Choonadi ndi chiti?

Choonadi ndi chiti? YOHANE 1:23
Anati, Ndine mau a wopfuula m'cipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye

Akuti azimayi akamapita ku msonkhano azigula nsalu ndikusokersa uniform yovalira ku msonkhano mpingo uliwonse uniform ya...
21/08/2026

Akuti azimayi akamapita ku msonkhano azigula nsalu ndikusokersa uniform yovalira ku msonkhano mpingo uliwonse uniform yake yake hmmmm

Mau a Mulungu amati bwanji inu? Tawerengani

08/07/2026

KUTHA KWA DZIKO LAPANSI.........3

Moni okondedwa nonse kuli konse komwe muli, ndabweranso ine m'bale wanu kufuna kupitilira ndi phunziro lathu la kutha kwa dziko lapansi.

Mu gawo lapita lija ndinayamba kuyankha funso la "ZIZINDIKIRO ZA KUTHA KWA DZIKO" ndipo mu kufotokozera kwanga ndinati Mulungu anaika dziko lapansi kuti likhale ndi mibadwo itatu: M'badwo wa Nowa, M'badwo wa Loti komanso M'badwo wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Ndiye lero ndikufuna tione zidzindikiro za kutha kwa dzikozi mwa tsatanetsatane.

Dziko lapansi Mulungu amakwaniritsa mau ake kudzera mmaulosi osiyanasiyana ndipo ma ulosiwa ndi omwe amatisonyeza kuti tili mu yanji.

Mu Buku Lopatulika (Bible) muli ma ulosi okwana 52, mwa maulosiwa 51 anakwaniritsidwa ndipo tikusala ndi ulosi umodzi.

Monga momwe mukuonera apapa ndi maulosi ambiri kwabasi, sindingakwanitse kufotokoza onse koma ndilemba omwe ndingakwanitsewo ndipo myvomerezana ndi mau a Mulungu kuti nthawi ya dziko lapansi yatha.

1. ULOSI 1
____________
Mateyu 24:3-8 Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano? Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu. Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike. Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m'malo akuti akuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.
_____________

Pa chapter ichi Yesu Khristu amakamba za zizindikiro za mathedwe a dziko lapansi ndipo anatchulapo zinthu zogwirika bwino ziwiri;
A. Aneneri onama
B. Nkhondo komanso mbiri za nkhondo (Kuukirana kwa anthu kwa anthu)

Tikaona dziko lapansi pano zinthu zonsezi zikuchitika.
Masiku ano a makono anthu ambiri adzuka ndi kumawauza anthu kuti akulalikira uthenga qa cipulumutso ndipo ambiri mwa iwo ali ndi zodzizwa zomwe akuonetsa kwa anthu mu dzina la Yesu Khristu koma zili zabodza.
Ndi amithenga a satana mdierekezi ndithu akungofuna kusokeretsa anthu mwa mseri!

Tikaonanso nkhaninya nkhondo tipeza kuti pano dziko lapansi lasokonekera ndi nkhondo zosiyanasiyana ndipo mitima ya anthu yasukunuka ndi izi zomwe zikusonyeza kuti tili mapeto a nthawi ya pansi pano.

Tikumva nkhani za Nkhondo ya ○Ukraine VS Russia
○Israel VS Palestine
○Israel America VS Iran
Ndi nkhondo komanso ziwawa malo osiyanasiyana monga ku DRC, Nigeria, Sudan ndi ena ambiri....

Taonani mau omwe Yesu anayankhula apa:
___________
Luka 21:20,22 Koma pamene pali ponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti cipululutso cace cayandikira. Cifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zicitike.
____________

Izi ndi zomwe Ambuye wathu Yesu Khristu anayankhula ali pa dziko pano zomwe zikusomikiziranso kuti nkhondo izi sikuti zikungochitika mwa chibwanabwana ayi.
Ndi zizindikiro za nthawi ya pansi pano: KHALANI MASO!

2. ULOSI 2
_____________
Ezekieli 7:12 Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve cisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wense.
____________

Palinso ulosi wina uwu omwe tikuona masiku ano.
Monga vesi iyi ikufotokozera tikaona dziko lapansi lero zinthu zafika povuta.
Katundu wakwera mtengo mosasimbika, katundu ochepachepa ndalama yomwe ikufunikayo yambirimbiri yoti munthu simaganizira....

Olo zitachitika kuti agogo akufuna kugula chimanga ndiye akumuuza ogulitsa kuti ali ndi ndalama yokwana basin limodzi la chimanga ndi hafu, ndiye mwina achotsereko mtengo kuti akwane ma basin awiri ndi cholinga choti akwanitse kusamala zidzukulu zao kunyumba. Ogulitsa akana ndipo ena atha kuyankhula mwa chipongwe chifukwa aziti aduka pa bizinesi yawoyo.
Zomwe ndi zofanana ndi lemba ilo kuti ogula sakukondwera ndipo agulitsa lero alibe chisoni chilichonse.

Tikakamba za sopo, mchere, mafuta, tomato ndi zina zafika posausa kwambiri.

Makolo amatiuza kuti kale akapita ku shop kogula kanthu amayamba awapasa kaye sugar abwire kenako azigula zomwe akufunazo kumapeto kwake amaperekanso ka mphoto koma pano zinatha zina linaipa

3. ULOSI 3
____________
Ezekieli 7:12,25 Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve cisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wense. Cionongeko cirinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe.
______________

Ndabweranso ndi ulosi wina uwu omwe ukukamba za mtendere wa dziko lapansi.
Nkhani iyi kuti imveke bwino tibwere kwathu komwekuno ku Malawi.

Kale kale kunali azungu omwe anthu akawatchula Asamunda ndipo a Malawi anadandaula chifukwa cha ukapolo ndi mavuti ena.
Pakupita kwa nthawi kunabwera Dr. Hastings Kamuzu Banda.
A Malawi anaombera mmanja kuti azilamulilidwa ndi wakuda mnzao.
Ndipo anadziwika ndi zina loti "mkango", Komatu sizinatenge nthawi anthu anapeza zofooka mwa mtsogoleri wao uja ndipo anafuna kuti achoke.

Kudzera mu njira zosiyanasiyana zomwe anthu ena anapanga zinathekadi anachoka ndipo analowa mmalo mwao Dr. Bakili Muluzi.
Mtsogoleri yu atalowa anthu ankakondwerera ndi zina zomwe anabweresa.
Munthu yemwe anadziwika ndi loti "Kuchikweza". Koma munthu sakoma zonse anapezazo zolakwika monga kulonjeza anthu za Feteleza wa ulere ndi nsapato za ulere zomwe zinachititsa kuti asapitilire kulamulira.

Kuchoka pamenepo panabwera Dr. Bingu M***arika.
Mtsogoleri anakondedwa ndi anthu uyu mpaka kumutchula dzina loti "Mose walero".
Chakudya ndi zina zambiri zinalipo koma anthu anadandaula za mafuta a galimoto komanso kusowa kwa ndalama.
Mwa tsoka anatisiya asanamalidze.

Kuchoka apo kunabwera Prof. Peter M***arika.
Uyunso anthu anati ali bwino ngati Bingu ndipo anadziwika ndi dziba la "Adad".
Koma ena ananyoza nkumati wakula, tikufuna mnyamata ife ndipo pa chisankho anasankhadi mnyamata yemwe amamfunayo.
Koma mnyamata akulamulira anthu anatinso ayi bola adadi omwe aja uyuyu ayi.....

Chisankho china chinabwera anthu abwereranso kwa Peter M***arika ndipo pano tsopano ndi "Nkulukuta moyo".
Pano anthu anenanso kale zambiri zomwe zikusonyeza kuti salinso bwino ayi

M***a kuona kuti zonsezi cholinga cha anthu akufuna munthu yemwe angabweretse mtendere mu dziko lino koma sakupezeka.

Kodi inu mukuti mtendere angabweretse ndi ndani?
Ndikuuzani okondedwa palibenso wina angakwanitse kubweretsa mtendere kupatula Ambuye wathu Yesu Khristu.
Inu ndi ine tikufunika tikhale okonzeka mitima yathu kuti tizalandire mtendere umenewo

Tiyeni tikumane mu gawo lotsatira pamene ndikupitilira ndi ma ulosi ena.......

08/07/2026

KUTHA KWA DZIKO LAPANSI.......2

Ndabweranso mu gawo lina lake phunziro lathu lomwe tinaliyamba.
Mu gawo loyamba ndinayankha funso loti "KODI DZIKO LIZATHA KAPENA AYI?"
Ndipo ndipereka mavesi angapo omwe amasimikizira zoti dziko ili lidzathadi

Mu gawo lino tiona komanso kuyankha funso loti "KODI ZIZINDIKIRO ZA KUTHA KWA DZIKO NDI CHIYANI (NDI ZITI)?"

Okondedwa mwa Ambuye wathu Yesu Khristu Mpulumutsi wa miyoyo yathu mulole kuti ine m'bale wanu ndifotokoze za funso limeneli.

ZOZINDIKIRO ZA KUTHA KWA DZIKO LAPANSI
______________
Luka 12:54-56 Koma iye ananenanso kwa makamu a anthu, Pamene pali ponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero. Ndipo pamene mphepo ya kumwela iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi. Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yace ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo yino?
_____________
Vesi ya ku Luka yomwe ili pamwambapa mutu wa nkhani analemba kuti Zizindikiro za nyengo yake, pomwe Yesu amauza anthu za mathedwe a dziko lapansi ndipo anafotokoza nkumawauza anthu kuti anthu amatha kulosera za mvula, ng'amba komanso mphepo ndikulondoladi koma chimodzi chomwe anthu amalephera ndi kudziwa kuti nyengo yomwe tili ino ndi iti
Ndipo anapereka chigamulo kuti anthuwa ndi onyenga, closing wao uli chabe.

Kuti muone dziko lapansi mmene likuyendera ndi mmenenso anthu akuchitira zinthu zao mupeza kuti ambiri sakudzindikira kuti nthawi ya dziko lapansi yapita ndipo ambiri akuganiza kuti apa ndi pamene dziko lapansi lafika pokoma kwambiri kuposa kale.
Ndipo makhalidwe a anthu asokonekera chifukwa chotengeka ndi zochita za pansi pano.

Komatu dziwani kuti zinthu sizili monga anthu akuganizira ayi.
(Ndikhala ndikufotokoza zambiri za izi popitilira ndi ohunziroli)

Mwachidule vesi ya pa Luka 12:54-56 imangofuna kutizindikiritsa kuti dziko lapansi silingathe modzidzimuka popanda zizindikiro ayi, zonse zikuyenera kuyenda mu ndondomeko yake.

Tatiyeninso tione chapter ichi.
______________
Luka 17:26-30 Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu. Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'cingalawa, ndipo cinadza cigumula, niciwaononga onsewo. Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; koma tsiku limene Loti anaturuka m'Sodoma udabvumba mota ndi sulfure zocokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo; momwemo kudzakhala tsiku lakubvumbuluka Mwana wa munthu.
______________
Dziko lapansi Mulungu atalilenga analipasa nthawi yake yoti likhale:
Yehova Mulungu analenga zonse masiku 6 ndipo anapumula tsiku la 7, ndiye chomwe Yehova anachita anatenga masiku 6 amenewo ndi kukhala zaka 7000, pa zaka zimenezi, 6000 ndi zoti anthu akhale pa dziko lapansi pomwe 1000 zosalazo ndi za anthu oyera mtima kuti azapumule kuyembekezera Yerusalemu wa tsopano (Paradizo).

(Ndikamalidza ka ndime aka ndiika vesi yomwe ikuonetsa masamu omwe ndikunena kuti 7 days = 7000 years)

Ndiye zaka 6000 zokhala oa dziko lapansizo Mulungu anazigawa kwa mibadw9 itatu monga mwa vesi ya pa Luka 17:26-30.

• Zaka 2000 zoyambilira ndi za m'badwo wa Nowa (Luka 17:26-27)
• Zaka 2000 zotsatira ndi za m'badwo wa Loti (Luka 17:28-29)
• Zaka 2000 zomalidza ndi za m'badwo wa Yesu Khristu omwe tili mu tsiku la lero (Luka 17:30)

Kusonyeza kuti ife tili mu m'badwo omalidza wa dziko lapansi kuti zaka 6000 zikwane
Mmene ndanena chonchi ambiri abalalalika kuti anthu akuona kuti zalowa bodza chifukwa pano ndi chaka cha 2026 kusonyeza kuti zaka 2000 zapitilira....
Ayi si choncho kuchokera pamene Yesu anabwera pa dziko lapansi kufika lero zaka 2000 sizinakwane, pano tili chaka cha 1786 (nkhani ya zakayi tizaphunzira tsiku lina).

Tsopano onani vesi yomwe imakamba zoti Mulungu anaika tsiku limodzi kukhala zaka 1000
____________
2 Petro 3:8 Koma ici cimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka cikwi, ndi zaka cikwi ngati tsiku limodzi.
______________
M***a kuona kuti ndi momwemo ndithu Mulungu ndi wanzeru zoposa.

Phunziro ili ndi lalitali kwambiri gawo ili ndikuima pomwepa kaye
Tiyeni mu gawo lotsatira momwe tione tsatanetsatane wa zizindikiro za kutha kwa nthawi zomwe ndafotokoza mmwambamo

Tikhalire limodzi okondedwa 🙏 🙏 🙏

08/07/2026

KUTHA KWA DZIKO LAPANSI.

Nkhani ya kutha kwa dziko lapansi ndi nkhani imene imamveka mosiyanasiyana pakati pa anthu a dziko lapansi, achipembezo (Ayuda, Akhristu komanso Asilamu) ndi ena ambiri.

Koma funso nkumati "KODI DZIKO LAPANSI LIDZATHA KAPENA AYI?"
Funso limeneli limakhala ndi mayankho osiyanasiyana motengeranso ndi mmene aliyense amamvera mau a Mulungu.

Kodi inu mumadziwa zotani za nkhani ya kutha kwa dziko lapansi?

Tiyeni tikhale limodzi tione mmene mau a Mulungu amafotokozera za nkhani imeneyi.

Pa mafunso angapo omwe tiunikire mu nkhani yathu okhuza kutha kwa dziko lapansi ndi choyamba ndiyambe funso loti KODI DZIKO LAPANSI LIDZATHA KAPENA AYI.
Tiyeni tione mavesi awa:
____________
Yesaya 51:6 Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko; pakuti kumwamba kudzacoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati copfunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa cimodzimodzi; koma cipulumutso canga cidzakhala ku nthawi lonse, ndi cilungamo canga sicidzacotsedwa.
_____________
Ezekieli 7:1-4 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti, Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israyeli, Kwatha; kwafika kutha kwace pa ngondya zinai za dziko. Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zanse. Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzacita cifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
_____________
Mateyu 24:29-31 Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwace, ndi nyenyezi zidzagwa kucokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka: ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo cizindikiro ca Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pacifuwa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru. Ndipo Iye adzatumiza angelo ace ndi kulira kwakukuru kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ace ku mphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ace ena.
_____________
1 Atesalonika 5:1-3 Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani, Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku, Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo cionongeko cobukapo cidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
_____________

Malinga ndi ma vesi awa buku lopatulika likutisimikizira kuti dziko lapansi tsiku lina lidzatha ndithu mosachita kukokeranso mavesi ayi akuchita kumveka bwino.
Iye amene ali ndi mzimu wa Mulungu wamvetsa chinthuchi
Apa tathana ndi funso loyamba.

Tiyeni tikumanenso mu gawo lachiwiri kuti tione nkhaniyi mwa tsatanetsatane.

CONTINUED........

11/06/2026

Kodi choonadi cha lemba la Genesis 6 ndi chani?

Inu kumeneko mumadziwa zotani?

Pali nkhani yomwe inalembedwa mu Buku Lopatulika (Bible) yomwe anthu ambiri samaimvetsa.Nkhani imeneyi ndi yomwe ikuonek...
27/05/2026

Pali nkhani yomwe inalembedwa mu Buku Lopatulika (Bible) yomwe anthu ambiri samaimvetsa.

Nkhani imeneyi ndi yomwe ikuoneka pa chithunzi chomwe chikuonekachi.

Nkhani imeneyi yakhala ikusoneza anthu ambiri mitu ndipo anthu ambiri akhala akuphunzitsa mosemphana ndi momwe chapter-chi chilili.

Ndawerengapo mabuku a zipembezo zosiyanasiyana, ma buku enanso omwe anthu ena amene anaphunzira za mau a Mulungu (Theology) analemba (Bible commentary) koma ndinapeza kuti nkhaniyi anthu samaimvesa mpaka pano

Tsono lero ndafuna kuti ndifotokozere za chapter chimenechi.

Chapter analemba chonchi:

Genesis 6:1-8
Ndipo panali pamene anthu anayamba kucuruka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo, kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, cifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ace adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.
Pa dziko lapansi panali anthu akurukuru masiku omwewo ndiponso pambuyo pace, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.
Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukuru pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.
Ndipo Yehova anamva cisoni cifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anabvutika m'mtima mwace.
Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva cisoni cifukwa ndapanga izo.
Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.

Nkhaniyo ndi imeneyi, kwinako ikupitilira koma ife tikufuna tione bwino pamenepa

Kwambiri anthu pomwe pamawasokoneza anthu ndi apa

Genesis 6:
1 Ndipo panali pamene anthu anayamba kucuruka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo,
2 kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
3 Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, cifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ace adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.
4 Pa dziko lapansi panali anthu akurukuru masiku omwewo ndiponso pambuyo pace, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.

Motengera ndi zimene ndinapeza nditawerenga mabuku angapo, anthu amaphunzitsana kuti anthu omwe akunenedwa kuti ndi ana a Mulunguwo anali angelo amene anagwetsedwa kuchokera kumwamba atalakwa pamaso pa Mulungu pomwe ana a anthu ndi omwe anali olengedwa (kapena kuti ana a Abraham).

Ndiye amanena kuti akuti angelo amenewo atagwetsedwa kuchoka kumwamba anabwera pa dziko lapansi ndi kuvala matupi a anthu ndikuwatira akazi a dziko lapansi kenako nkuzabereka ana omwe anali a mphamvu kwambiri kuposa munthu wamba.

Umu ndi momwe anthu amaphunzilira.
Koma kodi chilungamo cha nkhaniyi ndi chiti?

Malinga ndi dzina la page ino. Ndinaika dzina loti "Choknadi ndi Chiti?" Chifukwa cholinga chake ndi kibweretsa chilungamo pa mau a Mulungu omwe ena samawamvesa kapena anawapotoza kwa anthu.

Tiyeni tione chindunji cha chapter chimenechi kuti chikutanthauza Chiyani....

Aroma 9:6-16
Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala cabe ai. Pakuti onse akucokera kwa a Israyeli siali Israyeli; kapena cifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isake, mbeu yako idzaitanidwa.
Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yace. Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana Ndipo si cotero cokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isake; pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo, cotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau. Ndipo tsono tidzatani? Kodi ciripo cosalungama ndi Mulungu? Msatero ai. Pakuti anati ndi Mose, Ndidzacitira cifundo amene ndimcitira cifundo, ndipo ndidzakhala ndi cisoni kwa iye amene ndikhala naye cisoni. Cotero sicifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene acitira cifundo.

Mukaona verse imeneyi ya ku Aroma yomwe Paulo mtumwi wa Khristu analemba, mutu wa nkhani analemba kuti "ULAMULIRO WA MULUNGU WA KUSANKHA ENA"

Mwachidule verse imeneyo Paulo amafuna afotokoze kuti pali anthu ena Mulungu anawasankha kuti akhale ana ake ndipo ena sanawasankhe. Kusonyeza kuti pa dziko lapansi si onse amene ali ana ake ayi monga mwa kusankha kwa Mulungu.

Enatu mmene amva zimenezi abalalika, ndipo akufunsa kuti mesa tonse anatilenga ndi Mulungu yemweyo ndiye zitheka bwanji kuti ena sakhale ana ake?????

Indeee ndi zotheka, Mulungu amapanga chomwe chamkonda ndipo samalakwitsa.

Paulo akupereka chitsanzo kuti Mulungu anamkonda Yakobo koma anamuda Esau.
Apa wina sangabwere kumamuimba Mulungu mulandu ayi chifukwa Mulungu anapanga ganizo ndipo zinakhaladi momwemo

Izi zinakhalanso chimodzimodzi ndi pa nthawi ya mmbuyomu zisanafike pa Esau.

Genesis 4:1-24
(Kuopa kutalikitsa kwambiri nkhani sindilemba verse imeneyi, muwerenfe nokha mu bible komanso ndiika mu comment)

Apa tikuona nsembe ya Abele ikulandilidwa koma ya Kaini inakanidwa ndipo zitatero Kaini anamupha mphwake Abele.
Pamapeto pake Mulungu akumuchotsa Kaini pamaso pa abale makolo ake.

Kaini atachoka anakabereka ana ake kumeneko. Tiona pa verse 16 ndi pomwe akukamba za mbumba ya Kaini.

Mbumba iyi ndi yomwe ikutchedwa kuti "ANA A ANTHU"

Tsono tikaona pa Genesis 4 yemweyo alemba izi

Kubadwa kwa Seti

25 Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wace; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Seti: Cifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu yina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha,
26 Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwamwana wamwamuna: anamucha dzina lace Enosi: pomwepo anthu anayamba kuchula dzina la Yehova.

Mwana wa chitatu wa Adam atabadwa ndi pamene anthu pa dziko lapansi anayamba kutchula dzina la Yehova kusonyeza kuti mwa Seti Mulungu anaika mbewu yake.

Tsono pa chapter 5 ndi pomwe akulemba mbumba ya Seti.
Awa ndi omwe amatchedwa "ANA A MULUNGU"

Kusonyeza kuti lemba la pa Genesis 6 amakamba kuti ana a Seti ndi omwe amayang'ana pa ana a Kaini ndipo anakakwatira kumeneko nabala anthu a mphamvu osati angelo anakwatira akazi ayi

DZIWANI ICHI:
Nzosatheka kuti angelo akwatire mkazi mwa njira iliyonse ayi chifukwa mau oti mngelo okhawo apamakhala kuti cha umunthu mwa iwo mulibe.
Kukwatira pamafunika pakhale zilakolako ndiye mngelo sakhala ndi zilakolako ayi or atakhala ochimwa

Chinaso ndi chomwe analemba Yuda

Yuda 1:6 Angelonso amene sanasunga cikhalidwe cao coyamba, komatu anasiya pokhala pao pao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira ciweruziro ca tsiku lalikuru.

Angelo amene anachoka kumwamba Mulungu anawatsekera mu ndende ndiye sindikudziwa kuti angelo amene anthu amanena kuti anakwatirawo anachoka kuti????

Ngati pali funso, muli ololedwa kutero ndilipo ine.

M***a kuwatumiziranso anzanu kuti nawo apindule

Ambuye akudalitseni.... 🙏 🙏 🙏

Cholinga cha samba lino ndinkuzukuta mitu yosiyanasiyana kuchokera mu Buku Lopatulika (Bible)Ndipo tizibwera ndi mayankh...
18/05/2026

Cholinga cha samba lino ndinkuzukuta mitu yosiyanasiyana kuchokera mu Buku Lopatulika (Bible)
Ndipo tizibwera ndi mayankho pa mafunso omwe anthu amakhala akusausika nao komanso ena omwe inu otsatira athu mutifunsa.
Pazikhalanso ma ulaliki osiyanasiyana.

TSATIRANI TSAMBA LINO MWACHIDWI KUTI ZISAKUPHONYENI

Mau ooneka ngati ophiphiritsa koma omveka bwino ndithu
18/05/2026

Mau ooneka ngati ophiphiritsa koma omveka bwino ndithu

Address

Mianga
Phalombe
146

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Choonadi ndi chiti? posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share