18/01/2024
Kodi Yesu Khristu ndi mwana wa Mulungu?
Pamene taona kuti Quran likusimikizira ndi kuyikira umboni waukulu pa umphumphu wa Bible, tikuyeneranso kuona bwino Malo ena amene amatsutsana ndi bible.
Kodi Yesu Khristu ndi mwana wa Mulungu malingana ndi Quran? π
Surat 6:10 'Iye ndi Mlengi wathambo ndi nthaka, zingatheke bwanji kukhala ndi mwana pomwe iye alibe mkazi......? πChifukwa chaperekedwa apa ndi kungochepsa mphamvu ya Mulungu kuti sangakhale ndi mwana popanda mkazi. π Surat 3:45 "....Mulungu akukuuza nkhani yabwino kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu mau" β‘οΈ mukaonetsetsa Quran ikuchephya mphamvu ya Mulungu ndi kupereka mphamvu Kwa Mariya. πΆMariya anati atamva mau awa Kwa Mngeroπ
Mbuye wanga! Ndingakhale bwanji ndi mwana pomwe mwamuna aliyense sadandikhuze aliyense? Mngero adati, ndi momwemo Mulungu amalenga chomwe wafuna. Akafuna chinthu amachiuza 'chitika ndipo chimachitikadi (Surat 3:47). π Mungathe kukhala ndi ganizo through this Ayah kuti Mulungu amalenga chimene akufuna. Tikuona mabadwidwe a Yesu odabwitsa kuti ndithu Yesu Khristu ndi mwana wa Mulungu. 'Mateyu 1:18-21 Cholandilidwa mwa iye chilicha Mzimu woyera'. Luka 1:35 π '...Mzimu woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wankulukulu idzakuphimba iwe; chifukwa chakenso choyeracho chikadzabadwa, chizatchedwa Mwana wa Mulungu'. Quran ikuchitira umboni kuti kubadwa Kwa Yesu ndi chozizwitsa Kwa anthu. π Surat 19:20-21, 19:29-30. Tili ndi anthu amene anachitira umboni kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. 1. Nikodemo π Yohane 3:2, Yohane 20:30-31, Qur'an 3:49. Zizindikiro zimene Yesu anachita zili umboni wokwanira kuti Iye (Yesu) ali Mwana wa Mulungu.
Chifukwa china chaperekedwa pokana kuti Mulungu sangakhale ndi Mwana ndi "chakuti Chiyero chake Cha Mulungu" Quran 4:171 Ulemero wake ngotukuka kutali ndi kukhala ndi mwana" malingana ndi Quran nkwapatali Mulungu kukhala ndi mwana. Petro adayankha kuti; Inu ndinu Khristu Mwana wa Mulungu Wamoyo, Yesu anati ndiwe Odala Simon Bar-Yona....Mateyu 16:16-17. Mulungu mwini anayankhula kuti Yesu ndi Mwana wake; "Uyu ndie Mwana wanga wokondeka mwa Iyeyu ndikondwera" Mateyu 3:17. Mkulu wa Asilikari anati; π "Indedi Uyu ndi Mwana wa Mulungu " Mateyu 27:54. Mungathenso kuona mavesi osatirawa; Agalatiya 1:4, Aroma 1:1-4, Ahebri 1:1-2, Yohane 20:28. Ndi mavesi ena ambiri.
Conclusion; YESU KHRISTU NDI MWANA WA MULUNGU!