Chisita S.D.A Church

Chisita S.D.A Church Chisita Seventh-day Adventist (SDA) Church is a religious organization based in Dwangwa, Nkhotakota, Malawi.

ACHINYAMATA A YOUNG AMO ACHITA NTCHITO ZA CHIFUNDO PA CHIPATALA CHACHING'ONO CHA NKHUNGALero, pa 26 July 2026, achinyama...
26/07/2026

ACHINYAMATA A YOUNG AMO ACHITA NTCHITO ZA CHIFUNDO PA CHIPATALA CHACHING'ONO CHA NKHUNGA

Lero, pa 26 July 2026, achinyamata a gulu la Young AMO anachita pulogalamu ya Ntchito za Chifundo pa Chipatala Chaching'ono cha Nkhunga.
Monga mbali ya pulogalamuyi, achinyamatawa anakumana ndi amayi oyembekezera, kucheza nawo, kuwagawira mawu olimbikitsa ochokera m'Baibulo, komanso kuwaimbira nyimbo zotamanda Mulungu.

Elder Humphrey Kampira, omwe ndi sponsor wa gululi, ndi amene anawerenga Mawu a Mulungu kuchokera pa Genesis 22, pomwe Mulungu anayesa Abrahamu pomupempha kuti apereke mwana wake yekhayo, Isake, ngati nsembe. M'mawu awo analimbikitsa kuti ana onse ndi mphatso zochokera kwa Mulungu, choncho ayenera kuleredwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Anawerenganso Luka 2:52, ponena kuti amayi ndi aphunzitsi oyamba a ana awo, ndipo ali ndi udindo waukulu wowalera m'njira yoyenera.

Pambuyo pa uthengawo, achinyamatawa anapereka thandizo la zinthu zosiyanasiyana monga shuga, sopo, mafuta odzola, glycerin, ndi zinthu zina kwa amayi omwe anali pa chipatalapo.
Kenako anapitiriza ndi ntchito za ukhondo pa chipatalapo, kuphatikizapo kusesa bwalo, kufukura ngalande, kutchetcha udzu, komanso kukolopa malo osiyanasiyana.

Polankhula m'malo mwa mkulu wa chipatalacho, Mai Tembo, omwe ndi namwino, anayamikira kwambiri ntchito yomwe achinyamatawa anachita. Iwo anati:
"Mwapanga zinthu zazikulu kwambiri. Azimayi awa amasowa zinthu zambiri. Mwawapatsa uthenga wauzimu komanso katundu wothandiza. Mulungu akudalitseni kwambiri."

Nayenso mtsogoleri wa Young AMO, Success Heran, anasonyeza chisangalalo kuti cholinga cha gululi chikukwaniritsidwa. Iye ananena kuti achinyamata ali ndi udindo wotumikira Mulungu mwa kuthandiza anthu onse, mkati ndi kunja kwa mpingo. Anapemphanso utsogoleri wa mpingo kuti upitirize kuwathandiza ndi kuwathandizira pa mapulogalamu awo omwe akubwera.
Wolemba; Evangelist Humphrey Kampira


25/07/2026

The church found this song special Worthy to be repeated

Verse after verse, chapter after chapter, the children of Chisita S.D.A Church  reminded the entire congregation of God'...
25/07/2026

Verse after verse, chapter after chapter, the children of Chisita S.D.A Church reminded the entire congregation of God's greatest gift:
"For God so loved the world that He gave His only begotten Son, that whoever believes in Him should not perish but have everlasting life." β€” John 3:16
Their confident recitations, inspiring songs, powerful dramas, and heartfelt messages served as both a warning and an invitation to prepare for Christ's soon return.

25/07/2026

SEVENTH DAY ADVENTIST CHISITA
DATE: 25 JULY 2026
PREACHER: BILLY KAMPANTENGO AND MARRY MADEYA
"CHIKONDI CHA MULUNGU"
CHILDREN'S DAY

BAULEKANI CHAKA CHINO CHOKHA by CHISITA ADVENTIST YOUTH (LUKE 13:6-15. ISAIAH 5:1-7)This past Sabbath, Chisita S.D.A Chu...
19/07/2026

BAULEKANI CHAKA CHINO CHOKHA by CHISITA ADVENTIST YOUTH (LUKE 13:6-15. ISAIAH 5:1-7)
This past Sabbath, Chisita S.D.A Church Adventist Church witnessed the remarkable results of dedication, discipline, and consistent preparation by her Adventist Youth.

Every presentation reflected confidence and excellence no stammering, no hesitation, no doubt. Just outstanding performance built through resilience, commitment, continuous practice, and thorough training.

Indeed, excellence is never an accident; it is the product of hard work, perseverance, and God's guidance. We give all the glory to God for the success of our Adventist Youth!!

18/07/2026
18/07/2026

SEVENTH DAY ADVENTIST CHISITA CHURCH
DATE: 18 JULY 2026.
PREACHER: ALINAFE NAMPONYA
THEME IG THE DAY: BAUULEKANI CHAKA CHINO CHOKHA

11/07/2026

SEVENTH DAY ADVENTIST CHISITA.
PREACHER: ELDER Samson Walota. ( KUIMILIRA MULUNGU MMALO OVUTA NDI OIPA)
SINGING GROUP: CHISITA CHURCH CHOIR.

Mwawuka uli anthu amulungu?😊Pamene dziko lafika povuta ,pamene anthu akukana choonadi pakufunika amuna nda kazi olimba m...
11/07/2026

Mwawuka uli anthu amulungu?😊
Pamene dziko lafika povuta ,pamene anthu akukana choonadi pakufunika amuna nda kazi olimba mtima,omwe angayime nji ! Pa choonadi .
lelo yakonza chi program chabwino πŸ˜‡πŸ€—.chopeleka chiyembekezo mu dziko lopanda chembemezo.

Theme;Kuyimila Mulungu m'malo ovuta ndi oipa.
See you there 😊
Chisita S.D.A Church

On behalf of Chisita Seventh-day Adventist  Church, we would like to wish all Form 4 candidates God's blessings as they ...
29/06/2026

On behalf of Chisita Seventh-day Adventist Church, we would like to wish all Form 4 candidates God's blessings as they begin their examinations today.
May the Lord grant you wisdom, knowledge, strength and peace throughout your exams. We pray for success in all your efforts. May God be with you. All the best!" πŸ™πŸ“šβœοΈ
Let's wish them all the best .

Address

Chisita Seventh-day Adventist (SDA) Church Interstate A Religious Organization Based In Dwangwa, Nkhotakota
Dwangwa

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Chisita S.D.A Church posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share