13/06/2026
Mwambo wokumbukira moyo wa yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Saulos Klaus Chilima, ukuchitika lero kumudzi kwawo ku Nsipe m'boma la Ntcheu. Mwambowu wayamba ndi nsembe ya Ukaristia yomwe akutsogolera ndi episkopi wa dayosizi ya Zomba, Ambuye Alfred Mateyu Chaima. Ulaliki unachokera m'mabuku a Yesaya 25:6 mpaka 9 komanso kalata ya Paulo woyera kwa Aroma 8:31 mpaka 39.
Nduna ya zamaphunziro Bright Msaka ndiwo ali mlendo olemekezeka. Akulu akulu ena omwe afika pa mwambowu ndi Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko Lino Dr Jane Ansah, Mtsogoleri wa chipani cha UTM Dalitso Kabambe, yemwe anali Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko Lino Michael Usi, Mtsogoleri wakale wa dziko Lino Mayi Joyce Banda, nduna zosiyana siyana mwa ena.
Panthawi ya zoyankhulayankhula, Mkazi wa malemu Saulos Chilima mayi Mary Chilima wati kwa zaka ziwiri zomwe zadutsa kuchokera pomwe a Chilima anatisiya moyo wawo wakhala wopweteka. Iwo ati amawakumbukira amuna awo ngati mwamuna wodziwa kukonda ndikusamala banja lake komanso wokonda kutumikira Mulungu.
A Clement Chilima, oyimilira akubanja, ati wachiwiri kwa mtsogoleri wakale wa dziko lino, a Saulos Klaus Chilima anali mphatso yapaderadera kwa akubanja kufikira nthawi ya imfa yawo.
Iwo apempha aMalawi kuti apitilire kupemphelera banja la aChilima, ndipo ati mitima ya akubanja imakhala pansi akaona chikondi chomwe anthu mdziko lino amawaonetsera.
Pa mwambo uno, panalinso kuwonetsa chiliza cha malemuwa chomwe chamangidwa mwa makono.
Dr. Saulos Chilima omwe anabadwa pa 12 February 1973, anamwalira pa 10 June 2024 pa ngozi ya ndege yomwe inachitika mu nkhalango ya chikangawa yomwe inatenganso miyoyo ya anthu ena asanu ndi atatu omwe anali nawo mu ndegeyo pomwe amkapita ku maliro a woyimira anthu pa milandu, Ralph Kasambara m'boma la Nkhatabay.
Pamene mapemphero okumbukira komanso kukondwelera moyo wa yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima uli mkati ku Msipe, nako ku Ntcheu Stadium zokonzekera zili mkati kukonzekera mwambo wa masana wokumbukira a Chilima.
Uwu ndi mwambo womwe akonza ndi achipani cha UTM, chipani chomwe malemu Saulos Klaus Chilima anali mtsogoleri wake. Zina mwa zomwe zikhale zikuchitika ku mwambo waku stadium ndi monga kuyatsa makandulo komanso kukhale oyimba.
Zithuzi zili munsimu ndimwazina mmene mwambo unalili
# Corpus Christi Ntcheu Parish #