22/07/2026
MBUSA WA NKHOPE ZIWIRI
PART 11
Usiku unali wamdima kwambiri.
Evangelist Yohane sanagone konse pambuyo pa imfa ya Mr Gama.
Mawu aja olembedwa pa khoma la selo ankangobwereza m’maganizo mwake:
“CHOONA SICHINATHE…” 😳🔥
M’mawa mwake Evangelist Yohane anayitana Inspector Kalito mwachinsinsi.
“Tiyenera kudziwa anthu amene anali kumbuyo kwa Mr Gama.”
Inspector Kalito anangotsitsa mutu.
“Ndikukuuzani zoona… anthu amenewa ndi oopsa kwambiri.”
Mwadzidzidzi phone ya Inspector Kalito inayamba kulira.
Atayankha, nkhope yake inasintha.
“Kodi chiyani?!”
Evangelist Yohane anayamba kuchita mantha.
“Kwachitika chiyani?”
Inspector Kalito anayankha mwamantha:
“Church yanu yayaka moto!” 😭🔥
Nthawi yomweyo anathamangira ku church.
Atangofika, anthu ambiri anali kulira uku akuyang’ana moto wawukulu.
Mai Esther anayamba kukuwa:
“Bible zonse zapsa!”
Brother Chisomo anayamba kuthira madzi koma moto unkakulirakulira.
Evangelist Yohane anayima chete uku akuyang’ana church yake ikuyaka.
Koma mwadzidzidzi anaona munthu atavala hoodie wakuda ataima kutali uku akuyang’ana motowo.
Munthuyo atangoona Evangelist Yohane anayamba kuthawa.
“IMANI!” anafuula Evangelist Yohane.
Iye ndi Inspector Kalito anayamba kumuthamangitsa.
Munthuyo analowa m’nyumba yakale yosiyidwa.
Atalowa m’kati anapeza mdima waukulu kwambiri.
Mwadzidzidzi panamveka mawu kuchokera pamwamba:
“MUKUSEWERA NDI ANTHU AMENE SIMUKUWADZIWA…” 😳🔥
Inspector Kalito anayatsa torch.
Koma zimene anaona zinawachititsa mantha kwambiri.
Pa khoma panali zithunzi zambiri za ma pastor, ma evangelist ndi anthu ena amene anamwalira kale.
Ndipo pakati pa zithunzizo panali chithunzi chatsopano cha…
😳🔥
Evangelist Yohane
Pansi pa chithunzicho panalembedwa mawu amodzi:
“NEXT.”
Maiwe! 😭🔥
Kodi ndani akufuna kupha Evangelist Yohane?
Nanga chifukwa chiyani church yake yayakidwa moto?
TO BE CONTINUED… 🔥😳
📞 +265 88 42 83 545
WhatsApp
Dinani link ili musiyi kuti muzisate bwino.
Ciweluzo Chilipo -Judgement -by R R Malambo