Mua Parish Diocese of Dedza

Mua Parish Diocese of Dedza Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Mua Parish Diocese of Dedza, Religious organisation, Mua Mission, Dedza.

LAMULUNGU LA 3 LA PASAKA—A.“Yesu akutitsogolera m’njira yopita kwa Atate.”MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA N...
18/04/2026

LAMULUNGU LA 3 LA PASAKA—A.
“Yesu akutitsogolera m’njira yopita kwa Atate.”

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 2:14, 22-33 (Kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa).

Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mawu kuti, “inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga. Inu Aisraele mverani mawu awa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziwa. Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m’mene Iye amadziwiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda. Koma Mulungu adammasula ku zowawa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe pa mtanda. Paja Davide ponena za Iye adati, ‘ndinkaona Ambuye Mulungu pamaso panga nthawi zonse, pakuti amakhala ku dzanja langa lamanja kuti ndingagwedezeke. Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa, ndipo ndinkalankhula mosangalala. Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m’manda, ndikhulupirira kuti simudzandisiya ku malo akufa, kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole. Mudandidziwitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’ Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m’manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano. Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziwa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzalowe ufumu wake. Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, ‘Iye sadasiyidwe ku malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’ Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira.”

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 16:1-2, 5, 7-11.

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

Mundisunge In Mulungu pakuti ndikuthawira kwa Inu,
Ndimamuuza Chauta kuti, Inu ndinu Ambuye anga,
Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa,
Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe,
Nthawi zonse ndimalingalira za Chauta,
Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja palibe amene angandiopse konse.

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,
Ndipo m’katikati mwangamu ndikusangalala,
Thupi langanso lidzakhala pabwino,
Chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa,
Simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

Mumandiwonetsa njira ya ku moyo,
Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,
Ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.
--------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 1 PETRO 1:17-21 (Adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu).

Okondeka, Mulungu alibe tsankho. Amaweruza aliyense molingana ndi zochita zake. Ngati mumutcha Atate pamene mukupemphera, mchitireni ulemu nthawi yonse muli alendo pansi pano. Mukudziwa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema. Iyeyo Mulungu adaamsankhiratu dziko lapansi lisanalengedwe, koma wamuwonetsa nthawi yotsiriza ino chifukwa cha inu. Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adaamukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—LUKA 24: 32.
Alleluia, Alleluia—Ambuye Yesu, mutitanthauzire Malembo. Mitima yathu iyake
mwa ife pamene mumalankhula nafe—Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 24:13-35 (Maso ao adatsekuka, namuzindikira pamene adanyema buledi).

Tsiku lomwelo ophunzira awiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi. Ankakambirana za zonse zimene zidaachitika. Akukambirana choncho nkumafunsana, Yesu mwini wake adayandikira nkumatsagana nawo. Koma maso ao adachita chidima, mwakuti sadamzindikire. Tsono Yesu adawafunsa kuti, “kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?” Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni, kenaka mmodzi, dzina lake Kleopa, adamufunsa kuti, “kodi mlendo ndinu nokha m’Yerusalemu muno, wosadziwa zimene zochitika m’menemo masiku apitawa?” Yesu adawafunsa kuti, “zotani?” Iwo adati, “za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali za mphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe. Akulu a ansembe ndi akulu ena adampereka kuti azengedwe mlandu ndi kuphedwa, ndipo adampachita pamtanda. Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi. Komanso azimayi ena a m’gulu lathu anatidabwitsa. Iwowo anapita ku manda m’mamawa, ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti Yesu ali moyo. Ena mwa ife anapita kumandako, ndipo anakapezadi monga momwe Azimai aja amasimbira, koma Iyeyo sadamuone ai.” Apo Yesu adati, “Ha! Koma ndiye ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira mnsanga zonse zija zimene aneneri adanena. Kodi inu simukudziwa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zowawa zonsezi kuti alowe mu ulemerero wake?” Kenaka Yesu adayamba kuwatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m’Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse. Atayandikira kumudzi kumene ankapita, Yesu adachita ngati akupitirira. Koma iwo adamuumiriza kuti, “mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; Onani dzuwa likulowa.” Apo Iye adakalowa m’Nyumba nakakhala nawo. Pamene adakhala nawo podyera, Yesu adatenga buledi, ndipo atathokoza Mulungu, adamnyema nawagawira. Nthawi yomweyo maso ao adatsekuka, namuzindikira, Iye nkuzimirira. Tsono iwo adayamba kukambirana kuti, “zoonadi ndithu, mitima yathu inachita kuti phwii, muja amalankhula nafe panjira paja, nkumatitanthauzira malembo.” Nthawi yomweyo adanyamuka kubwerera ku Yerusalemu. Adakapeza ophunzira khumi ndi mmodzi aja atasonkhana pamodzi ndi anzao ena, akunena kuti, Ambuye adaukadi, ndipo Simoni wawaona. Tsono nawonso awiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira paja, ndiponso m’mene iwo adaamzindikira pamene iye ankanyema buledi.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------

Mapemphero a Akhristu

Abale, tamva mau a Yesu Khristu alikutanthauzira Malembo Oyera. Tiyeni timupemphe kuti kuwala kwake kuunikire anthu onse:

1. Mpingo wa Mulungu uunikire anthu onse ndi maphunzitso ake ndi makhalidwe ake, powaonetsa kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2. Anthu amene akuvutika mumtima ndi kuyenda mu mdima, maso ao atsekuke popezana ndi Yesu Khristu m’Malembo Oyera.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anzathu amene ali ku ulendo ndi ena onse okhala okha kutali ndi kumudzi kwao, adziwe kupirira mavuto aliwonse, pokhulupirira Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4. Ife tonse osonkhana pano, tipemphererane kuti tithe kuzindikira nkhope ya Yesu Khristu mwa anthu amene timakumana nawo masiku onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

Mulungu Atate athu, tikuyamikani chifukwa mudatipatsa Mwana wanu kuti atsagane masiku onse pa ulendo wathu wonka kwa Inu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

12/04/2026

MAU A MULUNGU OWERENGEDWA PA TSIKU LAMULUNGU PA 12 APRIL, 2026

LAMULUNGU LACHIWIRI LA NYENGO YA PASAKA

LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA MULUNGU - DIVINE MERCY SUNDAY

MAU OYAMBA A M'BUKHU LA NTCHITO ZA ATUMWI 2:42-47

Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.”

Mau a Ambuye

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 2-4, 15c-16b, 17-18,22-24

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino ndipo chikondi chake nchamuyaya

Aisraele anene kuti,
“Chikondi chake nchamuyaya.”
Banja la Aroni linene kuti,
“Chikondi chake nchamuyaya.”
Anthu oopa Chauta anene kuti,
“Chikondi chake nchamuyaya.”

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya

“Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,
dzanja lamanja la Chauta lapambana,
dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”
Sindidzafa, ndidzakhala moyo,
ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.
Chauta wandilanga koopsa,
koma sadandisiye kuti ndife.
Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya.

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,
womwewo wasanduka mwala wapangodya.
Chauta ndiye amene wachita zimenezi,
zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

MAWU ACHIWIRI A M'KALATA YOYAMBA YA PETRO 1:3-9

Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza. Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zoŵaŵa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthaŵi. Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.”

Mau a Ambuye

ALLELUIA
“Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.”
ALLELUIA

UTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA 20:19-31

Patapita masiku asanu ndi atatu Yesu adaonekera

Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adaŵaonetsa manja ake ndi m'nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri poŵaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adaŵauzira mpweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzaŵakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzaŵakhululukira, sadzakhululukidwa ai.” Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “Ife taŵaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “Ndikapanda kuwona mabala a misomali m'manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m'nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.” Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m'nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m'nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m'buku muno. Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m'dzina lake.“

Uthenga wa Ambuye

08/04/2026
06/04/2026

Njira ya Mtanda. Dera la Golomoti.

Address

Mua Mission
Dedza

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mua Parish Diocese of Dedza posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share