14/07/2026
⌚2:58 min
Pastor Martin Mkandawire
NGATI MUFUNA MUZAPITE UFUMU WAKUMWAMBA MUKUYENERA MULANDILE UBATIZO WA MZIMU WOYERA. ( _This is A Must_ )
Kuti Mulandile Ubatizo Wa Mzimu Woyera Muyenela Mulape Mosweka Mtima ( Osasiyako Ntchimo losalapidwa) , Mukatelo Mubatizidwe Mdzina La Ambuye Yesu Khristu Kuloza Kuchikhululukiro Chama Chimo Anu, Ndipo Muzalandila Mphatso Ya Mzimu Woyera.
Zichitike monga Zinaliri Matsiku Aah Atumwi, Pomwe Anthu ankawabatiza Mdzina La Ambuye Yesu Khristu. Osati Kunena kuti tikukubatiza iwe Mdzina la Atate Mwana Mzimu Woyera monga Mipingo ichitila lero, Osatchula dzina ,zimenezo Ayi . Satilani Momwe Ubatizo Ulili Monga Mwa Malemba,Kutengela ndi Vumbulutso lomwe linadza Patsiku La Pentecost, Muka Mabatizidwa Mdzina La Ambuye Yesu Khristu,Mubatizidwe Madzi Ambiri monga Zinaliri nthawi Ya Aah Atumwi,komanso Yesu Iye mwini Anapita Ku Madzi Ambiri.
MUKATELO Musanjikidwe manja ndi Atumiki Alindi Mzimu Woyera,kuti Akupempheleleni Kuti Mulandile Ubatizo Wa Mzimu Woyera ,Musate Dongosolo lonse loyenela lanenedwa Apa Mulandila Ubatizo Wa Mzimu Woyera.
Inuyo Ndindani Kuti Musamvele ??? Ndi Zoona kuti Atumwi ankabatiza m’dzina la Yesu Khristu ,ndipo ankabatiza Ubatizo omiza m’madzi ambiri, monga pa Machitidwe 10:48, 19:5. Kenako anasanjikidwa manja ndi atumiki odzazidwa ndi Mzimu Woyera kuti alandire Mzimu Woyera.
Dongosolo limeneli silinasinthe. Mipingo yambiri lero yasintha chiphunzitsocho, koma Mau a Mulungu akadali omwewo.
M’buku la Machitidwe 2:38.
Petro anati
- Lapani – tembenukani ku machimo anu
- Mubatizidwe m’dzina la Ambuye Yesu Khristu – kuloza ku chikhululukiro cha machimo
- Mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera
NDE PALI ENA AMATI NDINA BATIZIDWA KALE
- Muwelenge Machitidwe 19:1-6 , Pamenepo Anthu Ata Zindikila kuti Sanabatizidwe Ndi Mzimu Woyera Anabatizidwanso Kenaka Kulandila Ubatizo Wa Mzimu Woyera Uja.
Malemba Awonjezera Awubatizo
Maliko 16:16
Yohane 3:5
Yohane 3:23
Efeso 4:5
Ambuye Akudalitseni Pamene Mukuchita chimenechi