23/02/2023
GOOD MORNING SAINTS
*WELCOME* *TO* *TODAY'S* *MORNING* *DEVOTION*
23 February 2023
*YEHOVA* *AGWEDEDZA* *KACHIWILINSO*
*Bible* *reading* *Hagai* *2:6-7*
---------------------------------------
6. " Pakuti atero Yehova wa makamu kamodzinso , katsala kanthawi , ndidzagwededza miyamba ndi dziko lapansi , ndi nyanja ndi mtunda omwe
7 . Ndipo ndidzagwededza amitundu onse ndi zofunika za amitundu onse zidzafika ndipo ndizazaza nyumba iyi ndi ulememelero ati Yehova wa makamu
---------------------------------------
Kuchokera ku lemba lomwe tawelenga ku Hagai 2:6-7 Mulungu akuyankhula chifukwa cha ulememelero omwe unachoka pa nyumba yake , anafika nawo anthu onse kunyumba yake nawafumsa kuti kodi ndi ndani mwainu amene anaona ulemelero wa nyumbayi wakale nanga. Ndi momwe ukuonekera panomu zikufanana mwanjira ina Yehova amafuna kuonetsa kuti zinthu sizili momwe zinalili
Pali zinthu zambiri zomwe zimachotsa ulememelero omwe unali pa moyo wanu mukakhala mumatha kumva kuti koma moyo wanga momwe ndimakhalira si umumu, chikondi cha banja langa momwe chinalili poyamba simomwe chilili pano , business yanga momwe imayendera si umumu kunena zoona ulememelero wanu unachoka potengera momwe munalili masiku amenewo koma lero ambuye akuyankhula nanu kuti
*AGWEDEDZA* Yehova miyamba , nyanja ndi zitunda zomwe ndipo ndipo akuti adzadzadza nyumba yake ndi ulemelero ochuluka oposa wapoyamba
Tamverani pakufunika Yehova avute ndikugwededza paliponse pamene pasakamira dalitso lanu mawu oti kugwedeza ndiye kuti zinthu zo nzothekatheka kale koma zangoima pena pake koma Mbuye ndiwabwino *AGWEDEDZA* nsi dzanja lake LA mphamvu ndipo what ever belongs to you it coming in Jesus name
Ndipo pakutha pakugwededza kwake Yehova ulememelero omwe unachoka ubwerere pamoyo wanu , banja lanu , business yanu , utumiki wanu , mu dzina la yesu
Zinthu zibwerere momwe zinalili mu dzina la yesu
*Apostle* *I.s* *Malinda* *ministries* *intl*