24/05/2024
Anali katswiri wapamwamba kwambiri. Mbili yake inamveka patali. Ana achichepele ngakhalenso achikulire amadziwa bwino za luso lake loomba Batcha mwaukadaulo. Dzina lake linali Dande.
Dande sanali oomba Batcha wawamba ayi chifukwa nyimbo ikafika pamtsetse amatha kusakaniza maombedwe a Batcha ndi chibwano, chitendene, chigonkono mwa Zina
Amathanso kuiomba Batcha ataisenza pa mutu ngakhale ataibeleka kunsana kwinaku ndodo zoimbira akumaziponya mmwamba ndikumaziwakha koma nyimbo osasokonekela.
Luso la nkuluyu linakopa anthu ochuluka ndipo anali kuitanidwa mu zochitika zosiyanasiyana monga mu zikwati, zinamwali, zinkhoswe, kulonga ufumu, misonkhano ya zipani ndi kulikonse kumene kungafunike mavume a Batcha.
Ndukumbuka mchaka china achibale ena anali ndi ukwati ku tawuni, ndipo ife tinayenela kukapezeka nawo kumeneko. Tinapita kukamusaka Dande kuti timvane kuti akhonza kufuna zingati kuti akativinise ku tawuni.
Tinayenela kunyamuka lachisano kuti tikachezele kujaza usiku onse chifukwa mwambo wa ukwati unali wa loweruka.
Galimoto linafika kudzatenga anthu a mmudzi kuti tikaiontse kutauni. Dande anachedwelapo kufika chifukwa amachokela mudzi wa patali. Nkhawa inathawa pamene tonse tidamuona wachikulire wa Batcha akutulukira ali wefuwefu.
Ulendo unayambika kupita ku taoni, nyimbo zoyeselera zikulikitika mu lole imene tinakwela kuti tikaone poyambira.
Mmene nthawi imati 6koloko madzulo nkuti tikufika mu tawuni ya BCA munzinda wa Blantyre. Tinalandilidwa bwino ndi chakudya muja mudziwira mwambo wa ukwati.
Dande anayenela kuchita zokonzekela pa ntchito yake monga kuwamba Batcha ndi Zina kuti nthawi iliyonse mchezo uyambe. Nawonso ma Dj aku tawoni, anali kugwiragwira zida zao za magetsi, kusonkhanitsa ma kaseti ndi Zina.
Nthawi imeneyo nyimbo zobheba zinali za achina Malume Bokosi, black missionaries kuimba3, Mwana mulamba, Dan K uja wa ku Zambia ndizina munthawiyo,Ndipo momwe kunakonzedwela mwambo unayambadi.
Kunali kusokonezana chifukwa Dj amati akafaka nyimbo yomwe yavuta nthawi imeneyo, ndipamene Dande naye akuonetsa zisuzo kubwalo lake lomwe anapatsidwa kuti onse okonda Batcha akakhaleko.
Anthu a kutawuni amati akabwera kuzasunzumira ku bwalo la mganda, samafuna kuchoka kamba ka dansi ya fumbi yomwe imatcholedwa kumeneko.
Zinafika pokuti mpaka choimba adazimitsa chifukwa chidwi Cha anthu tsopano chinali ku mganda umene Batcha yake imaimbidwa mopatsa chikoka.
Katswiriyu sanali kupambadza Ng'oma chabe, analinso ndi luso loimba nyimbo. Amati akaiyambitsa nyimbo anthu ovomeleza samasowa poigwira.
Zikafika pankomati Nchikulireyu amatha kutulusa voice ina yopatsa chidwi pena kumveka ngati akulira atayang'ana kumwamba kwinaku akupukusa mutu wake.
Ndikuti sanali munthu wamasewera ikafika nthawi yosangalatsa khamu.
M'mawa kutacha pa tsiku la mwambo wa ukwati anthu onse akutaoni anasonkhana kufuna kumuona Dande chifukwa usiku samamuona bwino amangomva ntchito za manja ake.
Komatu apa nkuti Wachikulireyo agona Kaye kuzitolera kukonzekela nkhondo yoomba Batcha pa mwambo weniweni masana ake. Komabe poti anali osazikweza, atadzutsidwa kuti kwabwera khamu la anthu amene amavina usiku uja, anadzuka kuti akumane nao.
Masana nthawi yoyamba mwambo inakwana, ndipo onse anakanisitsa kuvina nyimbo za pamagetsi. Katswiri Dande, anaigwira ntchito yotamandika mpaka mwambo onse wa ukwati unayenda mwa pamwamba zedi.
Anasiya mbiri yabwino ku tawuni
Legend Dande munthawi yathu.