13/04/2025
YOHANE 6 V 55
Pakuti Thupi langa ndi chakudya ndithu ndi Mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.
PHUNZIRO:
Yesu mmene ankayankhula izi ankadziwa kuti amene adye Thupi ndi kumwa Mwazi wake ndiye kuti akuyenera kukhala Munthu woyeretsedwa chifukwa mkate ukuimirira Thupi la Yesu ndipo Vinyo ukuimirira Mwazi wake wa Yesu Khristu.
Ndikudziwa kuti pali anthu ambiri amene adya Mkate komanso kumwa Vinyo koma ali opanga zinthu zosakhala bwino zimene zili zotsutsana ndi Malamulo a Yehova Mulungu wathu wa Moyo.
Dziwani kuti tisanadye Mkate komanso kumwa Vinyo timayenera kudziyeretsa polapa machimo athu ndipo tikadya ndi kumwa Thupi ndi Mwazi wake tikuyenera kukhala masiku Asanu ndi awiri tisanachite tchimo liri lonse. Apa Mau a Yehova amati; Musadye Mkate wotupitsa ayi. Ndipo dziwani kuti ngati tidya chotupitsa pang'ono ndiye kuti zonse zimene tichita ndiye kuti zisanduka zotupitsanso.
Chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse. Apa tikuyenera kuchenjera pochita zinthu zathu osati tikondwe kuti tadya Thupi ndi kumwa Mwazi wa Yesu Khristu pamene mkati mwathu muli dumbo komanso milandu yambiri.
Ngati tachita zinthu zosakhala bwino tiyeni tigwade ndipo tilape chifukwa Mau a Yehova amati; Ngakhale tchimo litafiira ngati Kapezi koma tikalapa lidzayeretsedwa ngati Matalala.
Ambuye akudalitseni Abale ndi Alongo nonse.
Mukhale ndi Utsiku wabwino!