Sunnah Path Syllabus

Sunnah Path Syllabus Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Sunnah Path Syllabus, Religious organisation, Mangochi.

Pewani kudya za Haraam
13/06/2026

Pewani kudya za Haraam

Paja mawa loyang'ana mwezi wanyawani eti" Eshiiii high 5
16/05/2026

Paja mawa loyang'ana mwezi wanyawani eti" Eshiiii high 5

01/05/2026

Anthu akusaka saka Deen yeni yeni koma sakuipeza, chiwongoko chili kutali.

Koma omwe ali pachiwongoko amankonda Allah koopya.
Q 2:265

Uyu ndi ndani?Anabwelera ku Chisilamu 1975
19/04/2026

Uyu ndi ndani?
Anabwelera ku Chisilamu 1975

25/03/2026

Bismi llah rrwahmaan rrwaheem. ✍️

CHINTHU CHACHI 10 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN"Kuisiya Deen, kusailabadira, osaiphunzira kapena kuchita za Deen, kungok...
21/03/2026

CHINTHU CHACHI 10 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN

"Kuisiya Deen, kusailabadira, osaiphunzira kapena kuchita za Deen, kungokhala msilamu ndi dzina lokha".

Allah anayakhula za point imeneyi pa Qur'an 33:22

وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِآيَاتِ رَبِّهِ ثُمَّ أَعْرَضَ عَنْهَا ۚ إِنَّا مِنَ الْمُجْرِمِينَ مُنتَقِمُونَ.
Kodi ndani yemwe ali wopondeleza kwambiri koposa yemwe ma Aya a mbuye wake atchulidwa kwa iye kuti atsatire iye mkukana? Ndithu, Ife, tidzawabwezera zoipa anthu okanira.

NDEMANGA
Muli anthu mmidzimu, Swalah anaisiyiratu, kumaliro sapita, kusala ayi amangokhala ngati mbuzi, chisilamu chawo cha dzina. Amenewo akadzamwalira ndikosaloledwa kupemphelera Jeneza yawo, chifukwa anamkana Allah ali moyo poisiilatu Swalah.

ZOFUNIKA MUDZIWE
Palibe kusiyana pa zinthu zomtulutsa munthu pa Deen kaya anachita mocheza, kaya anachita ndi chitsimikizo, kaya anachita akuopa kupatula ngati wina wachita kukakamizidwa kuchita zimene zingamtulutse Deen.Zonsezo ndizoopya ndiponse nde zomwe zili common anthu kuzichita mmidzimu. So mkofunika kuti msilamu apewe zimenezo ndi mphavu zake zonse.

Timupemphe Allah chitetezo kuchokera ku chilichonse chomwe chingadzutse mkwiyo wake ndi chilango chake chopweteketsetsa. Allah amupatse wabwino muzolengedwa zake Muhammad, akubanja lake ndi maswahaba ake, ndikuwapatsa mtendere. Ameen.

CHINTHU CHACHI 9 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN Yemwe atakhulupilire kuti anthu ena akuyenera kukhala ndi ufulu wosankha ...
15/03/2026

CHINTHU CHACHI 9 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN

Yemwe atakhulupilire kuti anthu ena akuyenera kukhala ndi ufulu wosankha kutsatira or osatsatira Shar'iah ya mtumiki Muhammad s a w, ngati mmene zinalolezedwera kwa Khidhir kukhala kunja kwa Shar'iah ya Musa a,s,w, "watuluka Deen.

Allah alimbikitse mapazi anu ndi anga ndikulimbikitsa mitima yathu pa Deen yake. Allahumma Ameen.

CHINTHU CHACHI 8 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN Kuwathandiza ma mushriqoona/anthu azipembezo zina posakhala chisilamu mma...
04/03/2026

CHINTHU CHACHI 8 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN

Kuwathandiza ma mushriqoona/anthu azipembezo zina posakhala chisilamu mmalo momuthandiza msilamu ndekuti watuluka Deen.

يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَّخِذُوا الْيَهُودَ وَالنَّصَارَىٰ أَوْلِيَاءَ ۘ بَعْضُهُمْ أَوْلِيَاءُ بَعْضٍ ۚ وَمَن يَتَوَلَّهُم مِّنكُمْ فَإِنَّهُ مِنْهُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ.
Oh inu amene mwakhulupirira! Musakhale pachinzake ndi ayuda ndi akhrisitu. Iwo amachezerana ndipo amatetezana okha okha. Amene angachezerane nawo mwa inu, ndiye kuti ndi m'modzi wa iwo. Ndithudi, Allah Satsogolera anthu ochita zoipa.

MSILAMU ALIPOMPO AKUFUNA THANDIZO INU MUKUKATHANDIZA ENA OSAKHALA ASILAMU.
ALLAH AKUTETEZENI INU NDI INE POSIYA KUWALABADIRA ASILAMU ANZATHU. AMEEN

CHINTHU CHACHI 7 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN* Ufiti, mmenemo muli kumulekanitsa munthu ndi chinthu chomwe amachikonda ...
03/03/2026

CHINTHU CHACHI 7 CHOMTULUTSITSA MUNTHU MU DEEN*

Ufiti, mmenemo muli kumulekanitsa munthu ndi chinthu chomwe amachikonda or kumloza munthu azichikonda chinthu monkakamiza kudzera mmasenga {khuzumure}. Amene angachite zimenezo kapena kutsangalatsidwa nazo ndekuti wachita kufri/watuluka Deen.

Ndipo izi zili ndi umboni pa kuyankhula kwa Allah pa Qur'an 2:102 koti;

وَمَا يُعَلِّمَانِ مِنْ أَحَدٍ حَتَّىٰ يَقُولَا إِنَّمَا نَحْنُ فِتْنَةٌ فَلَا تَكْفُرْ......
Koma sadaphunzitse aliyense pokha pokha atamuuza kuti: 'Ife ndife mayeso, choncho musachite Kufri/kumkana Allah/'zisakutulutseni Deen.

Azichimwene ndi azichemwali pa Deen! Allah mbuye wanu akutetezeni inu ndi ine ku ufiti ndi matsenga. Ameen.

01/03/2026

Follow Amashi Iliyas Dines's WhatsApp channel. ‎أصحاب رسول الله كانوا يتعلمون الهدى من علم.‎ Join 1K followers for the latest updates.

Address

Mangochi

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Sunnah Path Syllabus posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share