09/06/2026
ππ¨π¬ππ‘πππ ππ¨π¬ππ§ππ‘π ππͺπ π π¨ππ¨π‘ππ¨
Pamene kwasala masiku asanu, bungwe la amayi mu mpingo wa Seventh-day Adventist , la Malawi Union Conference Women's Ministries likukuitanira amayi onse ku tsiku lolimbikitsa utumiki wa amayi odziwika kuti Women Ministries Emphasis Day mchaka chino cha 2026. Mwambowu uchitika pa 13 June 2026 m'mipingo yonse mdziko muno.
Chaka chino mutu wathu ndi βHenani, Ine Ndili Panoβ β mawu a kudzipereka ngati Yesaya, okonzeka kunena kuti βNdine, Nditumeniβ. Tiyeni tigwirizane monga amayi ndi atsikana kuti timvere ndikuyankha mawu a Mulungu mβmbadwo uno.
Tsikuli ndi la kupembedza, kulimbikitsana, ndi kuphunzira udindo wathu monga mboni za Khristu mβbanja, mβmipingo, ndi mβmadera. Kuchokera pa maulaliki, misonkhano, mpaka kuyimba pamodzi, tidzalimbikitsidwa kukhala βOvomera Kupitaβ - amayi olimba mtima, odzala ndi Mzimu Woyera, okonzeka kutumikira.
Tibwere tonse mu umodzi ndi kukongola kwa ana a Mulungu.
Ndipo mpingo onse ukulimbikitsidwa kutenga nawo mbali.
Olemba : McAllan Mapinda
EMC Media (8/6/2026)