03/08/2026
Uthenga
2 August 26
Machitidwe Atumwi 28:1-10
"Phindu lakugwila ntchito ndi Mulungu"
1. Mulungu amakhala muombolo
* Paulo akanatha kufela panyanja patauka namondwe ndi kuswa ngalawa, koma Mulungu anamuombola.
* Paulo akatha kufa ndi ululu wa njoka imene inamuluma, koma Mulungu anamuombola.
2. Mulungu amaonetsa ekha chilungamo chake mwa ife
* Itamuluma njoka, anthu anamunenela kuti ndi ochimwa ndipo akuyenela kufa ndithu.
* Paulo sanayankhe kapena kudzifotokoza ekha kuti ndi olungama ai, kufikila anthu omwe aja ananena kuti uyu ndi Mulungu.
* Pamene akhristu tikugwila ntchito ndi Mulungu nkumabeza mau kwa iwo amene akunenela zoipa, timanyozetsa dzina la Mulungu.
* Paulo sanafune kunyozetsa dzina la Mulungu, ndipo Mulungu anaonetsela chilungamo chake mwa Paulo.
3. Mulungu amadzutsa anthu kuti akhale thandizo
* Publio amene anali osamudziwa Mulungu anabwela nakhala thandizo kwa Paulo.
* Atamuthandiza Paulo, banja lake linalandila machilitso
* Ukamagwila ntchito ndi Mulungu umakhala gwelo la madalitso pa banja lako ngakhaleso ku mtundu wakwanu.
*Moyo wa Paulo unatsimikizika kutumikila Mulungu, olo mavuto anali ochuluka koma sanabweleleso m'mbuyo.
*Akhristu tikhale anthu olapa mtima, olo zitavuta bwanji, tisabweleleso ku uchimo umene tinachokako kale.
By Mrs Chimbende
Media