ndipafupi ndi school ya Kadasana primary. Tiyeni tonse tikhale nawo shepherdess Nkuziona ndi banja lonse munyengo yovutayi komaso tiwakumbukile mmapemphero.

Joshua 1:9 (NKJV)Have I not commanded you? Be strong and of good courage; do not be afraid, nor be dismayed, for the LOR...
28/06/2026

Joshua 1:9 (NKJV)
Have I not commanded you? Be strong and of good courage; do not be afraid, nor be dismayed, for the LORD your God is with you wherever you go.

Zabwino zonse Achinyamata amene mukulemba mayeso a Form 4. Mulungu akutsogolereni. Limbikani mtima ndipo osaopa!πŸ™πŸ™

30/05/2026
29/05/2026

Happy Sabbath, Brethren
Tonight let your heart be quiet. Whatever you couldn’t finish or that tried to break you this week lay it down. Sabbath rest is trust, not laziness. God isn’t disappointed in you. He’s still with you in the unfinished parts. You’re not forgotten, not alone, and your story isn’t over. The God who called light from darkness can bring peace to your mind now. So breathe, forgive yourself, and whisper β€œJesus, I trust You.” Praying you sleep without fear and wake up lighter. May His presence cover you tonight. Sabbath rest and peace to you all

set free
28/05/2026

set free

Matop fan a set free mwai ndi uwutu usatiphonye bravo SET FREE

Matop fan a set free mwai ndi uwutu usatiphonye bravo SET FREE
28/05/2026

Matop fan a set free mwai ndi uwutu usatiphonye bravo SET FREE

Address

Phalombe
Phalombe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Phalombe Zone Adventist Youth Ministries posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share