30/01/2025
Gulu la anthu ochita malonda ang'ono ang'ono mu mzinda wa Blantyre lotchedwa Business Connections lamanga ndi kupereka nyumba yatsopano ku banja la a Nkweza, omwe amakhala m'mudzi mwa Jamusoni, T/A Kapeni, m'boma la Blantyre.
Bambo James Nkweza, omwe ankachita malonda awo mu nsika wa Blantyre anadwala matenda okufa ziwalo (Stroke) m'chaka cha 2020, ndipo akhala akuvutika kusamalira banja lawo kuphatikizapo ana awo asanu.
Wapampando wa gululi a Edward Mona, wati nyumbayi yamangidwa ndi ndalama zokwana pafupifupi K4.3 million, zimene mamembala a gululi akhala akusonkha.
Patsikuli, gulu la Business Connections laperekanso katundu osiyanasiyana kuphatikizapo ufa, soya pieces komanso zavala kwa anthu ozungulira a m'mudzi mo.
Wolemba Llywellenie Mpasa