12/07/2020
2
7) Pasapezeke mtsogoleri aliyense woyika ndemanga pankhani za matendawa munjira
yowapeputsa ndikupangitsa anthu kuti asakhale siliyasi. Kulibwino kuti tilankhule pa
service munjira yothandiza ma membala athu kuti azidziteteza.
8) Kukanakhala bwino anthu onse alimbikitsidwe kuti azipereka chopereka kupyolera pa
mpamba, airtel money mo626 kapena banki ya pa Internet. Koma ngati izi sizingatheke
onse omwe amawerenga ndalama pa church azisamba mmanja ndi sopo akatha ndipo
asawerenge ndalama monyambitira malovu.
9) Osakakamira kusanjika manja popempherera anthu. Mphamvu ya Mulungu imayenda
ngakhale kungokweza mkono koma osamukhudza amene mukummpemphererayo.
10) Ma meeting onse a number ya anthu amene sali ambiri pa church achitike mu chipinda
choti chilli ndi Mawindo abwino ndipo makomo akhale otsekula.
11) Ngait pali matenda omwe ali wokaikiridwa kapena wodziwika kuti ndi akovidi, tiyeni
titsatire ndondomeko zoikika ndi boma motsatira ndondomeko ya a za umoyo. Tipange
ndondomeko zonse ndikupereka uthenga kapena pemphero mwa umunthu ndi
Chikondi komaso modzisamala ngati tapatsidwa mpata.
12) Ngati pali maliro omwe ali wokaikiridwa kapena wodziwika kuti ndi wakovidi, tiyeni
titsatire ndondomeko zoikika ndi boma motsatira ndondomeko ya a za umoyo. Tipange
ndondomeko zonse ndikupereka uthenga kapena pemphero mwa umunthu ndi
Chikondi komaso modzisamala ngati tapatsidwa mpata. Malangizo alipo ambiri koma
tisiyire p***a.
Pamene ndikulemba kalatayi ndikudziwa mwachisoni kuti pakati pathu pali atsogoleri ndi
mamembala ena omwe sakhulupirirabe kuti vailasi ya Covid-19 ilipo ndiponso ndikudziwaso
kuti ena amati inatha nthawi yomwe iwo anamaliza kusala kudya ndi kupemphera pamene
timasala masiku 21. Choona chake ndi choti ambirife tinasala masiku 40 ndipo ambirife
tikanapitiriza kutenga masiku apo ndi apo koma mapempherowa sakutanthauza kuti tilekerere
ai.
Ine ndikudziwanso kuti atsogoleri ambiri akunena kuti ma service ambiri akutopetsa