25/03/2022
MUSADANDAULE NDI ZAMAWA
◆◆◆◆
Ndi zachidziwikire kuti anthufe mwa chibadwa timadandaula kwambiri, timalira nthawi zambiri, timadera nkhawa nthawi zambiri, koma ngakhale ziri choncho Mulungu akutipempha kuti tikweze maso kwa iye,
Mvetserani zimene bukuli likunena
Mateyu 6:34
"Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace"
Kumbukirani kuti inu ndinu mkristu, ndi zowona kuti zosowa m'zambiri pa umoyo uno, maka polingalira kuti mawa tidzadya chani"
Koma Yesu akutipempha kuti "Tiyang'ane iye nthawi zonse", ndipo Yesu ndiye angalongosole za mawa lathu...
Nkutheka mawa mukupita kukaweruzidwa ku bwalo la milandu, ndipo mukudzifunsa kuti "Ndikayankha chani"?
Koma Yesu akutilonjeza kuti tikweze maso kwa iye' ndipo adzatithandiza...
Ngati ndinu mkristu kumbukirani kuti"Mulungu anakuchitirani chinthu chachikulu kwambiri pokupatsani mwayi kuti mukhulupirire Yesu' ndeno sangalephere kukuthandizani zochepazi....
Luka 12:29-30
"Ndipo inu musafunefune cimene mudzadya, ndi cimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima. Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi".
Chilichonse chimene muchisowa Mulungu akudziwa kuti muchisowa, ndipo monga mwa kuchuluka kwa chuma chake Mulungu adzakupatsani inu....
Ndi zoona imafika nthawi kuona kuti mavuto siyakuchoka pa nyumba lanu, koma kumbukira kuti "Pamene uli pafupi kulandira chabwino umavutika koopsa mpaka kulakalaka utapanga njira zina" Koma mupirire mukanthawika pakuti simudzadera nkhawa mpaka muyaya ayi...
Ndi chifukwa chake ndikukuuzani kuti "Tisafooke pakuti Yesu akuona" ndipo sadzalola kuti kapolo wake avutike mpaka nthawi yaikulu ayi....Koma iye adzapereka njira zoti mupezere chakudya ndi chobvala,
Ndimangofuna ndikulankhuleni mauwa basi,
ndingoti Ambuye akudalitseni kwambiri
onani musaiwale kupanga Like page ndiponso kupanga Share post kuti mauthenga ena yasakuphonyeni
tili ndi group ku WhatsApp, group la mau a Mulungu. ..ndipo ngati mukufuna kulowa eni nambala izi
+258878750070
+258862533330
+258868947783
Wolemba ndi Domingos Anthony
842405539
+258868947783