19/08/2026
📌ZAKA 8 ZAKUVUTIKA ZATHA KUMSONKHANO WA CHITSITSIMUTSO KU NTCHEU📌
Kwa zaka zisanu ndi zitatu 8, abambo awa anakhala ndi vuto la paphewa lomwe limawalepheretsa kukweza manja awo mmwamba.
M'chaka cha 2018, bambowa adamenyedwa paphewa lawo ndi musi, zomwe zidapangitsa kusemphana kwa mafupa a phewa lawo. Kuyambira nthawi imeneyo, ankavutika kukweza manja awo komanso ankavutika ngakhale kuvala malaya. Adapita kuchipatala kangapo konse, ndichikhulupiliro chakuti phewa lawo likhalanso bwino. Koma madotolo atawayesa kangapo, iwo adauzidwa kuti palibenso chimene angachite.
Ali mkati mwa vuto limeneli chinthu chinanso chachilendo chidayamba kuwachitikira. Bambowa adayamba kumakomoka usiku uliwonse nthawi ya 12 koloko. Akadzidzimuka amkayamba kukuwa. Sabata imene mnsonkhano wa chitsitsimutso umayenera kuchitika, vutoli lidakula moposera muyeso kufikira pakuti akakomoka aziluma lilime mpaka kutuluka magazi.
Akazi awo adafotokoza kuti iwo ndi mkazi wachisanu ndi chimodzi (6) amene anakwatirana ndi bambowa. Akazi asanu omwe adali atakwatirana nawo kale adawasiya ukwati chifukwa cha mavuto omwe ankakumana nawo chifukwa cha matenda abambowa. Koma pamene mkaziyu adakwatiwa naye miyezi isanu yapitayo, adasankha kukhala nawo komanso kuwathandiza. Mkaziyu adawauza amunawo kuti iye akhala mkazi womaliza chifukwa sadzawasiya ukwati monga ena adachitira kale.
Kwa miyezi isanu, mayiwa adati sadasangalale ndi moyo wa m’banja chifukwa cha zomwe mwamuna wake ankakumana nazo. Komabe, adapitiriza kumupempherera ndipo sadamusiye.
Pamene munthu wa Mulungu Apostle Joseph Ziba amapemphera ndi kulengeza machiritso kwa anthu, mphamvu ya Mulungu zidawakhudza bambowa. Ndipo adayamba kukweza phewa ndi manja awo bwinobwino mopanda vuto lili lonse komanso popanda ululu omwe udawazunza kwa zaka zisanu ndi zitatu zapitazi.
Ambuye alemekezeka chifukwa cha umboni wa mphamvu ngati umenewu.