29/03/2019
KUSALA KUDYA
Mawu oyamba
Phunziro la kusala kudya ndi lachilendo kwa akhristu ambiri. Chifukwa mawu akuti kusala amalumikizana kwambiri ndi zipembedzo zina osati chachikhristu. Muphunzilori tifuna kufotokozerana za kusala kudya koyenera ndi kosayenera pa chipembedzo chachikhristi.
KODI KUSALA KUDYA NDI KUTANI
Kusala kudya ndi kukhala osadya ndi osamwa kathu kwa masiku angapo. Ayuda ankasala kudya kawiri kawiri pa zifukwa zosiyanasiyana monga:
1. Kukonzekera chipembedzo
2. Chifukwa cha mavito, maliro , nkhondo
3. Kuonetsa kugonja pamaso pa Mulungu ndi zina zambiri. (2 Samuel 12:16, Genesis 50:10, Exsodo 34:28)