04/02/2026
*4 FEBRUARY, 2026*
_*LACHITATU LA MULUNGU WA 4 PACHAKA*_
*MAU OYAMBA, MAWU A MBUKU LACHIWIRI LA SAMUELI 24:2,9-17*
Mfumu Davide adauza Yowabu ndi atsogoleri ankhondo amene adali naye pamodzi kuti: “Pitani pakati pa mafuko onse a Israeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, mukawerenge anthu kuti ndidziwe chiwerengero chawo. Tsono Yowabu adapereka chiwerengero cha anthu onse kwa mfumu. Ku dziko la Israeli kudali anthu 800,000 otha kumenya nkhondo, ndipo ku Yuda kudali anthu 500,000 pamodzi. Pambuyo pake Davide adadzitsutsa mu mtima mwake atatha kaundulayo, ndipo adapemphera kwa Chauta kuti: “Ndachimwa kwambiri pochita zimenezi. Koma tsopano, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mundikhululukire tchimo langa, ine mtumiki wanu, popeza kuti ndachita zopusa kwambiri. Tsono Davide atadzuka mmawa, Chauta adamulankhula ndi Gadi, mneneri wa Davide, namuuza kuti: “Pita ukamuuze Davide kuti: ‘Ine Chauta ndikunena kuti: ndikuika pamaso pako zinthu zitatu zoti ndikuchitire. Tsono usankhepo chimodzi ndipo ndidzakuchitira.”
Choncho Gadi adabwera kwa Davide namuuza kuti: “Musankhe kuti kodi pabwere zaka zitatu za njala m’dziko mwanu, kapena inu mukhale mukuthawa adani anu pa miyezi itatu, kapena pakhale mliri wa masiku atatu mu dziko mwanu? Ganizani bwino, ndipo mutsimikize chiri chonse choti muyankhe kuti ine ndikauze amene adandituma ineyo.” Apo Davide adauza Gadiyo kuti: “Iyayi, ine pamenepa ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka tigwe m’manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu, koma chonde, tisagwe m’manja mwa anthu, ayi.” Choncho Chauta adagwetsa mliri pakati pa Aisraele kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene adafuna Mwini wake. Mwakuti kuchokera ku Dani mpaka ku Beereseba, adafa anthu okwanira 70,000 pamodzi. Ndipo pamene mnjelo adatambalitsa dzanja lake kuloza mzinda wa Yerusalemu kuti auwononge, Chauta adasintha maganizo a chilangowo nauza mnjelo, amene ankaononga anthu aja, kuti:
“Iyayi, basi tsopano. Kwakwanira. Bweza dzanja lakolo.” Nthawi imeneyo nkuti mnjelo wa Chautayo atayima pamalo wopunthira tirigu wa Arauna, Myebusi. Davide adaona mnjelo uja, ndipo adalankhula ndi Chauta adati: “Ndachimwa ndine, ndipo ndachita choipa. Koma nkhosa izi, kodi zachita chiyani? Amangonditsatira chabe. Tsono dzanja lanu likhale pa ine ndi banja la bambo wanga?”
*Mau a Ambuye*
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 32: 1-2, 5, 6, 7
*Inu Chauta, mundikhululukire kulakwa kwanga* (5c).
Ngodala amene zolakwa zake zakhululukidwa,
Amene machimo ake afafanizidwa.
Ngodala amene Chauta samuŵerengera mlandu wake,
Amene mu mtima mwake mulibe chinyengo.
*Inu Chauta, mundikhululukire kulakwa kwanga*.
Koma ine ndidavomera tchimo langa kwa Inu,
Sindidabise kuipa kwanga.
Ndidati: “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta.”
Pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.
*Inu Chauta, mundikhululukire kulakwa kwanga*.
Nchifukwa chake munthu aliyense wosamala za Inu
Apemphere kwa Inu.
Akadzafika mavuto, akadzafika madzi a chigumula,
Zonsezo sizidzamufika, ndipo Inu ndinu kobisalira kwanga.
Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto.
Potero ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.
*Inu Chauta, mundikhululukire kulakwa kwanga*.
*Aleluya*: (Yohane 10: 27) Nkhosa zanga zimamva mawu anga, akutero Ambuye: ndimazidziwa ndipo izo zimanditsatira Ine, *Aleluya*.
*MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO WOYERA 6:1-6*
Yesu adafika kumudzi kwawo. Ophunzira ake adatsagana naye. Litafika tsiku la Sabata, Iye adayamba kuphunzitsa m’nyumba ya mapemphero. Anthu ambiri, amene adalikumvetsera, adadabwa kwambiri, ndipo ankafunsana kuti: “Kodi Iyeyu zimenezi adazitenga kuti? Nzeru zimene adalandirazi nzotani? Akutha bwanji kuchita zinthu zamphamvu chotere? Kodi Iyeyu si mmisiri wa matabwa uja, mwana wa Mariya? Kodi si mbale wa Yakobe ndi Yose ndi Yuda ndi Simoni? Kodi alongo ake si alinafe konkuno? Motero adampeputsa. Koma Yesu adawauza kuti: “Mneneri amalemekezeka kwina kuli konse kupatula kumudzi kwawo, kwa abale ake kapenanso ku banja kwake.” Choncho kumeneko sadathe konse kuchita zinthu zamphamvu. Adangosanjika manja pa anthu pang’ono chabe odwala ndi kuwachiritsa, ndipo adadabwa kuti anthu a kumeneko sadamkhulupirire. Pamenepo Yesu adapita kumidzi yozungulira namangophunzitsa anthu.
*Mthenga wa Ambuye*