08/08/2026
CHIKONDI CHENICHENI | DIVINE SERVICE
08 AUGUST 2026 🌸 DORCAS SEMINAR
Preacher: Shepherdess Manase
🎶 Christ in Song: No. 17 & 133
🎵 Singing Group: DORCAS
“Mtima wofatsa, wachikondi ndi wokhululuka ndi mtima umene Mulungu amafuna mwa mwana wake.”
Pa Divine Service ya pa 08 August 2026, mpingo unakhala ndi Dorcas Seminar yomwe inatsogoleredwa ndi Shepherdess Manase. Uthenga wa tsikuli unakhazikika pa mutu wakuti “Chikondi Chenicheni,” ndipo tinaphunzira kuchokera mu nkhani ya Davide, Sauli ndi Yonatani.
Mu 1 Samueli 17, tinaona mmene Davide anagonjetsera Goliati chifukwa chokhulupirira Mulungu. Sauli atamupatsa zovala za nkhondo, Davide anakana chifukwa sanazolowere kuvala zovala zimenezo. Ngakhale kuti anali atapeza chipambano chachikulu, Davide sanadzikuze, koma anakhalabe wodzichepetsa. Izi zikutiphunzitsa kuti chipambano, udindo kapena kutamandidwa ndi anthu zisatichotse pa kudzichepetsa.
Yonatani ndi Davide anatisonyeza chitsanzo cha chikondi chenicheni ndi ubwenzi wokhulupirika. Yonatani sanayang’ane komwe Davide anachokera, udindo wake kapena zomwe anali nazo. Anamukonda m***a mtima ndipo anali wokonzeka kumuchitira zabwino. Chikondi chenicheni sichiyang’ana phindu limene tingapeze kwa munthu, koma chimafuna kuona zabwino mwa munthu wina ndi kumuthandiza pamene tingathe.
Ngakhale kuti Sauli ankafuna kupha Davide, Davide sanakondwere ndi imfa ya Sauli. M’malo mwake, analira maliro ake. Izi zikutiphunzitsa kuti tisamakondwere munthu amene watichitira zoipa akakumana ndi mavuto. Mkhristu ayenera kukhala ndi mtima wachifundo ndi wokhululuka, osati wa chidani ndi kubwezera. Tiyenera kupempherera anthu amene amatichitira zoipa, chifukwa Mulungu amafuna kuti anthu alape ndi kusintha moyo wawo.
Yonatani atamwalira, Davide sanaiwale ubwenzi wawo. Anakumbukira zabwino zimene Yonatani anamuchitira ndipo anafunsa ngati panali munthu aliyense wa m’banja la Yonatani amene akanamuchitira chifundo. Izi zikutisonyeza kuti chikondi chenicheni sichiyiwala zabwino zimene ena anatichitira.
Uthenga wa lero watikumbutsa kuti chikondi chenicheni chiyenera kuonekera mu mawu athu, zochita zathu, ubwenzi wathu komanso mmene timachitira ndi anthu ena. Tisamangonena kuti timakonda Mulungu, koma chikondi chimenecho chionekere mwa kukhululukira, kuthandiza, kulemekeza, kupempherera komanso kuchitira ena zabwino.
Mulungu akuchotseni mtima wa nsanje, chidani ndi kubwezera womwe unali mwa Sauli, ndipo akupatseni mtima wa chikondi, chifundo, kudzichepetsa ndi kukhulupirika womwe unaonekera mwa Davide ndi Yonatani.
Tiyeni tizikondana m***a mtima, kukhululukirana komanso kuchitirana zabwino, chifukwa chikondi chenicheni chimayambira mumtima ndipo chimaonekera mu zochita.
🙏 Mulungu atithandize kukhala anthu a chikondi chenicheni.
✍️ Wolemba: Gift M***a
📸 Wojambula: Kalabo Mchenga