20/09/2022
SATANA MDIEREKEZI KWAKE NDI KUPHA, KUBA NDI KUONONGA. MWA IYE MULIBE CHOONADI, KUKHALA BWENZI LASATANA KUONONGA NTHAWI CHABE CHIFUKWA PALIBE CHABWINO CHOMWE MUNGACHIPEDZE MWA SATANA MDIEREKEZI.
LOLANI YESU KHRISTU ALAMULIRE MOYO WANU NDI KUTI IYE AKKHALE BWENZI LANU, NDIPO SIMUDZAKHUMUDWA ,IYE AZAKUPASANI MTENDERE NDI MOYO WOSATHA. MUKAKHULUPILIRA YESU KHRISTU KUKHALA MBUYE NDI MPULUMUTSI WA MOYO WANU, CHILICHONSE CHOMWE MUFUNA CHIDZAPASITDWA KWA INU.
(📖 11 🆚 28-30)
#28➡️Idzani kuno kwa ine nonse akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu, senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa ine: chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. #30➡️Pakuti gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
-LA-KHRISTU
Okondedwa mwa Ambuye wathu Yesu khristu, Moyo ukuyenda bwanji kumene inu muli? Yesu khristu akuitana, bwerani kwa ine, bwerani kwa ine, musiyileni katundu wake satana. Ngati sakufuna kukutulani Ine Yesu khristu ndizakutulani.
Chifukwa alipo ena asing'anga anawapatsa chizimba koma anawauza kuti palibe kutembenuza, Tikunena pano atopa nacho chizimba koma pogwira alibe. Bwerani kwa Yesu khristu.
Alipo ena atopa ndikutumikira satanic koma akuopa athedwa nzeru chifukwa cha mantha. Moyo wawo uli pa chiopsezo chifukwa kusiya kwa satanic mkufa, Ai ai musaope, Bwerani kwa Yesu khristu ndamene ali ndi Mphamvu kuposa satana mdierekezi.
Kodi ndinu otchuka ndikutaya zimimba, mbava, wakupha, wabodza, wachiwerere, wolezera, wosuta fodya, Wochita machimo anyansisitsa
Bwerani kwa Yesu khristu, akufuna inu kuti akutuleni katundu wolemetsa wa satana mdierekezi.
Kodi inuyo mwatopa ndi chani? katundu wa machimo omwe inuyo mwanyamula mukuwadziwa. Yesu khristu akuti ngati mukufuna mtendere ndi moyo wosatha pa miyoyo yanu. Tipite kwa Iye sakusakha munthu, kapena kuchuluka kwa machimo akuti aliyense abwele kwa Iye.
Kuli bwino kusenza gori la Yesu khristu, kusiyana ndikusenza gori la satana. Chifukwa gori la khristu lili lofewa, Kwa bwino kuti anthu akunyozeni, akutukwaneni , anthu alakhule zoipa za inu, chifukwa cha Dzina la Yesu khristu.
Mukamatchuka ndi kukhwima, uhule, umbava, miseche, mabodza, kuba, kupha ndi ntchito zoipa zambiri zosiyana siyana. Wina akakunenani kuti wochimwa iwe mumapsa mtima chifukwa chani? Chifukwa kuti choti mumakhala kuti ntchito zoipa zimakusowesani mtendere chifukwa kuti inuyo mwasenza gori la satana.
Musaumitse mtima. Ali ndi Khutu amve, Amen