Mwimba College of Agriculture SCOM

Mwimba College of Agriculture SCOM Mwimba College of Agriculture SCOM, Jesus loves you,loves me & loves us

Uthenga Womaliza wa SemesitaPamene tikumaliza semesita ino, tikuthokoza kwambiri nonse chifukwa cha mgwirizano umene mun...
18/08/2026

Uthenga Womaliza wa Semesita

Pamene tikumaliza semesita ino, tikuthokoza kwambiri nonse chifukwa cha mgwirizano umene munauonetsa, makamaka pakupezeka kwanu pa ma service. Chipanda inu, ma service onsewa sakanatheka. Zikomo kwambiri chifukwa cha kudzipereka kwanu ndi chikondi chanu pa ntchito ya Ambuye.

Pamene mukulowa mu mayeso omaliza, tikupempha kuti Mzimu Woyera akutsogolereni, akupatseni nzeru, mphamvu ndi mtendere, kuti mukachite bwino zonse zimene mwaphunzira.

Mulungu akudalitseni nonse, ndipo akhale nanu nthawi zonse. Amen. 🙏

“Tikuyamika kwambiri azitumiki onse mu semesita ino, omwe anadzipereka kukhala nafe potumikira Ambuye. Kudzipereka kwanu...
18/08/2026

“Tikuyamika kwambiri azitumiki onse mu semesita ino, omwe anadzipereka kukhala nafe potumikira Ambuye. Kudzipereka kwanu ndi ntchito yanu zatidalitsa kwambiri. Ambuye akudalitseni nonse, akupatseni mphamvu, ndipo apitirize kukugwiritsani ntchito. Amen.” 🙏❤️@

UTHENGA WOTHOKOZAKwa semesita ino, ndili ndi chikhulupiriro chakuti tonse tidalitsidwa kwambiri ndi Joint Service. Chonc...
18/08/2026

UTHENGA WOTHOKOZA

Kwa semesita ino, ndili ndi chikhulupiriro chakuti tonse tidalitsidwa kwambiri ndi Joint Service. Choncho, ndikufuna kupereka ulemu ndi kuthokoza kwambiri kwa RELIGIOUS PRESIDENT, Mr. Benjamin Custom, chifukwa cha utsogoleri wake komanso khama lake pothandiza kuti ma service athu aziyenda bwino.

Komanso, ndikufuna kuthokoza kwambiri abusa athu amene anatsogolera service. Iwo ndi amene anatumikira ndi kutipatsa mawu a Mulungu omwe anatikhudza ndi kutilimbikitsa kwambiri. Zoonadi, maulaliki awo anali odabwitsa ndipo tatengapo madalitso ambiri.

Sitingathe kutchula aliyense payekhapayekha, koma kwa nonse amene munapezeka pa ma service komanso munathandizira m’njira zosiyanasiyana, tikunena kuti zikomo kwambiri. Kupezeka kwanu ndi kutenga nawo mbali kwanu kunathandiza kwambiri kuti Joint Service iyi ikhale yopambana.

Zikomo kwambiri nonse. Mulungu akudalitseni, akusungeni, ndipo apitirize kutitsogolera m’njira yake. 🙏❤️

HAPPY birthday 🎉 🎂 brother Felix Likwenga Our former Religious Director at Mwimba college of Agriculture, may the good l...
12/07/2026

HAPPY birthday 🎉 🎂 brother Felix Likwenga
Our former Religious Director at Mwimba college of Agriculture, may the good lord bless you we still appreciate your leadership Amen
let's celebrate with him Mlimi Felie

Kumaliza komaso kuyamba kwake kunali kosangalatsa kwambiri. Tidadalitsidwa ndi mayimbidwe abwino, mavinidwe osangalatsa,...
28/06/2026

Kumaliza komaso kuyamba kwake kunali kosangalatsa kwambiri. Tidadalitsidwa ndi mayimbidwe abwino, mavinidwe osangalatsa, komanso ulaliki wapamwamba wochokera pa mutu wakuti, "The Holy Spirit." Zikomo kwambiri kwa aliyense amene anatenga nawo mbali. Mulungu akudalitseni nonse. 🙏

"Iyi ndi Joint Service yoyamba mu semester ino. Tikuthokoza Mulungu chifukwa watifikitsa pano. Tikukuthokozani nonse chi...
28/06/2026

"Iyi ndi Joint Service yoyamba mu semester ino. Tikuthokoza Mulungu chifukwa watifikitsa pano. Tikukuthokozani nonse chifukwa chobwera. Ife tikukulandirani ndi manja awiri ndipo timakondwera kukhala nanu. Pamene tikuyamba mayeso a pakati pa semester (Mid-Semester Examinations), tikupemphera kuti Mulungu akutsogolereni, akupatseni nzeru, mphamvu ndi chisomo pa zonse zomwe mukuchita. Mulungu akudalitseni nonse. Amen."

26/05/2026

Palibe kathu kamene kamamulaka yehova Luka 1: 37

The bible say on Mateyu 18:20“Pakuti pamene pali awiri kapena atatu osonkhana m’dzina langa, Ine ndili pakati pawo.”Come...
22/05/2026

The bible say on Mateyu 18:20
“Pakuti pamene pali awiri kapena atatu osonkhana m’dzina langa, Ine ndili pakati pawo.”

Come an testifies the power en groly

22/05/2026

Ku Scom lero kuli program yanji?

16/05/2026

A SCOM mulipooo.

Address

Kasungu

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mwimba College of Agriculture SCOM posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share