Apostle Joseph Adams Phiri

Apostle Joseph Adams Phiri Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Apostle Joseph Adams Phiri, 0882806598/0991211410, Blantyre.

14/05/2024

Romans 8:35
Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?

Kuzipeleka kwathu kwa Mulungu palibe chomwe chingatilekanise
Palibe chomwe chingatilekanise ndi chikondi cha Mulungu
Akhristu ena amasiya kupephera chifukwa cha zopyinja zomwe akukumana nazo.
Ena amafika ponyoza Mulungu kuti Sakuva kulira kwawo, sakuona nyengo zawo zomwe akukumana nazo.
Paulo akulimbikisa mpingo wa ku Aroma kuti palibe nyengo yomwe ingatipangise kusiya kupephera, kulambira Mulungu kutumikira Mulungu.
Munyengo zonse Mulungu amakhala nafe. Mulungu amava kulira kwathu Amaona nyengo zathu ndipo muthawi yake yoikika azayankha. STAY BLESSED

By Apostle J Adams Phiri
088 280 6598

27/04/2024

Mateyu 6:25
Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala?

NKhawa siyabwino nkhawa imabwelesa matenda, nkhawa imapangisa munthu kuganiza zozipha. Anthu timakhala ndi nkhawa pazithu zosiyana siyana moyo uno.
Ndizotheka kugonjesa nkhawa
Choyamba khristu ali yense aziwe kuti moyo omwe tili nawo ndiwoposa zomwe timafuna, chifukwa moyo sitingagule ndi ndalama. Moyo ndiwoposa chili chonse, moyo ndi mpamba, ngati muli ndi moyo muli ndikuthekela kopanga zithu;
Muli ndikuthekela kopita ku school
Muli ndi kuthekela kopita ku tchito
Muli ndikuthekela kopita ku business
Muli ndikuthekela kopanga ulimi
Moyo ndi capital
Munthu wodwala sangapite ku tchito
Munthu wakufa sangapange kathu
STAY BLESSED

BY: Apostle Joseph Adams
088 280 6598

25/04/2024

Miyambo 16:32
Wosakwiya msanga aposa wamphamvu;
Wolamulira mtima wace naposa wolanda mudzi.

Kwiyo siwabwino, kwiyo umapha kwiyo umaonongesa zithu, kwiyo umapasula ma banja, ngakhale dziko, kwiyo umatha kubwelesa matenda monga BP, kwiyo umatha kukupangitsa kuyakhula molakwika.
Monga ife akhristu tiyeni tiphuzire kuleza mtima. Zokwiyisa zambiri ku dziko lapasi koma tiyeni timulore mzimu woyela azitithandiza kukhala anthu oleza mtima. Akhristu sakuyenela kugona ndi kwiyo sakuyenela kusunga kwiyo mutima mwawo kwa thawi yayitali chifukwa zosatila zakwiyo zoipa. Mulungu apitilize kutitsogolera, mzimu woyela monga khoswe yathu atiphuzitse kukhala anthu oleza mtima. STAY BLESSED
By Apostle J. Adams Phiri
088 280 6598

01/03/2024

Address

0882806598/0991211410
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Apostle Joseph Adams Phiri posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share