Mvunguti CCAP Nkhoma Synod

Mvunguti CCAP Nkhoma Synod The core point is to reach out to people's lives with the Gospel of God ��

MUSAMADERE KHAWA NDI KUVUTIKA KWANU CHIFUKWA AMAKWEZA MUNTHU NDI MULUNGU. Genesis 50 : 20 - 21Yohane 3 : 30 1. CHINTHU C...
25/08/2026

MUSAMADERE KHAWA NDI KUVUTIKA KWANU CHIFUKWA AMAKWEZA MUNTHU NDI MULUNGU.

Genesis 50 : 20 - 21
Yohane 3 : 30

1. CHINTHU CHIMENE CHIKUWONEKA NGATI TSOKA LERO,MULUNGU ADZACHISANDUTSA KUKHALA NJIRA YA MADALITSO NDI CHOLINGA CHAKE.

Mukawulondola bwino moyo wa Yosefe,zinalipo nyengo zimene iye anadutsamo kuti apambane. Abale ake a Yosefe anayesetsa kuti akhoza kupha loto la moyo wake pomugulutsa ku Egypt koma sizinaphule kathu,mapeto ake Yosefe anakakwezedwa kukhala wolamulira.
Zilipotu nyengo za moyo m'moyo uno zimene zimadza kudzalimbana ndi chipambano chanu koma maso anu asamakhale pa nyengozo chifukwa mukapilira ndi kukhala okhulupilika pamaso pa Mulungu Iye adzakukwezani.

2. MUZIDZICHEPETSA KWAMBIRI CHIFUKWA GWERO LA KUKWEZEDWA KWANU LAGONA MU NKUDZICHEPETSA KWANU.

Yohane 3 : 30
Mu m'moyo wa kudzichepetsa muli zambiri zimene Mulungu amayikizamo kupatula kuti ukadzichepetsa Mulungu amakukweza. Ukakhala m'moyo wodzichepetsa umakhala dalitso kwa anthu ena ndipo Chisomo cha Mulungu chimakulondora kulikonse. Chisomo cha Mulungu tikunenachi chimakuyankhulira m'ma bwalo aanthu amene amadzitcha a nzeru nadzitamandira ndipo Chisomo ichi chimayankhula kuposa malingaliro aanthu.

3. KUMADZIWA KUTI NYENGO ZA MOYO SIZIBWERA KUTI ZIKUWONONGENI KOMA KUTI ZIKUWUMBENI KUKHALA MUNTHU WENIWENI.

1 Samuele 1 : 10 - 11
Akuluakulu moyo uno kulibe chidule cha zinthu,kuti ufike poti wakwanilitsa khumbo la moyo umayenera udutsemo.
There's no shortcut in life,Ayi kulibe!!! Achimwene tamvani, mukhoza kukwanilitsa zokhumba zanu mu njira ya chidule koma zomwe mufuna kukwanilitsazo sizidzakhazikika pa moyo wanu, njira iliyonse ya chidule imapweteketsa ndipo dalitso kale limakhala la kathawi kochepa.

4. MUZIKHALA NAKO KULIMBIKA MTIMA KUTI PALIBE MUNTHU AMENE AKHOZA KULEPHELETSA TSOGOLO LA MOYO WANU.

Yobu 42 : 2
Yesaya 14 : 27

Nzeru ya dziko la pansi Mulungu anayipusitsa ndipo palibe munthu amene amadziwa za tsogoro la munthu koma Mulungu yekha kotero kuti musamachite matha ndi onse amayankhula za tsogolo lanu chifukwa tsogoro la moyo wanu amalidziwa ndi Mulungu ngakhale inu mwini simulidziwa.
Musamakhale ndi matha ndi onse amene amati akhoza kuyimitsa chipambano cha moyo wanu.
Chifukwa cha maloto amene ankasonyeza tsogoro la Yosefe,abale ake anayesetsa kubweretsa njira zofuna kulimbana naye ndipo atamuguritsa ankayesa kuti athana naye osadziwa kuti Mulungu ankalondora mwachidwi maloto a Yosefe kufikira kuti Yosefe anakwezedwa kukhala wolamulira.
Wolimbana nanu adzakhalapo inde!! Ofuna kukutsekelezani musapambane koma musamakhale nawo khawa chifukwa onse olimbana ndi tsogoro lanu amathandizira inu kuti mupambane.

Yet to Finish this Month of August in this way at Likuni CCAP. All Youths lest gather here from 27th to 30th, Presbytery...
24/08/2026

Yet to Finish this Month of August in this way at Likuni CCAP. All Youths lest gather here from 27th to 30th, Presbytery mwini waitana.🔥🔥🔥🔥

23/08/2026

TAKULANDIRANI KU CHIPEMBEDZO CHATHU CHA LERO PA 23 AUGUST, 2026.

OTUMIKIRA. : MAYI THOMSON

Pamene nzeru zatha, pamene mphamvu zatha, ndipo tikumva kuti palibe njira ina ndi pamene Mulungu amatsika mu ulemelero w...
21/08/2026

Pamene nzeru zatha, pamene mphamvu zatha, ndipo tikumva kuti palibe njira ina ndi pamene Mulungu amatsika mu ulemelero wake ndikuyamba kugwira ntchito m'miyoyo yathu.

YEREMIYA 29 : 11
Ambuye amadziwa zimene mudzadya ndi zimene mudzavala mawa. Ali ndi zabwino zambiri zimene akukusungirani ngakhale lero mukudutsa m'nthawi yovuta. Choncho musafike pofuna kudzipha kapena kudzichotsera moyo poganiza kuti imeneyo ndiyo njira yothetsera mavuto anu. Moyo wanu ndi wamtengo wapatali ndipo nthawi yanu ya kusintha ikhoza kukhala pafupi kuposa momwe mukuganizira.

YESAYA 40 : 31
Kumbukirani kuti nthawi zina Mulungu amalola kuti tidutse m'mavuto osati chifukwa chakuti watitaya koma chifukwa akufuna kutiphunzitsa, kutikhwimitsa komanso kutipatsa kulimbika mtima. Mavuto a lero si mapeto a nkhani yanu.

Pitirizani kukhulupirira Mulungu. Ngakhale simukuona njira, iye akuiona. Ngakhale mphamvu zanu zatha, mphamvu zake sizitha. Nthawi yanu ikafika Mulungu adzachita zimene palibe munthu angathe kuchita.

Ukadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu ndipo ukamulora iye atenge ulamuliro wa kena kalikonse  pa moyo wako,amakuyika...
17/08/2026

Ukadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu ndipo ukamulora iye atenge ulamuliro wa kena kalikonse pa moyo wako,amakuyika pamwamba pamene ndi mapazi amunthu sungafikepo.

YOHANE 3 : 30
Uyu ndi udindo umene Khristu Yesu adadzipatsa yekha wotsitsa ndi kukweza anthu potengera ndi chikhalidwe chawo.

16/08/2026

TAKULANDIRANI KU CHIPEMBEDZO CHATHU CHA LERO PA 16 AUGUST, 2026.

AKUTSOGOLERA. : ELDER LOT DZONZI

11/08/2026

Feedbacks from Men's annual conference which took place at Mvunguti CCAP

Pictures from Msonkhano wa Abambo, hosted by Mvunguti CCAP ✨️😇
10/08/2026

Pictures from Msonkhano wa Abambo, hosted by Mvunguti CCAP ✨️😇

09/08/2026

TAKULANDIRANI LERO PA 09 AUGUST, 2026.
LERO NDI TSIKU LOMALIZA MSONKHANO WA CHIGWIRIZANO CHA ABAMBO KUNO KU MVUNGUTI CCAP

Address

Chinsapo, Chimphangu
Lilongwe
±265

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mvunguti CCAP Nkhoma Synod posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share