14/08/2026
*TIYANKHULENI AMBUYE*
*14 AUGUST, 2026*
_LACHISANU LAMULUNGU WA 19 PACHAKA (II)_
KULEMEKEZA MAXIMILIAN KOLBE WOYERA, MMALITIRI
*MAU OYAMBA; MAU A MBUKU LA MNENERI EZEKIELI 16:1-15,60,63*
Chauta adandipatsira uthenga uwu, wakuti: ”Iwe, mwana wa munthu, umuonetse Yerusalemu makhalidwe ake onyansa. Umuuze kuti: Ambuye Chauta akukuuza kuti: ‘Kanani ndi dziko la makolo ako, ndipo udabadwira kumeneko. Atate ako adali Mwamori, amayi ako adali Muhiti. Ndipo utabadwa adakuchita izi: sadakusambitse m’madzi kuti akuyeretse. Sadakuthire mchere monga kudayenera, ndipo sadakukulunge mu nsalu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adakusamala, kapena kukumvera chisoni chokwanira, kuti akuchitire zimenezi. Koma adakutaya panja poyera, chifukwa adanyansidwa nawe pa tsiku limene udabadwa. ‘Ndiye Ine nditabwera, ndidakuona ukuvimvinizika. Ndidalankhula nawe ndi kukuuza kuti: ‘Ukhale ndi moyo, ndipo ukule ngati mbewu ya m’munda.’ Udakuladi, ndipo udatalika nkutha msinkhu. Maŵere adayamba kumera, tsitsi lako lidayamba kutalika. Komabe udali wa maliseche ndi wausiŵa.Nditabweranso, ndidaona kuti nthaŵi yako yomanga banja idakwana. Tsono ndidakufunditsa mwinjiro wanga, ndi kubisa maliseche ako. Ndidachita nawe chipangano cha ukwati, ndipo udasanduka wanga. Ndikutero, Ine Ambuye Chauta. Tsono ndidakusambitsa m’madzi ndi kukutsuka magazi ako, ndipo ndidakudzoza mafuta. Ndidakuveka zovala zopetapeta, ndi nsapato zachikopa. Ndidakupatsa nsalu za bafuta, ndi kukuveka zovala za silika. Ndidakukongoletsa ndi za makaka, nkukuveka zigwinjiri m’manja, ndi mkanda m’khosi mwako. Ndidakuveka chipini pa mphuno. Ndidakuika nsapule ku makutu ndi chisoti chaufumu chokongola kumutu kwako. Motero udavaladi zokongoletsa za golide ndi za siliva. Zovala zako zidali za bafuta wosalala, za silika ndi za nsalu zopetapeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta a olivi. Udakula mokongola zedi, ndipo udasanduka mfumukazi. Mbiri ya kukongola kwako idawanda pa dziko lonse lapansi, chifukwa choti ulemerero umene ndidakuveka nawo udakukongoletsa kwambiri. Ndikutero, Ine Ambuye Chauta. ”Koma udadzitama nako kukongola kwako ndi kutchuka kwako, ndipo udayamba kuchita zadama. Unkachita chigololo, kumangodzipereka kwa aliyense amene wabwera. Komabe ndidzakumbukira chipangano chimene ndidachita nawe pa ubwana wako. Ndidzachita nawe chipangano china, chipangano chake chosatha. Ndikadzakukhululukira zoipa zako zonse zimene udachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzathanso nkulankhula komwe. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
*Mau a Ambuye*
NYIMBO YA SALIMO: YESAYA 12: 2-3, 4BCD, 5-6
*Inu Chauta, ngakhale mudandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka* (1c).
Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga,
Ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa.
Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa,
Ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.
Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.
*Inu Chauta, ngakhale mudandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka*.
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake.
Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
Mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
*Inu Chauta, ngakhale mudandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka*.
Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu.
Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi.
Fuulani ndi kuimba mokondwa, inu anthu aku Ziyoni,
Pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.
*Inu Chauta, ngakhale mudandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka*.
*Aleluya*: (1 Atesalonika 2: 13) _Pamene mudamva mawu a Mulungu, amene tidakulalikirani, mudaŵalandira osati ngati mawu a anthu chabe, koma monga momwe aliri ndithu, mawu a Mulungu_, *Aleluya*.
*MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYU 19:3-12*
Afarisi ena adadza kwa Iye. Tsono kufuna pomupezera chifukwa, adamufunsa kuti: “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake pa chifukwa chiri chonse?” Yesu adaŵayankha kuti: “Kodi simudaŵerenge kuti Mulungu, amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi? Ndipo kuti Iye yemweyo adati: ‘Nchifukwa chake mwamuna adzasiya atate ake ndi amayi ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’ Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.” Afarisi aja adamufunsa kuti: “Nanga bwanji Mose adalamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo kenaka ndi kumpirikitsa?” Yesu adaŵayankha kuti: “Mose adakulolani kusudzula akazi anu, chifukwa ndinu anthu okanika. Komatu pa chiyambi sizidali choncho ayi. Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.”
Ophunzira ake adamuuza kuti: “Ndiyetu ngati zili choncho pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndi bwino tsono kusakwatira.” Yesu adaŵauza kuti: “Si anthu onse angamvetse zimenezi ayi, koma okhawo amene Mulungu aŵathandiza. Paja pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa adabadwa motero. Pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa anthu adaŵafula. Pali enanso amene adachita kusankha okha kusakwatira, kuti azitumikira bwino Mulungu. Yemwe angathe kumvetsa, amvetse.”
*Mthenga wa Ambuye*