Pastor Fredrick Mponda

Pastor Fredrick Mponda Glory to God

11/07/2026

Zinamutengera Yosefe kukhala ku ndende k*t akhale wolamulira, chipambano sichibwera mophweka, kuseli kwa mavuto ako kuli chipamban

Yobu 42 :10, Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, Pamene anapempherera mabwenzi ace, Yehova anacurukitsa zace zonse z...
10/07/2026

Yobu 42 :10, Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, Pamene anapempherera mabwenzi ace, Yehova anacurukitsa zace zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza

Halleyu!!!! Wokondedwa tamvetserani Yobu anali mu nyengo yowawa, yomwe amafunikira mapemphero a anthu ena koma tamuoneni Yobu ameneyu ndi amene akuwapempherera anthu ena

Wokondedwa nyengo zomwe mukudutsa zitsakupangitseni kuyiwala kupempherera ena kapena k*thandiza ena, gwiritsani chilichonse chomwe muli nacho k*thandizira ena omwe akuvutika osawerengera za nyengo zanu

Yobu anapempherera abwezi ake ndipo Mulungu anamuchotsera ukapolo wake ndipo Yehova anachurukitsa zace zonse mpaka kuziwirikiza.

Pemphero lanu litsakhale la inu nokha apempherereni anthu ena omwe akudutsa mu zowawa ngakhale inu muli mu zowawazo, muzaona ukulu wa Mulungu

Wina alipo ndithu k*ti nyengo zake zisinthe zingofunikira k*ti upempherere anthu odwala zipatala, wina wa iwe ungofunikira uchite ntchito ya chifundo kwa wina wake k*ti nyengo zako zisinthe, Chita chomwe ukumva mkat mwako chimene Mulungu a kukuyankhula lero,

Yobu sanachedwe ndi chomwe amayenera k*ti achite ndipo a tachita nyengo zake zinasitha, ena mwa inu Mulungu wakhala a kukuyankhula zoyenera kuchita mwina ku maloto kapena mu Chidziwitso,

Glory be to God all the time

Mulungu yemwe anachotsa ukapolo wa Yobu, akuchotsere iweso nyengo za ukapolo zomwe zili pa moyo wako, mwezi uno wa July ...
01/07/2026

Mulungu yemwe anachotsa ukapolo wa Yobu, akuchotsere iweso nyengo za ukapolo zomwe zili pa moyo wako, mwezi uno wa July

Ma plan ako omwe a khala asak*theka aja atheke mu dzina la Yesu khristu

Khomo lija wakhala uku gogoda lija Yehova ak*tsegulire mwezi uno

Khulupilirani k*ti ndi mau a Mulungu nyengo zanu zisintha,

AMEN 🙏🙏

Kuli Mulungu kunja kuno woyankha mapemphero, ochita zosathekaNdik*theka chikhulupiliro chako chayamba kufooka chifukwa c...
22/06/2026

Kuli Mulungu kunja kuno woyankha mapemphero, ochita zosatheka

Ndik*theka chikhulupiliro chako chayamba kufooka chifukwa cha nyengo zomwe ukudutsamo, wa pemphera koma sizikusitha, mwina ndipamene mavuto akuchulukirabe.

Koma Osafooka, dzukabe ndi pemphero, wachokera Kuja ndi k*tali osabwerela pa njira, Yankho lako layandikira

Mdima ukachuluka Kuja kumakhala kwayandikira k*ti kuyere, tsiku lina ndithudi iweyo uchitira umboni

Nyengo zomwe ukudutsazo ndi umboni wako wa mawa, ngakhale zikuwawa koma Osataya mtima

Wokondedwa tamuoneni Yobu anataye chilichonse chomwe anali nacho koma anayimabe pa Mulungu ndipo Mulungu anabwezeretsa zonse zomwe anataye kuposa zomwe anali nazo kale

Hana ananyozedwa chifukwa chosowa mphatso ya mwana koma Mulungu anayankha mapemphero ake

Wokondedwa mpamba ndi moyo, osazikiyira malire pamene tili ndi moyo zonse ndi zotheka Ndithu,

Monga Hana anachitira umboni za chosowa chake ali ndi moyo iweso uchitira umboni k*ti Mulungu wapereka zopempha, nkhan ndi nthaw basi

Sachedwa kapena ku fulumira Yehova,

Glory be to God all the time

Osamalimbana ndi anthu omwe akukunyozani chifukwa cha nyengo zomwe inu mukudutsamo, musiyireni Yehova ndi amene awayankh...
19/06/2026

Osamalimbana ndi anthu omwe akukunyozani chifukwa cha nyengo zomwe inu mukudutsamo, musiyireni Yehova ndi amene awayankha

Hana akunyozedwa ndi Peninah sanalimbane naye k*ti lero lokha Peninah a ndidziwa k*ti ine ndi ndan, sanamvule chikhristu chake

Koma iye anapempherabe kwa Yehova kusala kudya, ndikupereka zowinda zake kwa Yehova

Wokondedwa Ndik*theka mukunyozedwa chifukwa ca umbeta wanu, umphawi wina, kapena matenda, inu musafooke kapena kulimbana ndi omwe akukunyozaniwo, Yankho lanu lili pafupi Yehova awatseka pa kamwa ndi umboni omwe akupereka kwa inu

Musataye chikhulupiliro canu, chikhristu canu polimbana nawo, Khalan ngati Hana ameneyu

Mulungu akuchotseni nyengo iliyonse yomwe ikubweretsa chitonzo pa moyo mu dzina la Yesu khristu Amen

Glory be to God all the time

Ulendo wina ulionse umayamba ndi step imodziWokondedwa osaopa kuyamba business ngakhale muli ndi ndalama yochepa, kapena...
16/06/2026

Ulendo wina ulionse umayamba ndi step imodzi

Wokondedwa osaopa kuyamba business ngakhale muli ndi ndalama yochepa, kapena Osakhala ndi mantha kapena manyazi ndi mmene mumapezera ndalama kapena business yomwe mumachita

Ndalama zili mumanyazi, ndibwino kumathamanga ka business kenakake kusiyana ndi kumangopempha, kupempha kumachotsa ulemu

Ama business akuluakulu tikuwaonawa, ma utumiki akuluakulu wa nawo anayamba ndi pang'ono

Chomwe Mulungu akufuna ndi choti inu muyamba kuchita chinachake ndikumapemphera k*ti dzanja la Yehova likhale pa chonchita chanu

Anthu ambiri timakhala ndi ma plan abwino koma kuchita kapena kukwanilitsa, ma plan athu kumakhala k*tivuta

Alipo anthu ena anayamba ndi geni ya tomato pano ali pena ndithu zawo zikuwayendera, pamene ena amakhala akuchita manyazi, aaaa anthu azindione ndi kupanga izi mpaka amalorela kumavutika koma mwayi woti nyengo zawo zikhoza kusitha ulipo

2 mafumu 4:2,Ndipo Elisa anati kwa iye, ndikucitire ciani? Undiuze m'nyumba mwako muli ciani? Nati mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta, 3 Pamenepo anati......... Mulungu anagwiritsa ntchito kanthu kakang'ono koma kanali nyumba mwa mkazi wamasiye kusovera mavuto ake

Mulungu ali yemweyo kugwiritsa kakang'ono kalikonse komwe inu mwayamba kumasamalira banja lanu, kukwanilitsa masomphenya anu, nkhan ndikuyamba

Inu simukufunikira ndalama zambiri k*ti muyambe business koma mungofunikira vumbulutso, Mulungu akupaseni vumbulutso la moyo wanu ndi momwe mutuluka mu nyengo imeneyo mu dzina la Yesu khristu Amen

Yehova alibe size YakeWokondedwa Kuja kuno kunali anthu omwe ankazimva mphamvu, ena chifukwa ca ma udindo, ena chifukwa ...
09/06/2026

Yehova alibe size Yake

Wokondedwa Kuja kuno kunali anthu omwe ankazimva mphamvu, ena chifukwa ca ma udindo, ena chifukwa ca kukwima, nyanga, matsenga ndikumayetsayetsa kufuna funa kufanana ndi Yehova koma anawakhalitsa chete

Kunali achina pharaoh anatha muvetsa chinsoni kufuna kulimbana ndi ana a Mulungu, kunali achina Goliat anafa ngati mwana, kunali achina Nebukadinezara anatha momvetsa chisoni

Tamvetsera m'bale, Iwe mulongo kwina kuli konse komwe uli, usakhale ndi mantha ndi anthu a nyanga, a matsenga, amfit, omwe akulimbana ndi moyo wako, Iwe tamukhulupilire Yehova, Yehova ndiye mwini nkhondo akumenyera nkhondo zako iwe uli chete ungomva zotha itha k*ti adani ako agonja

Amene akulimbana ndi moyo wako, tsogolo lako, madalitso ako, Banja lako akumane ndi dzanja la Yehova

Dzenje lililonse lomwe akukumbira k*ti iwe ugweremo, amene wakumbayo agwere yekha

Wokondedwa kwa Yehova kuli chitetezo, Ak*tetezeni poyenda panu, pokhala panu mu dzina la Yesu khristu Amen

Musakhale ndi mantha ndi za ufitizo
Ahebri 12 :29 Yehova ndiye moto wonyeketsa, 🔥🔥🔥unyeketsa plan iliyonse ya satana pa moyo wanu

Kumaliopa mawa, Mulungu anatibisira za mawa la munthuOweruza 11:7 Ndipo Yefita anati kwa akulu a Gilead, simunandida Kod...
08/06/2026

Kumaliopa mawa, Mulungu anatibisira za mawa la munthu

Oweruza 11:7 Ndipo Yefita anati kwa akulu a Gilead, simunandida Kodi, ndi kundicotsa m'nyumba ya atate wanga? Ndipo mundidzeranji tsopano pokhala muli m'kusauka?

Wokondedwa tizikhala bwino ndi anthu za mawa la munthu amadziwa ndi Yehova alipo ena lero alibe mkathu koma ndi mabwana mawa tiyeni tisamathe mau pa anthu omwe sizikuwayendara

Ndik*theka amagwira ntchito pa nyumba panu alemekezeni, za mawa lawo simukulidziwa

Anamunyoza Yefita koma ndi omwewo omwe anayamba kumufunafuna, ndikupempha k*ti awathandize, wokondedwa ofuna nzake sakudziwika pa chifukwa ichi tiyeni tikhala bwino ndi aliyense

Tiphunzire kulemekeza aliyense, ena akuoneka lero ngati wopanda nzeru chifukwa cha nyengo zomwe akudutsa koma mawa ndi (hero)

Kwa iwe amene ukudutsa mu nyengo zotsalidwa, ku mtundu wakwanu limbikilabe kupemphera kugwira ntchito zako, osamaziyang'nire pansi, tsiku lina azakufuna ndipo anthu azafuna thandinzo lako

Kuja kuno kuli Mulungu wositha nyengo, Osamadaula k*ti ine ndimasalidwa chifukwa canu, Osalowelera, Iwe Bola ubale wako ndi Mulungu ukhale pa bwino

Mulungu akuchotseleni mbiri yanu yokanidwa, yosalidwe ndi ulemelero wake, nyengo yomwe imapangitsa k*ti anthu azikusalani Mulungu ayiyendere mu dzina la Yesu khristu

Glory be to God all the time

06/06/2026

Iweyo ndi umboni

Pena munthu umafika pokhetsa misozi wosati ya chisoni koma ya malambiro, ukalingalira za momwe Mulungu wakhala akuk*tetezera kwa adani, akukudalitsira, akuk*tchiritsira nthenda zako

Wokondedwa tadutsa mu zambiri akamafotokoza makolo zomwe zinatichitikira, tili ana, nakha zomwe takumana nazo titakula

Inu muli ndi umboni, woti mukakhala phee mumafika pokhudzika ndi k*ti koma Yehova anakapanda kukhala ku mbali yanga, bwezi kulibeko

Anakapanda Yehova kukhala nanu pa nthena ija munadwala ija bwezi inu kulibe, kuchipatala Kuja k*tulukako ndi moyo, pa oxygen paja kuchoka ndi moyo, ku operation Kuja k*tulukako ndi moyo, ndi umboni

Wokondedwa tili ndi zifukwa zambiri zomuyamikira Yehova, nyengo yomwe mukudutsayo isakupangitseni kumunyoza Yehova, wakuchotsani patali amenewo sangakhale matero anu

Wokondedwa mukulambira, mumayamiko muli mphamvu yoopsa, ndimafuna musayang'ana za vuto lanu koma muyang'ane za ukulu wa Mulungu,

Mulungu akudalitseni

Muyamiken Yehova mu zonse (voice of praise)

Osasiya kupemphera mukalandira chopempha canuAnthu ambiri timati tikalandira zimene timapempherela timakhala pansi( lela...
06/06/2026

Osasiya kupemphera mukalandira chopempha canu

Anthu ambiri timati tikalandira zimene timapempherela timakhala pansi( lelax), kusiya kupemphera ku dikira k*ti nyengo zidzadzukitso k*ti tizayambetso kupemphera uku ndi kuzichedwatsa Wokondedwa

Kupemphera ndi nkhondo, tikalandira satana samakondwa ndiye ukasiya kupemphera umamupatsa mpata woti atsokoneze chomwe iwe unalandira kale

1 Atesalonika 5 :17 Pempherani kosaleka. Wokondedwa pamene Mulungu akupereka zosowa zathu , zopempha zathu timbikitsani ena ndi ma umboni athu

Anthu ambiri tili malo amodzi modzi, tikupempherela chimodzmodzi chifukwa Mulungu angakotipatsa, timayiwala kupemphera ngakhale khomo la ku church, timati tili busy, tikabetsa ndipamene timadzuka ndikuyambatso kupemphera

Uthengawu ukubwera kwa inu ndi ine lero chifukwa chija takhala tikupempherela chija, Mulungu a k*tipatsa koma tisabetse pokhala chete, chomwe Mulungu akupereka, mayako a Mulungu kwa Ife akhale mangolomera mu chikhulupiliro chathu

Osafooka,

Mulungu adalitse mau ake, adalitsitso iwe amene wawelenga mu dzina la Yesu khristu Amen

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Pastor Fredrick Mponda posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share