Yesu akubweranso posacedwa by evangelist Jacob J Chikadza

Yesu akubweranso posacedwa by evangelist Jacob J Chikadza Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Yesu akubweranso posacedwa by evangelist Jacob J Chikadza, Full Gospel Church, Malawi university of business and applied sciences, private bag 3, chichiri, Blantyre.

18/05/2025

TINGAFIKE BWANJI KU MPANDO WA CHIFUMU?

Thawi zina timankhala ndi nkhawa, komanso mantha kuti koma zopempha zanga Mulungu a ndiyankha?

Maka ukamalingalira za ntchito zako zoyipa pena umangodziweluza kuti ndingodzitayitsa thawi.

Dzulo ndinatele, lelo ndatele komanso zoganiza zanga ndizosakondweletsa Mulungu.

Bola ndizingonkhala muuchimo momwemu.

Okondedwa ayi sichoncho ndiye kuti kubwela kwa yesu khristu kuli chabe,.

Iyeyutu anabwelera anthu ochimwa ngati ife kuti tikazindikila kulakwa kwanthu timulile iye kuti atichotsele chosalungama chanthu.

Ndizimamukondweletsa akamaona ochimwa ngati ine ndikusiya njira zanga zoyipa.

Chifukwa chake nthawi zonse munkhale ntcheru chifukwa akuti tsoka mtunda ndi nyanja poti oyipa watsikila komweko.

Nchifukwa chake ndi bwino nthawi zonse kusendera chifupi ndi mtanda ndipo timuuze ambuye ndilipano ndikonzeni ndikundimasula kuuchimo wanga.

AFILIPI 4:6

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

good night

17/05/2025

PENA UKAMACHIMWA UMANGOONA NGATI ALIYENSE AKUCHIMWA .

Munthu okagwa m'manja mwa MULUNGU umayesetsa upeze tizifukwa toti winaliyense akuvetsetse .

Ndipo umanyoza azitumiki a yehova omwe akukudzudzula ndikugwilizana ndi iwo akukondwela ndikulephera kwako mwa ambuye.

Koma chakuti mudziwe mchakuti kugwa m'manja mwa MULUNGU ndikooopsa moti ambiri amakathela konko

1 YOHANE 3:6

Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuona Iye, ndipo sanamdziwa Iye.

amen

15/05/2025

NJIRA YA KUMVERA NDI NJIRA YOPITA KU CHOYERA

(Ellen G. White)

Dziko lapansi ndi ngati bwalo la sewero. Anthu omwe ali m’dziko lino ndi osewera, ndipo akukonzekera kuchita mbali yawo mu sewero lalikulu lomaliza. Mulungu akuyiwalika. Palibe mgwirizano wa cholinga, kupatula pamene magulu a anthu akumangika limodzi kuti apeze zofuna zawo. Koma Mulungu akuyang’ana. Cholinga chake chokhudza anthu amene amumukira chidzachitika. Dziko lapansi silinaperekedwe m’manja mwa anthu ngakhale kuti Mulungu akulola chisokonezo ndi kusakhazikika kulamulira kwakanthawi.

Mphamvu yochokera pansi ikugwira ntchito ndi chinyengo chonse cha kusayenera mwa anthu amene akumangika limodzi m’magulu achinsinsi. Amene akulola kufuna mgwirizano monga cholinga chawo akugwira ntchito za mdani. Zimenezi zidzabweretsa zotsatira zake.

Kupandukira kwafika pafupi ndi malire. Kusokonekera kwadzaza dziko lapansi, ndipo mantha akulu akubwera posachedwa pa anthu. Mapeto ali pafupi kwambiri. Ife amene tikudziwa choonadi tiyenera kukonzekera zimene zikubwera posachedwa ngati kudabwa kwakukulu...

Oipa asankha Satana kukhala mtsogoleri wawo. M'manja mwake, mphamvu zazikulu zomwe Mulungu wapatsa anthu zamtima ndi malingaliro zikugwiritsidwa ntchito kupanga zida zowononga. Mulungu wapatsa anthu mphamvu zazikulu, kuti awonetse kuti Wopanga wathu watipatsa luso lopambana mdani wa chilungamo. Pamenepo tingaone zinthu zazikulu zomwe zingapezeke pakumenyana ndi zoyipa...

Koma pamene anthu amene Mulungu awapatsa maluso amapereka okha m’manja mwa mdani, amakhala mphamvu yowononga. Pamene anthu sasiya Mulungu kukhala woyamba, womaliza, ndi wabwino pa chilichonse, ndipo sathandiza kuti zofuna za Mulungu zichitike mwa iwo, Satana amalowa m’malo mwake ndipo amagwiritsa ntchito malingaliro awo. Pansi pa utsogoleri wake, amagwira ntchito yoipa ndi mphamvu yayikulu komanso luso lalikulu. Mulungu ankafuna kuti anthu amenewa agwire ntchito pa mlengalenga wapamwamba, kulowa m'maganizo ake, ndiponso kupeza maphunziro amene angawathandize kugwira ntchito zolungama. Koma iwo sadziwa kanthu za maphunziro amenewa. Ali osathandiza. Malingaliro awo sakuwatsogolera bwino chifukwa ali m’malo mwa mdani.

Njira ya ku chiyero ndi ya kumwamba imapezeka mu njira ya kumvera.
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapereka Mwana wake wokha yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatumize Mwana wake kudziko lapansi kuti awaweruze dziko, koma kuti dziko lapansi lidzapulumuke kudzera mwa Iye. Amene amakhulupirira Iye saweruzidwa: koma amene samakhulupirira akhala ataweruzidwa kale, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wa Mulungu wokha yekha. Ndipo kuweruzidwa n’kumeneku: kuti kuunika kwabwera kudziko lapansi, koma anthu anakonda mdima kusiyana ndi kuunika, chifukwa zochita zawo zinali zoyipa." (Yohane 3:16-19)

14/05/2025

*TIPEMPHE NZERU KWA MULUNGU*
Yakobo 1:5
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

*NGATI WINA NZERU YAMUSOWA APEMPHE NZERU KWA MULUNGU NDIPO ADZALWNDIRA MOPANDA KUTONZELA*

PA MOYO WATHU PAKUFUNIKA NZERU KWAMBIRI
- NZERU YA BUSINESS
- NZERU YA ULIMI
- NZERU YA NTCHITO
- NZERU YOKHULULUKA
- NZERU YODZICHEPETSA
- NZERU YAMAPHUNZIRO
- NZERU YA UZIMU
- NZERU YA MTENDERE
- NZERU YA BANJA
- NZERU YOLELERA ANA

ANTHU ANGA AKUONONGEKA CHIFUKWA CHA KUSADZIWA
NDI ZINA ZAMBIRI
Hoseya 4:6
Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.

13/05/2025

*KUOPA YEHOVA;*
Miyambi 1:7 *Kuopa Yehova* ndiko ciyambi ca kudziwa; Opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

Miyambi 8:13 *Kuopa Yehova* ndiko kuda zoipa; Kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.

Miyambi 1:22-23 Kodi mudzakonda zacibwana kufikira liti, acibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, Opusa ndi kuda nzeru? Tembenukani pamene ndikudzudzulani; Taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, Ndikudziwitsani mau anga.
🙏🏻🙏🏻🙏🏻

04/05/2025

MGONERO WA MAU A MULUNGU PA MOYO WATHU.

2 PETRO 3:14
Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, citani cangu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda cirema.

🌹✍️Okondedwa zakuti tili mmasiku otsiliza tauzidwa ndipo talalikidwa, zakuti tikuyenera kusamba ndi kuchoka mu uchimo tauzidwa, koma lero tikungofuna zakuti, tichite zimene tauzidwa koma mwa changu, Loti atauzidwa zakutuluka mu S***m mwachangu atava anachita ndipo chipulumutso chinafika pa moyo wake, lero chenjezo ili likupita pa moyo wathu zakuchotsa mawanga pa moyo wathu ndikukhazikika pamaso pa Mulungu, ndikudziwa za mphoto ya uchimo munalalikidwa, Okondedwa tiyeni tibwelere ndi kuchotsa mawanga pamoyo wathu kuti tidzakhare mzika mu Ufumu wa Kumwamba. Khalani akumva ndi kuchita kulankhura kwa Mulungu. AMBUYE AKUDALITSENIII NDI KUSUNGA MOYO WANU.AMENIIIÌI

03/05/2025

Amosi 9:11 mau akuti;

Tsiku lomwero ndidzautsa msasa wa David udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo.

Mwa mau awa, Mulungu akumbukire nyengo zanu okondedwa;
Ngati zidagwa Mulungu azidzutsenso
Ngati zidafooka Mulungu azilimbikitse
Ngati zidasokonekera Mulungu azibwezeretse
Ngati zilibwino Mulungu akulitse malire ake.

Yehova awalitse nkhope yawo pa ife natichitire zokoma,
Zabwino zonse

20/10/2024

Address

Malawi University Of Business And Applied Sciences, Private Bag 3, Chichiri
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Yesu akubweranso posacedwa by evangelist Jacob J Chikadza posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share