02/08/2026
'CHIKONDI CHA KHRISTU CHIONEKERE NGAKHALE KU NTCHITO'
Akhristu a mpingo wa Mangochi CCAP awalimbikitsa kuti adzionetserana chikondi pakati pawo kuyambira ku mpingo mpaka kulikonse monga malo a ntchito, bizinesi ndi ena pofuna kulimbikitsa umodzi.
M'busa wa mpingowu a Chikondi Banda ndiomwe apereka chilimbikitsochi Lamulungu pamene mamembala a Mangochi CCAP omwenso ndiogwira ntchito ku nthambi ya Immigration anatsogolera chipembezo cha Chichewa.
"Zimakhala zomvetsa chisoni kuti anthu opemphera komanso kugwira ntchito limodzi asamagwirizane chifukwa choti izi sizimapereka chithunzithunzi chabwino cha Khristu Yesu," atero a busa a Banda.
Mu uthenga wake omwe unachokera m'mabuku a Genesis 11 verse 6 komanso 1 Akorinto 13 verse 4 mpaka 7, a Blessings Kam'nyamata a mlaga wa Mtalimanja A, agwirizana ndi abusa a Banda ponena kuti 'Ulemerero Wa Mulungu Ndi Umodzi Ndi Chikondi'.
Mamembala a mpingo wa Mangochi CCAP omwe ndi ogwira ntchito ku immigration alipo oposa 40 pomwe mamembala okwana 20 ndiomwe anatenga nawo mbali potsogolera chipembedzochi.
Malingana ndi abusa a Banda, mamembala onse a mpingowu kuchokera m'madera awo osiyanasiyana ogwirako ntchito ali ndi mwayi otsogolera chipembezo ngati atafuna kutero.
MangochiCCAPMediaTeam