23/08/2026
MATEYU 6:25-34
MOYO UPOSA ZONSE
Mchithunzimu muli abambo amene akutsatira zochitika za pa msonkhano, ndipo mkono wakumanzere awukwezawo kuli phone imene alugwiritsa ntchito kujambula zochitika zona za pa msonkhanowu. Zinangondipatsa chidwi kuona mtundu wa phone yomwe akugwiritsa ntchito kujambula, ndipo mukaizumula muona kuti idamangidwaso ndi rubber band.
PHUNZIRO
Mulungu sangatiike tonse pa level imodzi mmoyo uno pa zifukwa zomwe mwini Wakeyo alinazo. Kodi mmudzi nonse mukhale osawuka athandize mzake ndani? Pa banja nonse osowa zikagwa zofuna ndalama athandize mzake ndani? Ngakhale pa mpingo Mulungu adaika ma level osiyana akapezedwe why? Ena mumpingomo ndi ma kingdom financiers monga azimai ena adathandizira utumiki wa Yesu ndi ndalama zawo mu bible aja. Sitikuyenera kudandaula, kumuimba milandu Mulungu pofanizira nyengo zathu ndi za anthu ena, ifeyo ndi ifeyo ndipo awowo ndi awowo. Mulungu amatikonda momwe tiliri, osachotsera osawonjezera; ndipo kukhutira ndizomwe tilinazo komaso pomwe tili zimapatsa mtendere popeza zimamulemekeza Mulungu. Kuchitira nsanje iwo amene kapezedwe kawo nkoposa ife sithandizo, kukwezedwa sikubwera, kapena level ya moyo wa munthu siimasintha chifukwa chakuti waakokera ena pansi. Kudandaula sikuonjezeraso masiku athu Okhala ndi moyo, likwanire tsiku ndizofuna zake pakuti moyo uposa zonsezo.
Ambuye akudalitseni