Nancholi CCAP Church

Nancholi CCAP Church Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Nancholi CCAP Church, Religious organisation, Chikwawa Load after Blantyre city and at Manase Police turn to right, Blantyre.

achinyamata mwayi uwu ndiwathu tiyen tiugwilise ukuku sikojombayi
17/04/2026

achinyamata mwayi uwu ndiwathu tiyen tiugwilise

ukuku sikojombayi

Palm Sunday with moderator
31/03/2026

Palm Sunday with moderator

your all invited
31/03/2026

your all invited

Akhristu a mpingo wa Nancholi CCAP amene akuchita maphunziro otathauzira Mau a Mulungu a Veritas lero alandira ma certif...
31/08/2025

Akhristu a mpingo wa Nancholi CCAP amene akuchita maphunziro otathauzira Mau a Mulungu a Veritas lero alandira ma certificate awo atatsiliza magawo osiyanasiyana.

Pa mwambo'wu umene unachitikira pa mpingo wa Nancholi CCAP mu presbytery ya Blantyre City mlendo olemekezeka anali Bambo Bello Mawindo kuchokera Ku office ya CCAP Blantyre Synod Veritas.

Mawindo walimbikitsa onse amene alandira certificate kamba kotsiriza gawo lawo kuti apitirize ndi magawo ena mpaka afike kumapeto kwa maphunziro'wa.

Moderator wa mpingo wa Nancholi CCAP amenenso ndi mkulu wa wa nthawi yolalikira mau a Mulungu mu CCAP Blantyre Synod mbusa Davidson Moyo walimbikitsa ophunzila amene achita bwino pa maphunziro'wa kuti akachite zimene aphunzi

Mbusa Moyo wati maphunziro amene'wa amathandiza akhristu kudziwa mawu a Mulungu komanso amathandiza kupewa kunamizidwa ndi alaliki ena omwe sadziwa malemba.

08/08/2025

Morning Devotion

Tayamba ndikupembezera, kupemphelera mabanja athu, mpingo wathu komaso chipembezo chathu chikubwelachi popeza chikutsogoleredwa ndi ana athu.
Tapempheleraso dziko lathu pamene tikuyembekezera ku voter nde taikiza mapemphero kuti Mulungu atithandizire kuti tisankhe mtsogoleri oopa Ambuye, Odziwa mau kuti dziko lathu lisapite kuchionongeko.

ULARIKI
tinawelenga ma bukhu awiri
2 Samueli 11:1
Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.
2 Samueli 11:2
Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa k**a wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
2 Samueli 11:3
Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti?
2 Samueli 11:4
Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake.
2 Samueli 11:5
Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti Ndili ndi pakati.
2 Samueli 11:6
Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide.
2 Samueli 11:7
Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yowabu ali bwanji? Ndi anthu ali bwanji? Ndi nkhondo ili bwanji?
Komaso
Tawelenga
Mateyu 12:43
Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.
Mateyu 12:44
Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.
Mateyu 12:45
Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.

Kumasulira
Mutu wa ulariki ndwo ULESI NDI TCHIMO
tikuona mfumu Davide anachita ulesi kupita ku nkhondo ndipo ulesi unabala tchimo losiona nkazi wa Uliya ulesi omwewo unamupasa chilakolako chogona naye ndipo atapereka mimba tikumuona akumuitanitsa Uliya kuti adzagone ndi nkazi wake kuti asadziwike kuti wapanga tchomo logona ndi nkazi wa mwini. Tikaipitiliza nkhaniyo ikulongosora kuti Uliya sanapite kunyumba kwake anagona ndi anyamata pa gate ya mfumu pachifukwa ichi mfumu Davide tikuiona ikumuledzeletsa Uliya ncholinga choti akagonebe kunyumba koma sizinatero pamapeto pake Davide wampanga chiwembu Uliya pouza wankulu wa nkhondo kuti amuike kutsogolo cholinga choti afe. Phunziro
Ukamulora Mulungu kuti akhale tate ndi mupulumitsi wa moyo wako ukhale omvera chomwe Mzimu oyera ukulamulira, chifukwa ukapanda kumvera Umakuchokera ukakuchokera chiwanda chimabwera ndi zinzake kulowa mwa iwe ndipo umakhala oyipitsitsa kuposa pachiyambi. Tikumuona Davide chifukwa cha ulesi wapanga tchimo losilira nkazi wa mwini , chifukwa cholipatsa mpata tchimo lakatenga machimo ochuluka kudzalowa mwa iye. Ndiko kusilira nkazi wamwini, kugona naye, kuledzeletsa Uliya, ndi kupha. Ambuye akudalitseni
Mkhale ndi tsiku lopambana
Amen.

06/08/2025

Morning Devotion
Kupembezera mpimgo wathu, dziko lathu, miyoyo yathu tapempheleraso ma banja athu, odwala, osauka ndi amasiye komanso tapempheleraso ana a sunday school athu.

Ulariki.
Tawelenga mawu kuchokera pa
Eksodo 13:17
Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.
Kumasulira
Akuti mulungu adaumitsa dala mtima wa Farao kuti ana a Israel asawalore kumka ku dziko la malonjezano, koma pamapeto pake adawamasula kuti atha kumapita. Izi Mulungu adazichitila dala kuti ukulu wake uonekere. Zilipo nyengo zanu zidalimba kale kale ndipo mmapemphera koma sizikuenda, msatope nkupemphera chifukwa mulungu amaumitsa dala nyengo zanu kuti ukulu wake uonekere ndipo tsiku lina adzayendera nyengo zanu ndipo chipambano chizadza.
Amen

31/12/2024

Happy new year

Kodi mwakodzeka !!!
27/12/2024

Kodi mwakodzeka !!!

10/12/2024

We thank God for Another Day in the Land of the Living, Welcome to another Glorious day. I pray that the Almighty God will count you worthy as a recipient of His Favour as you step out today. No plan of the evil ones from the pit of hell shall come to pass in your life. Every trap set for you and your family by the agents of death shall miss their target. Those who are waiting to announce your failure shall receive the Greatest shock of their lives, as the Lord God Almighty, announce your breakthrough, Do have a blessed day in Jesus Christ Mighty Name Amen 🙏

17/11/2024

Ulariki wa lero wachokera pa Genisis 3v1-10 ndi masalimo 150 v 1-6 komanso Yohane 10v 10 ndi Agalantiya 4 v 19-20

Genesis 3:2
Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m'mundamu tidye.
Genesis 3:3
Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.
Genesis 3:4
Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;
Genesis 3:5
chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.
Genesis 3:6
Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso.
Genesis 3:7
Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.
Genesis 3:8
Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda.
Genesis 3:9
Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?
Genesis 3:10
Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.

Masalimo 150:1
Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake.
Masalimo 150:2
Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji.
Masalimo 150:3
Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze.
Masalimo 150:4
Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro.
Masalimo 150:5
Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa.
Masalimo 150:6
Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.

Yohane 10:10
Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.

Agalatiya 2:19
Pakuti ine mwa lamulo ndafa kulamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.
Agalatiya 2:20
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

06/11/2024

Machitidwe 3 Vs 6

6 Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.

Address

Chikwawa Load After Blantyre City And At Manase Police Turn To Right
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Nancholi CCAP Church posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share